Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 11-12

Ataliya ndi Yowasi

11 Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu. Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.

Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu, gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo. Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo. Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.”

Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada. 10 Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova. 11 Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.

12 Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”

13 Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo. 14 Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”

15 Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.” 16 Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo.

17 Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu. 18 Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo.

Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. 19 Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu. 20 Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.

21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.

Yowasi Akonzanso Nyumba ya Yehova

12 Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba. Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova masiku onse amene wansembe Yehoyada ankamulangiza. Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.

Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.”

Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo. Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.” Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.

Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. 10 Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. 11 Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, 12 amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.

13 Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova. 14 Ndalamazi anazipereka kwa anthu antchito amene anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. 15 Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri. 16 Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.

17 Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. 18 Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.

19 Ndipo ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 20 Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu ndi kumupha ku Beti Milo, pa njira yotsikira ku Silo. 21 Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

2 Timoteyo 2

Tsono iwe, mwana wanga, limbika mʼchisomo chimene chili mwa Khristu Yesu. Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena. Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu. Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira. Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo. Mlimi wolimbika ndi amene amayembekezereka kukhala woyambirira kulandira gawo la zokolola. Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi.

Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo. 10 Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha.

11 Mawu oyenera kuwadalira ndi awa:

Ngati ife tinafa naye pamodzi,
    tidzakhalanso moyo pamodzi naye.
12 Ngati tinapirira,
    tidzalamuliranso naye pamodzi.
Ngati ife timukana,
    Iye adzatikananso.
13 Ngati ndife osakhulupirika,
    Iye adzakhalabe wokhulupirika
    popeza sangathe kudzikana.

Kuthana ndi Aphunzitsi Onyenga

14 Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. 15 Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola. 16 Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera. 17 Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto. 18 Iwowa apatuka pa choonadi. Iwo amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale, motero amawononga chikhulupiriro cha anthu ena. 19 Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”

20 Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba. 21 Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

22 Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa. 23 Ukane matsutsano oyipa ndi opusa, chifukwa amayambitsa mikangano. 24 Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. 25 Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi. 26 Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.

Hoseya 3-4

Hoseya Ayanjana ndi Mkazi Wake

Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.”

Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.”

Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano. Pambuyo pake Aisraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndi Davide mfumu yawo. Adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzalandira madalitso mʼmasiku awo otsiriza.

Yehova Ayimba Mlandu Israeli

Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova,
    chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu
    amene mumakhala mʼdzikoli:
“Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi
    mulibe kulabadira za Mulungu.
Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha.
    Kuba ndi kuchita chigololo;
machimo achita kunyanya
    ndipo akungokhalira kuphana.
Chifukwa chake dziko likulira
    ndipo onse amene amakhalamo akuvutika;
zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
    ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.

“Koma wina asapeze mnzake chifukwa,
    wina aliyense asayimbe mlandu mnzake,
pakuti anthu ako ali ngati anthu
    amene amayimba mlandu wansembe.
Mumapunthwa usana ndi usiku
    ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi.
Choncho ndidzawononga amayi anu.
    Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.

“Pakuti mwakana kudziwa,
    Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;
chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,
    Inenso ndidzayiwala ana anu.
Ansembe ankati akachuluka
    iwo ankandichimwiranso kwambiri;
    iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
Amalemererapo pa machimo a anthu anga
    ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe.
    Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo,
    ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.

10 “Iwo azidzadya koma sadzakhuta;
    azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana,
chifukwa anasiya Yehova
kuti adzipereke 11     ku zachiwerewere,
ku vinyo wakale ndi watsopano,
    zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
12 za anthu anga.
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo
    ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha.
Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa;
    iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
13 Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri
    ndi kufukiza lubani pa zitunda,
pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi,
    pamene pali mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere
    ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.

14 “Ine sindidzalanga ana anu aakazi
    pamene iwo adzachita zachiwerewere,
kapena akazi a ana anu
    pamene adzachita zigololo.
Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,
    ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako.
    Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!

15 “Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli,
    Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.

“Usapite ku Giligala.
    Usapite ku Beti-Aveni.
    Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
16 Aisraeli ndi nkhutukumve,
    ngosamva ngati ana angʼombe.
Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji
    ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
17 Efereimu waphathana ndi mafano;
    mulekeni!
18 Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha,
    amapitiriza kuchita zachiwerewere;
    atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
19 Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu
    ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.

Masalimo 119:121-144

Ayini

121 Ndachita zolungama ndi zabwino;
    musandisiye mʼmanja mwa ondizunza.
122 Onetsetsani kuti mtumiki wanu akukhala bwino,
    musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.
123 Maso anga alefuka, kufunafuna chipulumutso chanu,
    kufunafuna lonjezo lanu lolungama.
124 Muchite naye mtumiki wanu molingana ndi chikondi chanu chosasinthika,
    ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
125 Ine ndine mtumiki wanu; patseni mzimu wondizindikiritsa,
    kuti ndimvetsetse umboni wanu.
126 Yehova, ndi nthawi yoti muchitepo kanthu;
    malamulo anu akuswedwa.
127 Chifukwa choti ndimakonda malamulo anu
    kuposa golide, kuposa golide woyengeka bwino,
128 ndiponso chifukwa choti ndimaona kuti malangizo anu onse ndi wowongoka,
    ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Pe

129 Maumboni anu ndi odabwitsa
    nʼchifukwa chake ndimawamvera.
130 Mawu anu akamaphunzitsidwa amapereka kuwunika;
    ngakhale anthu wamba amamvetsetsa.
131 Ndimatsekula pakamwa panga ndi kupuma wefuwefu,
    kufunafuna malamulo anu.
132 Tembenukirani kwa ine ndipo mundichitire chifundo,
    monga mumachitira nthawi zonse kwa iwo amene amakonda dzina lanu.
133 Tsogolerani mayendedwe anga molingana ndi mawu anu;
    musalole kuti tchimo lizindilamulira.
134 Ndiwomboleni mʼdzanja la anthu ondizunza,
    kuti ndithe kumvera malangizo anu.
135 Nkhope yanu iwalire mtumiki wanu
    ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
136 Mitsinje ya misozi ikuyenda kuchoka mʼmaso mwanga,
    chifukwa anthu sakumvera malamulo anu.

Tsade

137 Yehova ndinu wolungama,
    ndipo malamulo anu ndi abwino.
138 Maumboni amene munatipatsa ndi olungama;
    ndi odalirika ndithu.
139 Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga
    chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.
140 Mawu anu ndi woyera kwambiri
    nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.
141 Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka,
    sindiyiwala malangizo anu.
142 Chilungamo chanu nʼchamuyaya,
    ndipo malamulo anu nʼchoona.
143 Mavuto ndi masautso zandigwera,
    koma ndimakondwera ndi malamulo anu.
144 Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse;
    patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.