M’Cheyne Bible Reading Plan
4 Anthu onse atatha kuwoloka Yorodani, Yehova anati kwa Yoswa, 2 “Sankha amuna khumi ndi awiri, mmodzi pa fuko lililonse. 3 Tsono uwalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iwiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodani, pamalo pamene ansembe anayimirirapo. Miyalayo muwoloke nayo ndi kudzayitula pamalo pamene mukagone usiku uno.’ ”
4 Choncho Yoswa anayitana amuna khumi ndi awiri amene anawasankha aja kuchokera pakati pa Aisraeli, mmodzi pa fuko lililonse, 5 ndipo anawawuza kuti, “Lowani pakati pa mtsinje wa Yorodani, patsogolo pa Bokosi la Yehova Mulungu wanu. Ndipo aliyense wa inu atenge mwala pa phewa lake, monga mwa chiwerengero cha mafuko a Aisraeli, 6 kuti ikhale chizindikiro kwa inu. Mʼtsogolo muno ana anu akamadzakufunsani kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ 7 Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ”
8 Aisraeli anachitadi monga Yoswa anawalamulira. Iwo ananyamula miyala khumi ndi iwiri kuchokera pakati pa Yorodani, fuko lililonse la Israeli mwala wake, monga Yehova analamulira Yoswa. Miyalayo anapita nayo ku misasa yawo nakayikhazika kumeneko. 9 Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino.
10 Ansembe onyamula Bokosi lija anayimirirabe pakati pa Yorodani mpaka zonse zimene Yehova analamulira Yoswa kuti awuze anthu zinatha. Zimenezi zinali monga momwe Mose anamufotokozera Yoswa. Tsono anthu anawoloka mtsinjewo mofulumira. 11 Anthu atatha kuwoloka, ansembe anatsogolera anthuwo atanyamula Bokosi la Yehova. 12 Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira. 13 Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo.
14 Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose.
15 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, 16 “Lamula ansembe onyamula Bokosi la Chipanganowo kuti atuluke mu Yorodani.”
17 Choncho Yoswa anawalamuladi ansembe aja kuti atuluke mu Yorodani muja.
18 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova aja atangotuluka mu mtsinje muja nʼkuponda powuma, madzi a mu Yorodani anayambanso kuyenda ngati poyamba mpaka kumasefukira.
19 Aisraeli anawoloka Yorodani tsiku lakhumi la mwezi woyamba ndipo anakamanga misasa yawo ku Giligala mbali ya kummawa kwa Yeriko. 20 Ku Giligala, Yoswa anayimikako miyala khumi ndi iwiri imene anayitenga mu Yorodani ija. 21 Ndipo iye anati kwa Aisraeli, “Mʼtsogolo muno pamene adzukulu anu adzafunsa makolo awo kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ 22 Muzidzawawuza kuti, ‘Aisraeli anawoloka Yorodani pansi pali powuma.’ 23 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anawumitsa Yorodani pamaso panu mpaka inu mutawoloka. Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yorodani monga mmene anachitira ndi Nyanja Yofiira mpaka ife tinawoloka powuma. 24 Iye anachita zimenezi kuti anthu onse pa dziko lapansi adziwe kuti dzanja la Yehova ndi lamphamvu, ndi kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.”
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
129 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,”
anene tsono Israeli;
2 “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,
koma sanandipambane.
3 Anthu otipula analima pa msana panga
ndipo anapangapo mizere yayitali:
4 Koma Yehova ndi wolungama;
Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.”
5 Onse amene amadana ndi Ziyoni
abwezedwe pambuyo mwamanyazi.
6 Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba,
umene umafota usanakule;
7 sungadzaze manja a owumweta
kapena manja a omanga mitolo.
8 Odutsa pafupi asanene kuti,
“Dalitso la Yehova lili pa inu;
tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
130 Ndikulirira kwa Inu Yehova ndili mʼdzenje lozama;
2 Ambuye imvani mawu anga.
Makutu anu akhale tcheru kumva
kupempha chifundo kwanga.
3 Inu Yehova, mukanamawerengera machimo,
Inu Yehova, akanayima chilili ndani wopanda mlandu?
4 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro;
nʼchifukwa chake mumaopedwa.
5 Ndimayembekezera Yehova, moyo wanga umayembekezera,
ndipo ndimakhulupirira mawu ake.
