M’Cheyne Bible Reading Plan
Kubadwa kwa Samsoni
13 Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, kotero Yehova anawapereka mʼmanja mwa Afilisti kwa zaka makumi anayi.
2 Ku Zora kunali munthu wina dzina lake Manowa, wochokera ku fuko la Dani. Mkazi wake analibe ana popeza anali wosabereka. 3 Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. 4 Tsono mudzisamale bwino, osamwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso musamadye chakudya chilichonse chodetsedwa, 5 chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.”
6 Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake. 7 Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”
8 Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.”
9 Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye. 10 Tsono mkaziyo anathamanga kukawuza mwamuna wake kuti, “Wandionekeranso munthu uja amene anabwera kwa ine tsiku lija.”
11 Choncho Manowa ananyamuka namutsatira mkazi wake. Atafika kwa munthuyo anamufunsa kuti, “Kodi ndinu munayankhula ndi mkazi wanga?”
Iye anayankha kuti, “Ndine.”
12 Kenaka Manowa anafunsa kuti, “Tiyerekeze kuti mawu anuwa akwaniritsidwadi, ndiye mwanayu azidzakhala bwanji ndipo azidzachita chiyani?”
13 Ndipo mngelo wa Yehova uja anamuyankha kuti, “Zonse zimene ndinawawuza akazi anuwa asamale ndipo adzazichitedi. 14 Asadzadye chilichonse chochokera ku mphesa. Asadzamwe vinyo kapena choledzeretsa chilichonse, ngakhale kudya chakudya chilichonse chodetsedwa. Zonse zimene ndinawalamula azisunge bwino.”
15 Manowa anamuwuza mngelo wa Yehova uja kuti, “Chonde dikirani pangʼono, timati tikukonzereni mwana wambuzi.”
16 Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu).
17 Tsono Manowa anapempha mngelo wa Yehova kuti, “Chonde tidziwitseni dzina lanu kuti zikadzachitika zimene mwanenazi ife tidzakulemekezeni?”
18 Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.” 19 Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona. 20 Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi. 21 Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova.
22 Iye anawuza mkazi wake kuti, “Ife tifa basi pakuti taona Mulungu!”
23 Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.”
24 Motero mkaziyo anabereka mwana wa mwamuna, namutcha dzina lake Samsoni. Iye anakula ndipo Yehova anamudalitsa. 25 Mzimu wa Yehova unayamba kumulimbikitsa pamene ankakhala ku misasa ya anthu a fuko la Dani, malo amene anali pakati pa Zora ndi Esitaoli.
Paulo ku Tesalonika
17 Atadutsa ku Amfipoli ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge ya Ayuda. 2 Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, 3 kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.” 4 Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.
5 Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu. 6 Koma atalephera kuwapeza, anakokera Yasoniyo ndi abale ena ku bwalo la akulu a mzindawo akufuwula kuti, “Anthu awa, Paulo ndi Sila, amene akhala akusokoneza dziko lonse lapansi, tsopano afikanso kuno. 7 Yasoni ndiye anawalandira mʼnyumba mwake. Onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara pomanena kuti palinso mfumu ina, yotchedwa Yesu.” 8 Atamva zimenezi, gulu la anthu ndi akulu a mzinda anavutika mu mtima. 9 Iwo analipiritsa Yasoni ndi anzakewo ndipo anawamasula.
Ku Bereya
10 Mdima utagwa, abale anatumiza Paulo ndi Sila ku Bereya. Atafika kumeneko anapita ku sunagoge ya Ayuda. 11 Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona. 12 Ayuda ambiri anakhulupirira, monga anachitiranso amayi ndi amuna ambiri odziwika a Chigriki.
13 Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulalikira Mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko, ndi kuwutsa mitima ya anthu nayambitsa chisokonezo. 14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja koma Sila ndi Timoteyo anatsalira ku Bereya. 15 Anthu amene anamuperekeza Paulo nafika naye ku Atene, ndipo anabwerera ku Bereya atawuzidwa kuti Sila ndi Timoteyo amutsatire msanga.
Ku Atene
16 Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano. 17 Tsono anakambirana ndi Ayuda ndi Agriki amene amaopa Mulungu mʼsunagoge, komanso anthu amene amapezeka pa msika tsiku ndi tsiku ndi ena amene amakumana nawo. 18 Gulu la Aepikureya ndi Astoiki, anthu anzeru, anayamba kutsutsana naye. Ena a iwo anafunsa kuti, “Kodi wolongololayu akufuna kunena chiyani?” Enanso anati, “Akuoneka ngati akulalikira milungu yachilendo.” Iwo ananena zimenezi chifukwa Paulo amalalikira Uthenga Wabwino wa Yesu ndi kuuka kwa akufa. 19 Kenaka iwo anamutenga nafika naye ku bwalo la Areopagi kumene anamufunsa kuti, “Kodi tingadziweko chiphunzitso chatsopano chimene ukuchifotokozachi? 20 Iwe ukubweretsa zinthu zina zachilendo mʼmakutu mwathu, ndipo ife tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21 Atene onse ndi alendo amene amakhala kumeneko samachita kanthu kena koma kufotokoza ndi kumvera fundo zatsopano.
22 Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri. 23 Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, kwa mulungu wosadziwika. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.
24 “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. 25 Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. 26 Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. 27 Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’
29 “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. 30 Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. 31 Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”
32 Atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anaseka, koma enanso anati, “Ife tikufuna tidzamvenso zimenezi tsiku lina.” 33 Ndipo Paulo anatuluka mʼBwalolo. 34 Anthu ena ochepa anamutsatira Paulo ndipo anakhulupirira. Pakati pawo panali Dionisiyo mmodzi wa bwalo la Areopagi ndi mayi wina wotchedwa Damalisi ndi enanso.
Yeremiya Amangidwa
26 Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe. 3 Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa. 4 Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, 5 ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, 6 ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”
7 Ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akuyankhula mawu amenewa mʼNyumba ya Yehova. 8 Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa! 9 Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.
10 Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova. 11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”
12 Ndipo Yeremiya anawuza nduna zija ndi anthu onse kuti, “Yehova anandituma kunenera mawu onse amene mwawamva otsutsa Nyumba ino ndi mzinda uno. 13 Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni. 14 Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera. 15 Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.”
16 Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”
17 Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, 18 “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’
19 Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”
20 (Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. 21 Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. 22 Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. 23 Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).
24 Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.
Fanizo la Alimi
12 Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. 2 Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. 3 Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. 4 Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. 5 Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.
6 “Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’
7 “Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ 8 Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.
9 “Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. 10 Kodi simunawerenge lemba lakuti:
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wakhala mwala wa pa ngodya.
11 Ambuye achita zimenezi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”
12 Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.
Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara
13 Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. 14 Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? 15 Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”
Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” 16 Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”
17 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
Ndipo anazizwa naye.
Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa
18 Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. 19 Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 20 Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. 21 Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. 22 Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. 23 Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”
24 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? 25 Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 26 Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ 27 Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”
Lamulo Lalikulu Koposa
28 Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”
29 Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! 30 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ 31 Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”
32 Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. 33 Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”
34 Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.
Khristu ndi Mwana wa Yani?
35 Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ 36 Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti,
“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
‘Khalani pa dzanja langa lamanja
kufikira nditayika adani anu
pansi pa mapazi anu.’
37 Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”
Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.
Yesu Achenjeza Anthu za Aphunzitsi a Malamulo
38 Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. 39 Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. 40 Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”
Chopereka cha Mayi Wamasiye
41 Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. 42 Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.
43 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. 44 Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.