M’Cheyne Bible Reading Plan
Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu
6 Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.
2 Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. 3 Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka. 4 Anapanga mazenera amene maferemu ake anali olowa mʼkati mwa makoma a Nyumbayo. 5 Mʼmbali mwa makoma a Nyumba yayikulu ndi chipinda chopatulika chamʼkati, anamanga zipinda zosanjikizana, mozungulira. 6 Chipinda chapansi, mulifupi mwake chinali mamita awiri, chipinda chapakati mulifupi mwake chinali mamita awiri ndi theka ndipo chipinda chapamwamba penipeni mulifupi mwake chinali mamita atatu. Iye anapanga zinthu zosongoka kunja kwa khoma la kunja kuzungulira Nyumbayo kuti asamapise kanthu pa makoma a Nyumba ya Mulungu.
7 Poyimanga Nyumbayo, anagwiritsa ntchito miyala yosemeratu, ndipo pogwira ntchitoyo sipanamveke nyundo, nkhwangwa kapena chida china chilichonse.
8 Chipata cholowera ku chipinda chapansi chinali mbali ya kummwera kwa Nyumbayo. Panali makwerero okwerera ku chipinda chapakati ndiponso chipinda cha pamwamba. 9 Choncho anamanga Nyumbayo mpaka kuyimaliza ndipo denga lake linali la mitanda ndi matabwa a mkungudza. 10 Msinkhu wa chipinda chilichonse unali mamita awiri, ndipo anazilumukiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.
11 Yehova anayankhula ndi Solomoni kuti, 12 “Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako. 13 Ndipo Ine ndidzakhazikika pakati pa ana a Israeli ndipo sindidzawasiya anthu anga Aisraeli.”
14 Kotero Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu nayimaliza. 15 Anakuta khoma la mʼkati mwake ndi matabwa a mkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku denga ndipo pansi pa Nyumbayo anayalapo matabwa a payini. 16 Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri. 17 Chipinda chachikulu chimene chinali kutsogolo kwa Malo Wopatulika Kwambiriwa, chinali mamita 18 mulitali mwake. 18 Mʼkati mwa Nyumbayi munali matabwa a mkungudza, pamene anajambulapo zithunzi za zikho ndi maluwa. Paliponse panali mkungudza wokhawokha. Panalibe mwala uliwonse umene unkaonekera.
19 Anakonza malo wopatulika mʼkati mwa Nyumbayi kuti ayikemo Bokosi la Chipangano cha Yehova. 20 Malo wopatulika a mʼkatiwo anali a mamita asanu ndi anayi mulitali mwake, mulifupi mwake, ndi msinkhu wake. Anakuta mʼkati mwake ndi golide weniweni ndiponso anapanga guwa lansembe la matabwa a mkungudza. 21 Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide. 22 Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.
23 Mʼchipinda chopatulika cha mʼkati anapangamo akerubi awiri a mtengo wa olivi. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. 24 Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita awiri ndi theka, phiko linanso linali mamita awiri ndi theka, kutambasula mapiko awiriwo, kuchokera msonga ina mpaka msonga ina kutalika kwake kunali mamita anayi ndi theka. 25 Kerubi wachiwiriyo msinkhu wake unalinso mamita anayi ndi theka, pakuti akerubi awiriwo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanana. 26 Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. 27 Solomoni anayika akerubiwo mʼchipinda cha mʼkati mwenimweni mwa Nyumba ya Mulungu, atatambasula mapiko awo. Phiko la kerubi wina limakhudza khoma lina, pamene phiko la winayo limakhudza khoma linanso ndipo mapiko awo amakhudzana pakati pa chipindacho. 28 Akerubiwo anawakuta ndi golide.
29 Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa. 30 Anayala golide pansi mu Nyumbamo mʼzipinda zamʼkati ndi zakunja zomwe.
31 Ndipo pa khomo lolowera ku malo wopatulika amʼkati anapanga zitseko za mtengo wa olivi ndipo khonde lake linali ndi mbali zisanu. 32 Ndipo pa zitseko ziwiri zija za mtengo wa olivi anajambulapo kerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa ndipo anapaka golide akerubiwo ndi mitengo ya mgwalangwayo. 33 Anapanganso chimodzimodzi mphuthu za mbali zinayi za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo. 34 Solomoni anapanganso zitseko ziwiri za payini. Chitseko chilichonse chinali ndi mbali ziwiri zotha kuzipinda. 35 Pa zitsekozo anagobapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa wotambasuka ndipo zojambulazo anazikuta ndi golide wopyapyala.
36 Ndipo anamanga bwalo la mʼkati lokhala ndi khoma lokhala ndi mizere itatu ya miyala yosema ndiponso mzere umodzi wa matabwa osemedwa a mkungudza.
37 Maziko a Nyumba ya Yehova anamangidwa pa chaka chachinayi, mwezi wa Zivi. 38 Pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumba anatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Anamanga Nyumbayo kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
Paulo Mlaliki wa Anthu a Mitundu Ina
3 Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina.
2 Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu, 3 ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule. 4 Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu, 5 chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri. 6 Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu.
7 Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu. 8 Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu. 9 Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. 10 Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. 11 Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. 12 Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima. 13 Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu.
Paulo Apempherera Aefeso
14 Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate, 15 amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo. 16 Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, 17 kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi 18 kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. 19 Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini.
20 Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, 21 Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni.
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
36 “Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’ 2 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’ 3 Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani, 4 choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani. 5 Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’ 6 Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’ 7 Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.
8 “Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo. 9 Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa. 10 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso. 11 Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 12 Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.
13 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’ 14 nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero. 15 Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
16 Yehova anandiyankhulanso kuti: 17 “Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake. 18 Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo. 19 Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo. 20 Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’ 21 Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.
22 “Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako. 23 Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
24 “Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. 25 Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. 27 Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. 28 Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 29 Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala. 30 Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala. 31 Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi. 32 Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!
33 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja. 34 Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa. 35 Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu. 36 Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’
37 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa. 38 Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Pemphero la Davide.
86 Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,
pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
2 Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga;
pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga.
3 Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,
pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
4 Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,
pakuti ndimadalira Inu.
5 Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,
wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
6 Yehova imvani pemphero langa;
mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
7 Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,
pakuti Inu mudzandiyankha.
8 Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;
palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
9 Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga
idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;
iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;
Inu nokha ndiye Mulungu.
11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,
ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;
patseni mtima wosagawikana
kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;
ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;
mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.
14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;
anthu ankhanza akufuna kundipha,
amene salabadira za Inu.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;
perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu
ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu
kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,
pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.