6 Moyo wanga umayembekezera Ambuye,
kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
7 Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
pakuti Yehova ali ndi chikondi chosasinthika
ndipo alinso ndi chipulumutso chochuluka.
8 Iye mwini adzawombola Israeli
ku machimo ake onse.
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide.
131 Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza,
maso anga siwonyada;
sinditengeteka mtima
ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
2 Koma moyo wanga ndawutontholetsa
ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa,
moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.
3 Yembekeza Yehova, iwe Israeli,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
64 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
2 Monga momwe moto umatenthera tchire
ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
3 Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
4 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
5 Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
ife tinapitiriza kuchimwa.
Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
6 Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
7 Palibe amene amapemphera kwa Inu
kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
8 Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
9 Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
yatenthedwa ndi moto
ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
Yesu Mbuye wa Sabata
12 Pa nthawi imeneyo Yesu anadutsa pakati pa minda ya tirigu pa tsiku la Sabata. Ophunzira ake anamva njala nayamba kuthyola ngala za tirigu nʼkumadya. 2 Afarisi ataona zimenezi anati kwa Iye, “Taonani! Ophunzira anu akuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata.”
3 Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene anachita Davide pamene iye ndi anzake anamva njala? 4 Analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo iye ndi anzakewo anadya buledi wopatulika amene sikunali kololedwa kwa iwo kudya koma ansembe okha. 5 Kodi simunawerenge mʼmalamulo kuti pa Sabata ansembe mʼNyumba ya Mulungu amaphwanya lamulo la Sabata komabe sawayesa olakwa? 6 Ine ndikuwuzani kuti wamkulu kuposa Nyumba ya Mulunguyo ali pano. 7 Ngati mukanadziwa zomwe mawu awa atanthauza, ‘Ine ndifuna chifundo osati nsembe,’ inu simukanatsutsa osalakwa. 8 Pakuti Mwana wa Munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
Yesu Achiritsa Munthu Wolumala Dzanja
9 Atachoka kumeneko anakalowa mʼsunagoge mwawo. 10 Ndipo mʼmenemo munali munthu wolumala dzanja. Pofuna chifukwa chokamunenezera, iwo anamufunsa Yesu kuti, “Kodi nʼkololedwa kuchiritsa munthu tsiku la Sabata?”
11 Iye anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu ali ndi nkhosa nigwera mʼdzenje tsiku la Sabata, kodi simudzayigwira ndi kuyitulutsa kunja? 12 Nanga munthu sali oposa nkhosa kwambiri! Chifukwa chake nʼkololedwa kuchita zabwino pa Sabata.”
13 Pamenepo Yesu anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola ndipo linakhala monga linalili kale. 14 Koma Afarisi anatuluka kunja ndi kukonza njira yoti amuphere.
Mtumiki Wosankhidwa ndi Mulungu
15 Podziwa zimenezi, Yesu anachoka kumalo amenewo. Ambiri anamutsata Iye ndipo anachiritsira odwala awo onse 16 nawachenjeza kuti asamuwulule kuti yani. 17 Uku kunali kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
18 “Taonani mnyamata wanga amene ndinamusankha,
Wokondedwa wanga, amene moyo wanga ukondwera naye.
Pa Iye ndidzayika Mzimu wanga,
ndipo Iye adzalalikira chiweruzo kwa akunja.
19 Sadzalimbana, sadzafuwula,
ngakhale mmodzi sadzamva mawu ake mʼmakwalala.
20 Bango lophwanyika sadzalithyola,
ndi nyale yofuka sadzayizimitsa,
kufikira Iye adzatumiza chiweruziro chikagonjetse.
21 Ndipo akunja adzakhulupirira dzina lake.”
Mwano wa Afarisi
22 Pomwepo anthu anabwera naye kwa Yesu munthu wogwidwa ndi chiwanda amene anali wosaona ndi wosamva ndipo Yesu anamuchiritsa kotero kuti atatha anayamba kumva ndi kuona. 23 Anthu onse anadabwa ndipo anati, “Kodi uyu ndi kukhala mwana wa Davide?”
24 Koma Afarisi atamva zimenezi, anati, “Uyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mkulu wa ziwandazo.”
25 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse ukagawanika mwa iwo udzawonongeka ndi mzinda uliwonse kapena banja likagawanika, mwa izo zokha sizidzayima. 26 Ngati Satana atulutsa Satana, iye adzigawa yekha. Nanga ufumu wake ungayime bwanji? 27 Ndipo ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi Belezebule, anthu anu amatulutsa ziwandazo ndi chiyani? Potero tsono adzakhala oweruza anu. 28 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Mzimu wa Mulungu, pamenepo ufumu wa Mulungu wafika pa inu.
