M’Cheyne Bible Reading Plan
Yehowahazi Mfumu ya Israeli
13 Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo. 3 Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse.
4 Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli. 5 Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale. 6 Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya.
7 Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.
8 Ntchito zina za Yehowahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 9 Yehowahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya. Ndipo Yowasi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehowasi Mfumu ya Israeli
10 Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16. 11 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli.
12 Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? 13 Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli.
14 Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!”
15 Elisa anamuwuza kuti, “Tenga uta ndi mivi.” Ndipo anaterodi. 16 Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo.
17 Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.”
18 Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka. 19 Munthu wa Mulungu anapsera mtima mfumuyo ndipo anati, “Ukanalasa pansi kasanu kapena kasanu nʼkamodzi. Pamenepo ukanatha kuwagonjetsa Aaramu ndi kuwawononga kwathunthu. Koma tsopano udzawagonjetsa katatu kokha.”
20 Elisa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda.
Tsono magulu a ankhondo a Amowabu ankabwera kudzalowa ndi kudzathira nkhondo dzikolo nthawi ya dzinja. 21 Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira.
22 Hazaeli mfumu ya Aramu inazunza Aisraeli nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehowahazi. 23 Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.
24 Hazaeli mfumu ya Aramu inamwalira ndipo mwana wake Beni-Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. 25 Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.
Zoopsa za Mʼmasiku Otsiriza
3 Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri. 2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. 3 Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, 4 opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. 5 Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
6 Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu, 7 amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi. 8 Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa. 9 Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.
Paulo Alimbikitsa Timoteyo
10 Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, 11 mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi. 12 Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, 13 pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso. 14 Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi. 15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. 16 Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo 17 kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.
Chiweruzo cha Israeli
5 “Ansembe inu, imvani izi!
Inu Aisraeli, tcherani khutu!
Inu nyumba yaufumu, mvetserani!
Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu:
Inu munali ngati msampha ku Mizipa,
munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
2 Owukira azama mʼmoyo wakupha,
Ine ndidzawalanga onsewo.
3 Ndimadziwa zonse za Efereimu;
Aisraeli ndi osabisika kwa Ine.
Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere;
Israeli wadziyipitsa.
4 “Ntchito zawo siziwalola
kubwerera kwa Mulungu wawo.
Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere;
Iwo sadziwa Yehova.
5 Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa;
Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo;
Yudanso anagwa nawo pamodzi.
6 Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo
kukapereka nsembe kwa Yehova,
iwo sadzamupeza;
Iye wawachokera.
7 Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova;
amabereka ana amʼchigololo
ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano
chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
8 “Womba lipenga mu Gibeya,
liza mbetete mu Rama.
Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni;
iwe Benjamini tsogolera.
9 Efereimu adzasanduka bwinja
pa tsiku la chilango.
Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi
pakati pa mafuko a Israeli.
10 Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu
amene amasuntha miyala ya mʼmalire.
Ndidzawakhutulira ukali wanga
ngati madzi a chigumula.
11 Efereimu waponderezedwa,
akulangidwa chifukwa chotsatira
mafano.
12 Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu,
ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
13 “Efereimu ataona nthenda yake,
ndi Yuda ataona zilonda zake,
pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya,
ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza.
Koma mfumuyo singathe kukuchizani,
singathe kuchiritsa mabala anu.
14 Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu.
Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda.
Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo;
ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
15 Ndipo ndidzabwerera ku malo anga
mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo.
Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga;
mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
Kusalapa kwa Israeli
6 “Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Iye watikhadzula,
koma adzatichiritsa.
Iye wativulaza,
koma adzamanga mabala athu.
2 Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa;
pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa
kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
3 Tiyeni timudziwe Yehova,
tiyeni tilimbike kumudziwa Iye.
Adzabwera kwa ife mosakayikira konse
ngati kutuluka kwa dzuwa;
adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe,
ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
4 Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani?
Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda?
Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa,
ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
5 Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga,
ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga;
chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
6 Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe,
ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
7 Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa,
iwo sanakhulupirike kwa Ine.
8 Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa,
okhala ndi zizindikiro za kuphana.
