Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 9

Yehova Aonekera Solomoni

Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna, Yehova anamuonekera kachiwiri, monga momwe anamuonekera ku Gibiyoni. Yehova ananena kwa iye kuti:

“Ndamva pemphero ndi pembedzero lako pa zimene wapempha pamaso panga. Ndayipatula Nyumba iyi, imene wamanga, poyikamo Dzina langa mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepo nthawi zonse.

“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika, mwangwiro ndi moona mtima monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu pa Israeli mpaka muyaya, monga ndinalonjezera abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu pa mpando waufumu wa Israeli.’

“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Igupto, ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”

Zina zimene Solomoni Anachita

10 Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, 11 Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna. 12 Koma Hiramu atabwera kuchokera ku Turo kudzaona mizinda imene Solomoni anamupatsa, sanasangalatsidwe nayo mizindayo. 13 Iye anafunsa kuti, “Mʼbale wanga, kodi iyi nʼkukhala mizinda yondipatsa?” Ndipo iye anayitcha mizindayo Dziko la Kabuli, dzina lomwe amatchedwa mpaka lero lino. 14 Koma Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide oposa makilogalamu 4,000.

15 Izi ndi zimene anachita Mfumu Solomoni: Analamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Yehova, nyumba yake, malo achitetezo a Milo, mpanda wa Yerusalemu, Hazori, Megido ndi Gezeri. 16 (Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni. 17 Ndipo Solomoni anamanganso Gezeri.) Iye anamanga Beti-Horoni Wakumunsi, 18 Baalati ndi Tadimori ku chipululu, mʼdziko lake lomwelo, 19 pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.

20 Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). 21 Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. 22 Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 23 Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za Solomoni. Anthu okwana 550 ndiwo ankayangʼanira anthu amene ankagwira ntchitowo.

24 Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.

25 Katatu pa chaka Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe limene anamangira Yehova ndiponso ankafukiza lubani pamaso pa Yehova. Potero ankakwaniritsa zoyenera kuchitika mu Nyumba ya Yehova.

26 Mfumu Solomoni anapanganso sitima zapamadzi ku Ezioni Geberi, malo amene ali pafupi ndi Eloti ku Edomu, mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. 27 Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni. 28 Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni.

Aefeso 6

Ana ndi Makolo Awo

Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye.

Antchito ndi Mabwana Awo

Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.

Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.

Zida Zankhondo za Mulungu

10 Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11 Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13 Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14 Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15 Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17 Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18 Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

19 Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20 Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.

Mawu Otsiriza

21 Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. 22 Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni.

23 Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. 24 Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.

Ezekieli 39

39 “Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala. Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli. Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja. Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo. Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’

“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli. Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.

“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 10 Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.

11 “Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.

12 “Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko. 13 Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

14 “Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo. 15 Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. 16 (Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.

17 “Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi. 18 Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani. 19 Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera. 20 Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.

21 “Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. 22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. 23 Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. 24 Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.

25 “Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. 26 Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. 27 Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. 28 Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. 29 Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Masalimo 90

BUKU LACHINAYI

Masalimo 90–106

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
    pa mibado yonse.
Mapiri asanabadwe,
    musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
    kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
    mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
    zili ngati tsiku limene lapita
    kapena ngati kamphindi ka usiku.
Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
    iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
    pofika madzulo wauma ndi kufota.

Ife tathedwa ndi mkwiyo wanu;
    ndipo taopsezedwa ndi kuyipidwa kwanu.
Mwayika mphulupulu zathu pamaso panu,
    machimo athu obisika poonekera pamaso panu.
Masiku athu onse amatha ali pansi pa ukali wanu;
    timatsiriza zaka zathu ndi kubuwula.
10 Kuchuluka kwa masiku athu ndi 70,
    kapena 80 ngati tili ndi mphamvu;
komabe zaka zonsezi ndi za mavuto ndi nkhawa,
    zimatha mofulumira ndipo ife timawulukira kutali.

11 Kodi ndani amadziwa mphamvu ya mkwiyo wanu?
    Pakuti ukali wanu ndi waukulu ngati ulemu umene uyenera Inu.
12 Tiphunzitseni kuwerenga masiku athu molondola,
    kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
    Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
    kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
    kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
    kukongola kwanu kwa ana awo.

17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
    tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
    inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.