M’Cheyne Bible Reading Plan
Eliya ndi Obadiya
18 Patapita masiku ambiri, mʼchaka chachitatu cha chilala, Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Pita ukadzionetse kwa Ahabu ndipo ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.” 2 Choncho Eliya anapita kukadzionetsa kwa Ahabu.
Tsono nthawi imeneyi njala inakula kwambiri mu Samariya, 3 ndipo Ahabu anayitana Obadiya amene ankayangʼanira nyumba yake yaufumu. (Obadiya ankaopa Yehova kwambiri. 4 Pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 ndi kuwabisa mʼmapanga awiri, phanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi). 5 Ahabu anawuza Obadiya kuti, “Pita mʼdziko kulikonse kumene kuli zitsime za madzi ndi ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu oti nʼkumadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale ndi moyo, kuti tisaphe chiweto chilichonse.” 6 Choncho anagawana dziko loti apiteko, Ahabu anapita mbali ina, Obadiya nʼkupita ina.
7 Obadiya akuyenda mʼnjira anakumana ndi Eliya. Ndipo taonani, Obadiya anamuzindikira Eliyayo, naweramira pansi ndipo anati, “Kodi ndinu, mbuye wanga Eliya?”
8 Eliya anayankha kuti, “Inde. Pita kawuze mbuye wako kuti, ‘Eliya wabwera.’ ”
9 Obadiya anafunsa kuti, “Kodi ndalakwa chiyani kuti inu mupereke mtumiki wanu kwa Ahabu kuti akaphedwe? 10 Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuye wanga sanatumeko anthu okakufunafunani. Ndipo pamene mtundu wa anthu kapena ufumu unena kuti kuno kulibe, Ahabu ankawalumbiritsa kuti atsimikizedi kuti inuyo kulibe kumeneko. 11 Koma tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ 12 Ine sindikudziwa kumene Mzimu wa Yehova udzakupititsani ine ndikachoka. Ngati ndipita kukamuwuza Ahabu ndipo iye wosadzakupezani, adzandipha. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndi kupembedza Yehova kuyambira ubwana wanga. 13 Mbuye wanga, kodi simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ine ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼmapanga awiri, mʼphanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi akumwa. 14 Ndiye inu tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ Iyeyo adzandipha ndithu!”
15 Eliya anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamutumikira, ine lero ndidzaonekera ndithu pamaso pa Ahabu.”
Eliya pa Phiri la Karimeli
16 Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu, namuwuza, ndipo Ahabu anapita kukakumana ndi Eliya. 17 Pamene Ahabu anaona Eliya, anati kwa iye, “Kodi ndiwedi, munthu wovutitsa Israeli uja?”
18 Eliya anayankha kuti, “Ine sindinavutitse Israeli, koma ndinuyo ndi banja lanu. Mwasiya malamulo a Yehova ndipo mwatsatira Abaala. 19 Tsopano sonkhanitsani anthu a mʼdziko lonse la Israeli kuti akumane nane pa Phiri la Karimeli. Ndipo mubwere nawo aneneri a Baala 450 ndi aneneri a fano la Asera 400, amene amadya pa tebulo la Yezebeli.”
20 Choncho Ahabu anatumiza mawu mʼdziko lonse la Israeli, ndipo anasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimeli. 21 Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.”
Koma anthu aja sanayankhe.
22 Pamenepo Eliya ananena kwa iwo kuti, “Ine ndilipo ndekha mneneri wa Yehova, koma Baala ali ndi aneneri 450. 23 Tibweretsereni ngʼombe zazimuna ziwiri. Iwo asankhepo okha ngʼombe imodzi, ndipo ayidule nthulinthuli ndi kuziyika pa nkhuni nthulizo, koma osakolezapo moto. Ndipo ine ndidzadula nthulinthuli ngʼombe inayo ndi kuyika pa nkhuni koma sindikolezapo moto. 24 Kenaka inu muyitane dzina la mulungu wanu, ndipo ine ndidzayitana dzina la Yehova. Mulungu amene ati ayankhe potumiza moto, iyeyo ndiye Mulungu.”
Pamenepo anthu onse anati, “Izi mwanena zamveka bwino.”
25 Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.” 26 Choncho iwo anatenga ngʼombe yayimunayo imene anawapatsa, nayikonza.
