Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 20

Beni-Hadadi Athira Nkhondo Samariya

20 Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ”

Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.”

Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”

Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”

Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.”

Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.

10 Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”

11 Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ”

12 Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.

Ahabu Agonjetsa Beni-Hadadi

13 Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

14 Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”

Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”

Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”

Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”

15 Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. 16 Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. 17 Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.

Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”

18 Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.”

19 Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. 20 Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. 21 Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa.

22 Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”

23 Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo. 24 Inu chitani izi: chotsani mafumu onse pa maudindo awo ndipo mʼmalo mwawo muyikemo atsogoleri a ankhondo. 25 Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo.

26 Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli. 27 Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo.

28 Munthu wa Mulungu anabwera, nawuza mfumu ya Israeli kuti, “Yehova akuti, ‘Popeza Aaramu akuganiza kuti Yehova ndi mulungu wa ku mapiri, osati wa ku zigwa, Ine ndidzapereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

29 Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha. 30 Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.

31 Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.”

32 Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ”

Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.”

33 Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!”

Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake.

34 Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.”

Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite.

Mneneri Adzudzula Ahabu

35 Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana.

36 Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha.

37 Mneneriyo anapeza munthu wina ndipo anamuwuza kuti, “Chonde, menye.” Choncho munthuyo anamumenya ndi kumuvulaza. 38 Pamenepo mneneriyo anapita nakayima pa msewu kudikirira mfumu. Iye anadzibisa nakulunga nsalu nkhope yake. 39 Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’ 40 Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.”

Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.”

41 Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. 42 Iye anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chakuti mwamasula munthu amene Ine ndinati ndi woyenera kuphedwa, inuyo ndi amene mudzaphedwe mʼmalo mwa iyeyo, anthu anu mʼmalo mwa anthu ake.’ ” 43 Mwachisoni ndi mokwiya, mfumu ya Israeli inapita ku nyumba yake yaufumu ku Samariya.

1 Atesalonika 3

Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.

Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo

Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.

11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

Danieli 2

Maloto a Nebukadinezara

Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona. Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”

Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”

Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja. Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”

Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.”

Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita. Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”

10 Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. 11 Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”

12 Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe. 13 Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe.

14 Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni. 15 Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli. 16 Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake.

17 Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 18 Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni. 19 Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba, 20 ndipo anati:

“Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi;
    nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake.
21 Amasintha nthawi ndi nyengo;
    amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso.
Amapatsa nzeru kwa anzeru
    ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.
22 Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika;
    amadziwa zimene zili mu mdima,
    ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.
23 Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga:
    mwandipatsa nzeru ndi mphamvu,
mwandiwululira zomwe tinakupemphani,
    mwatiwululira maloto a mfumu.”

Danieli Atanthauzira Maloto

24 Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.”

25 Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.”

26 Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?”

27 Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, 28 koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:

29 “Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. 30 Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.

31 “Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe. 32 Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa. 33 Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo. 34 Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya. 35 Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.

36 “Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. 37 Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero; 38 Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.

39 “Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. 40 Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. 41 Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. 42 Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka. 43 Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo.

44 “Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya. 45 Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa.

“Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”

46 Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani. 47 Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”

48 Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru. 49 Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.

Masalimo 106

106 Tamandani Yehova.

Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
    kapena kumutamanda mokwanira?
Odala ndi amene amasunga chilungamo,
    amene amachita zolungama nthawi zonse.
Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
    bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
    kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
    ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.

Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
    tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
Pamene makolo athu anali mu Igupto,
    sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
    ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
    kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
    anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
    anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo,
    palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
    ndi kuyimba nyimbo zamatamando.

13 Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita,
    ndipo sanayembekezere uphungu wake.
14 Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo;
    mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
15 Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha,
    koma anatumiza nthenda yowondetsa.

16 Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni,
    amene Yehova anadzipatulira.
17 Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani;
    inakwirira gulu la Abiramu.
18 Moto unayaka pakati pa otsatira awo;
    lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.

19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
    ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo
    ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
    amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu
    ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
    pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
    ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.

24 Motero iwo ananyoza dziko lokoma;
    sanakhulupirire malonjezo ake.
25 Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo
    ndipo sanamvere Yehova.
26 Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake,
    kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
27 kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina
    ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.

28 Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori
    ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
29 anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa,
    ndipo mliri unabuka pakati pawo.
30 Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo,
    ndipo mliri unaleka.
31 Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake,
    kwa mibado yosatha imene ikubwera.

32 Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova
    ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
33 pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu,
    ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.

34 Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu
    monga momwe Yehova anawalamulira.
35 Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo
    ndi kuphunzira miyambo yawo.
36 Ndipo anapembedza mafano awo,
    amene anakhala msampha kwa iwowo.
37 Anapereka nsembe ana awo aamuna
    ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
38 Anakhetsa magazi a anthu osalakwa,
    magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,
amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani,
    ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
39 Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita;
    ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.

40 Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake
    ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
41 Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina,
    ndipo adani awo anawalamulira.
42 Adani awo anawazunza
    ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
43 Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri,
    koma iwo ankatsimikiza za kuwukira
    ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.

44 Koma Iye anaona kuzunzika kwawo
    pamene anamva kulira kwawo;
45 Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake
    ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
46 Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo
    awamvere chisoni.

47 Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu,
    ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina
kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera
    ndi kunyadira mʼmatamando anu.

48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli,
    Kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Anthu onse anene kuti, “Ameni!”

Tamandani Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.