M’Cheyne Bible Reading Plan
Debora
4 Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. 2 Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. 3 Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri.
4 Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. 5 Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. 6 Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. 7 Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ”
8 Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.”
9 Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. 10 Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi.
11 Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi.
12 Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, 13 anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni.
14 Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. 15 Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. 16 Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala.
17 Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja.
18 Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda.
19 Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso.
20 Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ”
21 Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo.
22 Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake.
23 “Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. 24 Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu.
8 Ndipo Saulo anavomerezana nawo pa imfa ya Stefano.
Kuzunzika kwa Mpingo
Tsiku lomwelo, mpingo wa mu Yerusalemu unayamba kuzunzidwa, ndipo onse, kupatulapo atumwi, anabalalikira ku madera onse a Yudeya ndi Samariya. 2 Anthu okonda Mulungu anayika maliro a Stefano ndipo anamulira kwambiri. 3 Koma Saulo anayamba kuwononga mpingo. Amapita nyumba ndi nyumba, ndipo amagwira amuna ndi amayi ndi kukawatsekera ku ndende.
Filipo ku Samariya
4 Okhulupirira amene anabalalika amalalikira konse kumene amapita. 5 Filipo anapita ku mzinda wa ku Samariya ndipo analalikira za Khristu kumeneko. 6 Gulu la anthu litamva Filipo akulalikira komanso kuona zizindikiro zozizwitsa zimene ankazichita, onse anamvetsetsa zimene iye amanena. 7 Mizimu yoyipa inatuluka mwa anthu ambiri ikufuwula kwambiri ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo ndi olumala anachiritsidwa. 8 Kotero munali chimwemwe chachikulu mu mzindawo.
Simoni Wamatsenga
9 Koma mu mzindawo munali munthu dzina lake Simoni, amene amachita za matsenga ndi kudabwitsa anthu a mu Samariya. Iye amadzitamandira kuti ndi wopambana, 10 ndipo anthu onse, aakulu ndi aangʼono anamumvera ndi kunena kuti, “Munthu uyu ndi mphamvu ya Mulungu yotchedwa Mphamvu yayikulu.” 11 Anthu amamutsata chifukwa kwa nthawi yayitali amawadabwitsa ndi matsenga akewo. 12 Koma atakhulupirira Filipo akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ndiponso dzina la Yesu Khristu, anthuwo anabatizidwa amuna ndi amayi. 13 Nayenso Simoni anakhulupirira ndipo anabatizidwa, natsatira Filipo kulikonse, ndipo anadabwa kwambiri pamene anaona zizindikiro zazikulu ndi zozizwitsa.
14 Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane. 15 Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera, 16 chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 17 Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
18 Simoni ataona kuti Mzimu anaperekedwa kwa iwo atumwi atawasanjika manja, iye anafuna kuwapatsa ndalama ndipo anati, 19 “Inenso ndipatseni mphamvu imeneyi kuti aliyense amene ndimusanjika manja anga azilandira Mzimu Woyera.”
20 Petro anayankha kuti, “Ndalama zako utayike nazo pamodzi, chifukwa unaganiza kuti ungathe kugula mphatso ya Mulungu ndi ndalama! 21 Ulibe gawo kapena mbali pa utumikiwu, chifukwa mtima wako suli wolungama pamaso pa Mulungu. 22 Lapa zoyipa zakozi ndipo upemphere kwa Ambuye. Mwina adzakukhululukira maganizo a mu mtima mwako. 23 Pakuti ine ndikuona kuti ndiwe wowawidwa mtima ndiponso kapolo wa tchimo.”
24 Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.”
25 Atatha kuchitira umboni ndi kulalikira mawu a Ambuye, Petro ndi Yohane anabwerera ku Yerusalemu, atalalikira Uthenga Wabwino mʼmidzi yambiri ya Asamariya.
Filipo ndi Nduna ya Zachuma ya ku Etiopia
26 Mngelo wa Ambuye anati kwa Filipo, “Nyamuka pita chakummwera, ku msewu wa ku chipululu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu.” 27 Ndipo ananyamuka napita, ndipo akuyenda anakumana ndi munthu wa ku Etiopia wa udindo waukulu woyangʼanira chuma cha Kandake, mfumu yayikazi ya ku Etiopia. Munthu ameneyu anapita ku Yerusalemu kukapembedza Mulungu, 28 ndipo akubwerera kwawo atakwera pa galeta lake amawerenga buku la mneneri Yesaya. 29 Mzimu anamuwuza Filipo kuti, “Pita pa galeta ilo ndipo ukakhale pafupi nalo.”
