M’Cheyne Bible Reading Plan
Kuwukira kwa Mowabu
3 Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga. 3 Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.
4 Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna. 5 Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli. 6 Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse. 7 Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
8 Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?”
Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
9 Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
10 Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
11 Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?”
Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
12 Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
13 Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.”
Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
14 Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe. 15 Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.”
Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa, 16 ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’ 17 Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’ 18 Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu. 19 Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
20 Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
21 Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo. 22 Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo. 23 Ndipo iwo anati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha ndipo aphana. Amowabu, tsopano ndi nthawi yofunkha!”
24 Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu. 25 Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
26 Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera. 27 Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.
Tipempherereni
3 Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. 2 Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. 3 Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. 4 Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. 5 Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.
Awachenjeza za Kusagwira Ntchito
6 Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7 Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8 ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9 Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”
11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
14 Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15 Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.
Malonje Otsiriza
16 Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
17 Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.
18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.
Maloto a Danieli a Zirombo Zinayi
7 Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.
2 Danieli anati, “Mʼmasomphenya anga usiku, ndinaona nyanga yayikulu ikuvunduka ndi mphepo zochokera mbali zonse zinayi za mlengalenga. 3 Ndipo mʼnyangayo munatuluka zirombo zazikulu zinayi, chilichonse chosiyana ndi chinzake.
4 “Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu.
5 “Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’
6 “Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.
7 “Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi.
8 “Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama.
9 “Ine ndikuyangʼanabe ndinaona
“mipando yaufumu ikukhazikitsidwa,
ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake.
Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana;
tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje.
Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto,
ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.
10 Mtsinje wa moto unkayenda,
kuchokera patsogolo pake.
Anthu miyandamiyanda ankamutumikira;
ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake.
Abwalo anakhala malo awo,
ndipo mabuku anatsekulidwa.
11 “Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Zirombo zina zija zinalandidwa ulamuliro wawo, koma zinaloledwa kukhala ndi moyo kwa kanthawi.
13 “Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye. 14 Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.
Tanthauzo la Maloto
15 “Ine Danieli ndinavutika mu mzimu, ndipo zimene ndinaziona mʼmasomphenya zinandisautsa mʼmaganizo. 16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi.
“Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi: 17 ‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi. 18 Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’
19 “Kenaka ndinafuna kudziwa tanthauzo lenileni la chirombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse ndi choopsa kwambiri, cha mano ake achitsulo ndi zikhadabo zamkuwa; chirombo chimene chinapweteka ndi kumeza zinazo ndi kupondaponda chilichonse chimene chinatsala. 20 Ndinafunanso kudziwa za nyanga khumi za pa mutu pake ndiponso ina ija, nyanga imene inaphuka pambuyo pake ndi kugwetsa zitatu zija. Imeneyi ndi nyanga ija yokhala ndi maso ndi pakamwa poyankhula modzitamandira, ndipo inkaoneka yayikulu kupambana zina zonse. 21 Ndikuyangʼanitsitsa, nyanga imeneyi inathira nkhondo anthu oyera mtima ndi kuwagonjetsa, 22 mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu.
23 “Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula. 24 Nyanga khumi zija ndiwo mafumu khumi amene adzatuluka mu ufumu umenewu. Pambuyo pake mfumu ina idzadzuka, yosiyana ndi mafumu a mʼmbuyomu; iyo idzagonjetsa mafumu atatu. 25 Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka.
26 “ ‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya. 27 Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”
28 “Apa ndiye pa mapeto pa nkhaniyi. Ine Danieli, ndinasautsidwa kwambiri mʼmaganizo anga, ndipo nkhope yanga inasandulika, koma ndinasunga nkhaniyi mu mtima mwanga.”
114 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,
nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,
Israeli anasanduka ufumu wake.
3 Nyanja inaona ndi kuthawa,
mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,
timapiri ngati ana ankhosa.
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?
iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,
inu timapiri, ngati ana ankhosa?
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,
pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,
thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.
115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
“Mulungu wawo ali kuti?”
3 Mulungu wathu ali kumwamba;
Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula,
maso ali nawo koma sapenya;
6 makutu ali nawo koma samva,
mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
mapazi ali nawo koma sayenda;
kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israeli,
adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.