Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 11

Akazi a Solomoni

11 Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake.

Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.

Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse. 10 Ngakhale kuti Yehova anamuletsa Solomoni kutsatira milungu ina, iyeyo sanamvere lamulo la Yehova. 11 Pamenepo Yehova anati kwa Solomoni, “Popeza mtima wako ndi wotere ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo anga amene ndinakuwuza, ndithudi, Ine ndidzawugawa ufumuwu kuwuchotsa kwa iwe ndi kuwupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. 12 Koma chifukwa cha Davide abambo ako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo. Ndidzawugawa mʼdzanja la mwana wako. 13 Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.”

Adani a Solomoni

14 Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, Hadadi Mwedomu, wochokera ku banja laufumu ku Edomu. 15 Kale pamene Davide ankachita nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wa ankhondo, amene anapita kukakwirira Aisraeli akufa, anakantha amuna onse ku Edomu. 16 Yowabu ndi Aisraeli onse anakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi mpaka anawononga amuna onse a ku Edomu. 17 Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake. 18 Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.

19 Farao anamukomera mtima Hadadi ndipo anamupatsa mkazi amene anali mngʼono wake wa Mfumukazi Tahipenesi. 20 Mngʼono wake wa Tahipenesi anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Genubati, amene analeredwa mʼnyumba yaufumu ndi Tahipenesi. Genubatiyo ankakhala limodzi ndi ana a Farao.

21 Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.”

22 Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?”

Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!”

23 Ndipo Mulungu anawutsira Solomoni mdani wina, Rezoni mwana wa Eliada, amene anali atathawa mbuye wake, Hadadezeri mfumu ya ku Zoba. 24 Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira. 25 Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli.

Yeroboamu Awukira Solomoni

26 Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye.

27 Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake. 28 Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe.

29 Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko, 30 ndipo Ahiya anagwira mwinjiro watsopano umene anavala ndi kuwungʼamba zidutswa 12. 31 Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 32 Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha. 33 Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.

34 “ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga. 35 Ndidzalanda ufumu mʼdzanja la mwana wake ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. 36 Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa. 37 Koma kunena za iwe, ndidzakutenga ndipo udzalamulira chilichonse chimene mtima wako ukukhumba; udzakhala mfumu ya Israeli. 38 Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli. 39 Ine ndidzalanga zidzukulu za Davide chifukwa cha zimenezi, koma osati kwamuyaya.’ ”

40 Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.

Kumwalira kwa Solomoni

41 Ntchito zina za Solomoni, zonse zomwe anachita komanso za nzeru zake, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya Solomoni? 42 Solomoni analamulira Aisraeli onse mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. 43 Ndipo anagona ndi makolo ake nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo ake.

Afilipi 2

Kutsanzira Kudzichepetsa kwa Khristu

Ngati muli ndi chilimbikitso chilichonse chifukwa cholumikizana ndi Khristu, ngati muli ndi chitonthozo chifukwa cha chikondi chake, ngati muli ndi mtima umodzi mwa Mzimu, ndipo ngati mumakomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, tsono tsirizani chimwemwe changa pokhala amaganizo ofanana, achikondi chimodzimodzi, amodzi mu mzimu ndi acholinga chimodzinso. Musachite kalikonse ndi mtima odzikonda chabe kapena odzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa ndipo aliyense aziona mnzake ngati womuposa iyeyo. Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena.

Pa ubale wanu wina ndi mnzake, mukhale ndi mtima wofanana ndi wa Khristu Yesu:

Iyeyu, pokhala Mulungu ndithu,
    sanatenge kufanana ndi Mulungu kukhala chinthu choyenera kuchigwiritsa.
Koma anadzichepetsa kotheratu
    nakhala ndi khalidwe ngati la kapolo
    ndi kukhala munthu ngati anthu ena onse.
Ndipo pokhala munthu choncho
    anadzichepetsa yekha
    ndipo anamvera mpaka imfa yake,
        imfa yake ya pamtanda!
Choncho Mulungu anamukweza Iye kukhala wapamwamba kwambiri,
    ndipo anamupatsa dzina loposa dzina lina lililonse
10 kuti pakumva dzina la Yesu, bondo lililonse limugwadire,
    kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi pansi pa dziko,
11 ndipo lilime lililonse livomereze kuti Yesu Khristu ndi Ambuye
    kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Kuwala monga Nyenyezi

12 Tsono, abwenzi anga okondedwa, monga mwakhala omvera nthawi zonse, osati pamene ndinali nanu pokha, koma tsopano koposa pamene ndili kutali. Pitirizani kugwira ntchito ya chipulumutso chanu mwa mantha ndi kunjenjemera, 13 pakuti ndi Mulungu amene amagwira ntchito mwa inu kuti mufune ndi kuchita zimene zimamukondweretsa Iyeyo.