Kenaka anayitana dzina la Baala kuyambira mmawa mpaka masana. Iwo anafuwula kuti, “Inu Baala, tiyankheni ife.” Koma panalibe yankho; palibe amene anayankha. Ndipo anavinavina mozungulira guwa lansembe limene anapanga.
27 Nthawi yamasana Eliya anayamba kuwanyogodola ndipo anati, “Fuwulani kwambiri. Ndithudi, iye ndi mulungu! Mwinatu akulingalira kwambiri, kapena watanganidwa, kapena ali paulendo. Mwina wagona ndipo nʼkofunika kuti adzutsidwe.” 28 Choncho iwo anafuwula kwambiri ndi kudzichekacheka ndi malupanga ndi mikondo, potsata miyambo yawo, mpaka kutuluka magazi. 29 Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.
30 Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka. 31 Eliya anatenga miyala 12, mwala uliwonse kuyimira fuko lililonse la Yakobo, amene Yehova anamuwuza kuti, “Dzina lako lidzakhala Israeli.” 32 Ndi miyala imeneyo anamanga guwa mʼdzina la Yehova, ndipo anakumba ngalande yayikulu yolowa malita 15 a madzi kuzungulira guwalo. 33 Anayika nkhuni zija mʼmalo mwake nadula nthulinthuli ngʼombe yayimuna ija ndi kuyika nthulizo pa nkhunipo. Pamenepo Eliya anati, “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi ndipo muwathire pa nyama ya nsembeyo ndi nkhunizo.”
34 Eliya anati, “Thiraninso kachiwiri.” Anthu aja anathiranso madziwo kachiwiri.
Iye analamula kuti, “Thiraninso kachitatu.” Ndipo iwo anathiranso kachitatu. 35 Madziwo anayenderera pansi kuzungulira guwa lansembe, nadzaza ngalande yonse.
36 Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. 37 Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.”
38 Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.
39 Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”
40 Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.
41 Ndipo Eliya anati kwa Ahabu, “Pitani, kadyeni ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.” 42 Choncho Ahabu anapita kukadya ndi kumwa, koma Eliya anakwera pamwamba pa Phiri la Karimeli, ndipo anawerama mpaka pansi, nayika mutu wake pakati pa mawondo ake.
43 Eliya anawuza mtumiki wake kuti, “Pita kayangʼane ku nyanja.” Ndipo iye anapita nakayangʼana.
Mtumikiyo anati, “Kulibe kanthu.”
Kasanu nʼkawiri Eliya anati, “Pitanso.”
44 Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, “Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja.”
Pamenepo Eliya anati, “Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ ”
45 Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli. 46 Dzanja la Yehova linali pa Eliya ndipo atamangira lamba chovala chake, anathamanga ndi kumupitirira Ahabu mpaka kukhala woyamba kukafika ku Yezireeli.
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.
Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
Chisomo ndi mtendere kwa inu.
Kuyamikira Chikhulupiriro cha Atesalonika
2 Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. 3 Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.
4 Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani, 5 chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. 6 Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. 7 Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya. 8 Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu, 9 pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10 Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.
Magawidwe ka Dziko
48 “Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.
2 “Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
3 “Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
4 “Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
5 “Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
6 “Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
7 “Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
8 “Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.
9 “Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 10 Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. 11 Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera. 12 Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.
13 “Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. 14 Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.
15 “Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati. 16 Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250. 17 Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125. 18 Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda. 19 Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli. 20 Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.
21 “Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu. 22 Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.
23 “Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.
24 “Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
25 “Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
26 “Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
27 “Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
28 “Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
29 “Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Zipata za Mzinda
30 “Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250, 31 kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.
32 “Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.
33 “Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.
34 “Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.
35 “Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000.
“Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala:
Yehova Ali Pano.”
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;
madziwo amayenda pakati pa mapiri.
11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;
abulu akuthengo amapha ludzu lawo.
12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;
zimayimba pakati pa thambo.
13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;
dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.
14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,
ndi zomera, kuti munthu azilima
kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,
mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,
ndi buledi amene amapereka mphamvu.
16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,
mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.
17 Mbalame zimamanga zisa zawo;
kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.
18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale;
mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.
19 Mwezi umasiyanitsa nyengo
ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.
20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,
ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.
21 Mikango imabangula kufuna nyama,
ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.
22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;
imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.
23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,
kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.
27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
izo zimalengedwa
ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.
31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.
33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
pamene ndikusangalala mwa Yehova.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.