30 Pamenepo Filipo anathamangira ku galeta ndipo anamva munthuyo akuwerenga buku la mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti, “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazi?”
31 Iye anayankha kuti, “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Ndipo iye anayitana Filipo kuti abwere ndikukhala naye mʼgaleta.
32 Mawu amene ndunayo imawerenga anali awa:
“Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
33 Iye ananyozedwa ndipo panalibe chilungamo pa mlandu wake.
Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake
poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?”
34 Ndunayo inamufunsa Filipo kuti, “Chonde, uzeni, kodi mneneri akuyankhula za ndani, za iye mwini kapena za munthu wina?” 35 Pamenepo Filipo anayambira pa malemba omwewo kumuwuza za Uthenga Wabwino wa Yesu.
36 Akuyenda mu msewu anafika pamalo pamene panali madzi ndipo ndunayo inati, “Taonani madzi awa. Kodi pali chondiletsa kuti ndibatizidwe?” 37 Filipo anati, “Ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse mukhoza kubatizidwa.” Ndunayo inayankha kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.” 38 Ndipo analamulira galeta kuti liyime. Onse awiriwo, Filipo ndi Ndunayo anatsika ndi kulowa mʼmadzi ndipo Filipo anamubatiza. 39 Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.
17 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,
lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.
Uchimowo walembedwa pa mitima yawo
ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
2 Ngakhale ana awo amakumbukira
maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,
pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,
pa mapiri aatali mʼdzikomo.
3 Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense
ndidzazipereka kwa ofunkha
kuti zikhale dipo lawo
chifukwa cha machimo
ochitika mʼdziko lonse.
4 Mudzataya dziko limene ndinakupatsani
kuti likhale cholowa chanu.
Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu
mʼdziko limene inu simukulidziwa,
chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,
ndipo udzayaka mpaka muyaya.”
5 Yehova akuti,
“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,
amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize
pamene mtima wake wafulatira Yehova.
6 Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;
iye sadzapeza zabwino.
Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,
mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.
7 “Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,
amene amatsamira pa Iye.
8 Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi
umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.
Mtengowo suopa pamene kukutentha;
masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.
Suchita mantha pa chaka cha chilala
ndipo sulephera kubereka chipatso.”
9 Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse
ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.
Ndani angathe kuwumvetsa?
10 “Ine Yehova ndimafufuza mtima
ndi kuyesa maganizo,
ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake
ndiponso moyenera ntchito zake.”
11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo
ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.
Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,
ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
12 Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero
wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.
13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,
onse amene amakusiyani adzachita manyazi.
Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi
chifukwa anakana Yehova,
kasupe wa madzi amoyo.
14 Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;
pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,
chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
15 Anthu akumandinena kuti,
“Mawu a Yehova ali kuti?
Zichitiketu lero kuti tizione!”
16 Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.
Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.
Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
17 Musandichititse mantha;
ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.
18 Ondizunza anga achite manyazi,
koma musandichititse manyazi;
iwo achite mantha kwambiri,
koma ine mundichotsere manthawo.
Tsiku la mavuto liwafikire;
ndipo muwawononge kotheratu.
Kusunga Tsiku la Sabata
19 Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. 20 Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ 21 Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. 22 Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. 23 Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. 24 Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. 25 Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. 26 Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. 27 Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”
Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja
3 Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. 2 Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. 3 Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”
4 Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
5 Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira. 6 Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.
Magulu a Anthu Amutsata Yesu
7 Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. 8 Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. 9 Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. 10 Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. 11 Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” 12 Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
Yesu Asankha Ophunzira Khumi ndi Awiri
13 Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. 14 Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira 15 ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. 16 Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); 17 Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); 18 Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, 19 ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
Yesu ndi Belezebabu
20 Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. 21 Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
22 Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
23 Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. 25 Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. 26 Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. 27 Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. 28 Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, 29 koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”
30 Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
Amayi ndi Abale ake a Yesu
31 Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. 32 Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
33 Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”
34 Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga! 35 Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.