29 “Kapenanso wina aliyense angathe bwanji kulowa mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kunyamulamo zinthu zake, sipokhapo atayamba wamanga munthu wa mphamvuyo? Pamenepo iye akhoza kuba mʼnyumbamo.
30 “Iye amene sali ndi Ine atsutsana nane ndipo iye amene sasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amamwaza. 31 Ndipo potero Ine ndikuwuzani inu, tchimo lililonse ndi cha mwano chilichonse zidzakhululukidwa kwa anthu koma chamwano cha pa Mzimu Woyera, sichidzakhululukidwa. 32 Aliyense amene anena mawu otsutsana ndi Mwana wa Munthu adzakhululukidwa koma aliyense wonena motsutsana ndi Mzimu Woyera sadzakhululukidwa mu mʼbado uno kapena umene ukubwerawo.
Mtengo ndi Zipatso Zake
33 “Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino ndipo mtengo woyipa umabalanso zipatso zoyipa, pajatu mtengo umadziwika ndi zipatso zake. 34 Ana anjoka inu, woyipa inu, mungathe bwanji kuyankhula kanthu kalikonse kabwino? Pakuti pakamwa pamayankhula zosefuka kuchokera mu mtima. 35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zomwe zili mumtima mwake ndipo munthu woyipa amatulutsanso zinthu zoyipa zomwe zili mwa iye. 36 Ine ndikukuwuzani kuti pa tsiku la chiweruziro munthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mawu aliwonse wopanda pake amene anayankhula. 37 Pakuti ndi mawu anu mudzapezeka osalakwa ndiponso ndi mawu anu mudzapezeka olakwa.”
Chizindikiro cha Yona
38 Pamenepo ena mwa Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anati kwa Iye, “Aphunzitsi, tikufuna tione chizindikiro chodabwitsa kuchokera kwa Inu.”
39 Iye anayankha kuti, “Mʼbado woyipa ndi wachigololo ufunsa za chizindikiro chodabwitsa! Koma ndi chimodzi chomwe sichidzapatsidwa kwa inu kupatula chizindikiro cha mneneri Yona. 40 Pakuti monga Yona anali mʼmimba mwa nsomba yayikulu masiku atatu, usana ndi usiku, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala masiku atatu, usana ndi usiku, mʼkati mwa nthaka. 41 Anthu a ku Ninive adzayimirira pachiweruzo ndi mʼbado uwu ndi kuwutsutsa pakuti iwo analapa Yona atalalikira ndipo tsopano wamkulu kuposa Yona ali pano. 42 Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira pa tsiku lachiweruzo ndi mʼbado uwu ndipo idzawutsutsa pakuti inachokera kumathero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni, ndipo pano pali woposa Solomoni.
Za Mzimu Woyipa
43 “Pamene mzimu woyipa utuluka mwa munthu, umadutsa malo wopanda madzi kufunafuna malo opumulira ndipo suwapeza. 44 Pamenepo umati, ‘Ndidzabwerera ku nyumba yanga komwe ndinatuluka.’ Pamene ufika, upeza mopanda kanthu, mosesedwa ndi mokonzedwa bwino. 45 Kenaka umapita kukatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa uwowo ndipo imapita ndi kukakhala mʼmenemo. Choncho khalidwe lotsiriza la munthu uyu limakhala loyipa kwambiri kuposa loyambalo. Umo ndi mmene zidzakhalire ndi mʼbado oyipawu.”
Amayi ndi Abale Ake a Yesu
46 Pamene Yesu anali kuyankhulabe ndi gulu la anthu, amayi ndi abale ake anayimirira kunja, akufuna kuyankhulana naye. 47 Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunjaku akufuna kuyankhulana nanu.”
48 Iye anayankha kuti, “Amayi anga ndani ndipo abale anga ndi ndani?” 49 Ndipo akuloza ophunzira ake, Iye anati, “Awa ndiwo amayi anga ndi abale anga. 50 Pakuti aliyense amene achita chifuniro cha Atate anga akumwamba ndiye mʼbale wanga, mlongo wanga ndi amayi anga.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.