9 Monga momwe mbala zimadikirira anthu,
magulu a ansembe amachitanso motero;
iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu,
kupalamula milandu yochititsa manyazi.
10 Ndaona chinthu choopsa kwambiri
mʼnyumba ya Israeli.
Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere,
ndipo Israeli wadzidetsa.
11 “Kunenanso za iwe Yuda,
udzakolola chilango.
“Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”
Kofu
145 Ndimayitana ndi mtima wanga wonse; ndiyankheni Inu Yehova,
ndipo ndidzamvera zophunzitsa zanu.
146 Ndikuyitana kwa Inu; pulumutseni
ndipo ndidzasunga umboni wanu.
147 Ndimadzuka tambala asanalire kuti ndipemphe thandizo;
chiyembekezo changa chili mʼmawu anu.
148 Maso anga amakhala chipenyere nthawi yonse ya usiku,
kuti ndithe kulingalira malonjezo anu.
149 Imvani mawu anga molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
Yehova sungani moyo wanga, molingana ndi malamulo anu.
150 Iwo amene amakonza njira zoyipa andiyandikira,
koma ali kutali ndi malamulo anu.
151 Koma Inu Yehova muli pafupi,
malamulo anu onse ndi woona.
152 Ndinaphunzira kalekale kuchokera mʼmaumboni anu
kuti maumboni amene munakhazikitsawo ndi amuyaya.
Reshi
153 Yangʼanani masautso anga ndipo mundipulumutse,
pakuti sindinayiwale malamulo anu.
154 Mundiyimirire pa mlandu wanga ndi kundiwombola;
sungani moyo wanga molingana ndi lonjezo lanu.
155 Chipulumutso chili kutali ndi anthu oyipa,
pakuti iwowo safunafuna zophunzitsa zanu.
156 Chifundo chanu Yehova nʼchachikulu;
sungani moyo wanga molingana ndi malamulo anu.
157 Adani amene akundizunza ndi ambiri,
koma ine sindinatembenuke kuchoka pa umboni wanu.
158 Ndimawayangʼana monyansidwa anthu opanda chikhulupiriro,
popeza samvera mawu anu.
159 Onani momwe ndimakondera malangizo anu;
sungani moyo wanga, Inu Yehova, molingana ndi chikondi chanu chosanthika.
160 Mawu anu onse ndi owona;
malamulo anu onse olungama ndi amuyaya.
Sini ndi Shini
161 Olamulira amandizunza popanda chifukwa,
koma mtima wanga umanjenjemera ndi mawu anu.
162 Ine ndimakondwa ndi lonjezo lanu,
ngati munthu amene wapeza chuma chambiri.
163 Ndimadana ndi chinyengo, kwambiri ndimanyansidwa nacho,
koma ndimakonda malamulo anu.
164 Ndimakutamandani kasanu ndi kawiri pa tsiku
pakuti malamulo anu ndi olungama.
165 Amene amakonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu,
ndipo palibe chimene chingawapunthwitse
166 Ndikudikira chipulumutso chanu, Inu Yehova,
ndipo ndimatsatira malamulo anu.
167 Ndimamvera umboni wanu
pakuti ndimawukonda kwambiri.
168 Ndimamvera malangizo anu ndi umboni wanu,
pakuti njira zanga zonse ndi zodziwika pamaso panu.
Tawu
169 Kulira kwanga kufike pamaso panu Yehova;
patseni nzeru zomvetsa zinthu molingana ndi mawu anu.
170 Kupempha kwanga kufike pamaso panu;
pulumutseni molingana ndi lonjezo lanu.
171 Matamando asefukire pa milomo yanga,
pakuti Inu mumandiphunzitsa malamulo anu.
172 Lilime langa liyimbe mawu anu,
popeza malamulo anu onse ndi olungama.
173 Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza
pakuti ndasankha malangizo anu.
174 Ndikufunitsitsa chipulumutso chanu Yehova,
ndipo ndimakondwera ndi malamulo anu.
175 Loleni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni,
ndipo malamulo anu andichirikize.
176 Ndasochera ngati nkhosa yotayika,
funafunani mtumiki wanu,
pakuti sindinayiwale malamulo anu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.