14 Muzichita zonse mosawiringula kapena mosatsutsapo, 15 kuti mukhale wopanda cholakwa ndi angwiro, ana a Mulungu wopanda cholakwika mu mʼbado uno wachinyengo ndi wosocheretsa. Mukatero mudzawala pakati pawo ngati nyenyezi zakumwamba 16 powawuza mawu amoyo. Ndipo ine ndidzatha kunyadira pa tsiku la Khristu kuti sindinathamange kapena kugwira ntchito pachabe. 17 Koma ngakhale ndikuthiridwa ngati nsembe ya chakumwa yoperekedwa pa nsembe ndi pa utumiki wochokera mʼchikhulupiriro chanu, ndine wokondwa ndi wosangalala pamodzi ndi inu nonse. 18 Chomwechonso, inu khalani okondwa ndi osangalala nane pamodzi.

Timoteyo ndi Epafrodito

19 Ngati Ambuye Yesu alola, ndikukhulupirira kuti ndidzamutuma Timoteyo msanga kwanuko, kuti mwina ndingadzasangalale ndikadzamva za moyo wanu. 20 Ndilibenso wina monga iyeyu amene ali ndi chidwi chenicheni pa za moyo wanu. 21 Pakuti aliyense amangofuna zokomera iye yekha osati zokomera Yesu Khristu. 22 Koma inu mukudziwa kuti Timoteyo wadzionetsa yekha, chifukwa watumikira ndi ine pa ntchito ya Uthenga Wabwino monga mwana ndi abambo ake. 23 Choncho ndikuyembekezera kumutuma msanga ndikangodziwa mmene zinthu zanga ziyendere. 24 Ndipo ndikukhulupirira kuti Ambuye akalola ine mwini ndidzafikanso kwanuko posachedwapa.

25 Koma ndikuganiza kuti nʼkofunika kuti ndikutumizireni mʼbale wanga Epafrodito, mtumiki mnzanga ndi msilikali mnzanga, amenenso ndi mtumiki wanu amene munamutumiza kuti adzandithandize pa zosowa zanga. 26 Pakuti akukulakalakani nonsenu ndipo akusauka mu mtima chifukwa munamva kuti akudwala. 27 Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke. 28 Choncho khumbo langa lofulumiza kumutumiza lakula, kuti pamene mumuonenso musangalale komanso kuti nkhawa yanga ichepe. 29 Mulandireni mwa Ambuye ndi chimwemwe chachikulu, ndipo anthu onga iyeyu muziwachitira ulemu. 30 Iyeyu anatsala pangʼono kufa chifukwa cha ntchito ya Khristu, anayika moyo pa chiswe kuti akwaniritse thandizo limene inu simukanatha.

Ezekieli 41

41 Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake. Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.

Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu. Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”

Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake. Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu. Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.

Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu. Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho 10 ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu. 11 Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.

12 Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.

13 Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. 14 Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.

15 Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.

Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo, 16 mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), 17 pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati, 18 anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri: 19 imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse. 20 Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.

21 Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati 22 guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.” 23 Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri. 24 Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana. 25 Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati. 26 Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.

Masalimo 92-93

Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.

92 Nʼkwabwino kutamanda Yehova
    ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
Kulengeza chikondi chanu mmawa,
    ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi
    ndi mayimbidwe abwino a zeze.

Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;
    Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova,
    maganizo anu ndi ozamadi!
Munthu wopanda nzeru sadziwa,
    zitsiru sizizindikira,
kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu
    ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula,
adzawonongedwa kwamuyaya.

Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

Zoonadi adani anu Yehova,
    zoonadi adani anu adzawonongeka;
    onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati;
    mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane,
    makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa,
    adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova,
    adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo,
    adzakhala anthete ndi obiriwira,
15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama;
    Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”
93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
    Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
    dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
    Inu ndinu wamuyaya.

Nyanja zakweza Inu Yehova,
    nyanja zakweza mawu ake;
    nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
    ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
    Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
    chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
    mpaka muyaya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.