Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 19

Eliya Athawira ku Phiri la Horebu

19 Tsono Ahabu anawuza Yezebeli zonse zimene anachita Eliya ndi momwe anaphera aneneri onse ndi lupanga. Choncho Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya kuti akamuwuze kuti, “Milungu indilange, ndipo indilange koopsa, ngati mawa nthawi ngati yomwe ino sindidzakupha iwe monga unaphera aneneriwo.”

Eliya ataona zimenezi, ananyamuka nathawa kupulumutsa moyo wake. Atafika ku Beeriseba ku Yuda, anasiya mtumiki wake kumeneko, ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.” Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.

Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye.” Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.

Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali.” Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu. Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.

Ambuye Aonekera Eliya

Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”

10 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”

11 Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.”

Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. 12 Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. 13 Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.

Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”

14 Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”

15 Yehova anati kwa Eliyayo, “Bwerera njira imene unadzera, ndipo upite ku Chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya ku Aramu. 16 Ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi kuti akhale mfumu ya Israeli, ndiponso ukadzoze Elisa mwana wa Safati wa ku Abeli-Mehola kuti akhale mneneri wolowa mʼmalo mwako. 17 Yehu adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaeli, ndipo Elisa adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu. 18 Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”

Kuyitanidwa kwa Elisa

19 Kotero Eliya anachoka kumeneko, nakapeza Elisa mwana wa Safati. Iye ankatipula ndi mapulawo khumi ndi awiri okokedwa ndi ngʼombe ziwiriziwiri zapamagoli, ndipo iye mwini ankayendetsa goli la khumi ndi chiwiri. Eliya anapita kumene anali namuveka chofunda chake. 20 Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, “Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani.”

Eliya anayankha kuti, “Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?”

21 Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.

1 Atesalonika 2

Utumiki wa Paulo ku Atesalonika

Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa. Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu.

Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu. Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.

10 Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira. 11 Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake, 12 kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.

13 Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. 14 Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda, 15 amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse 16 ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.

Paulo Afunitsitsa Kuonanso Atesalonika

17 Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni. 18 Pakuti ife tinafuna kubweranso kwa inu, makamaka ine Paulo, ndinayesa kangapo koma Satana anatiletsa. 19 Nanga chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu kapena chaufumu chimene ife tidzanyadira pamaso pa Ambuye athu Yesu Khristu pamene abwere ndi chiyani? Kodi si inu? 20 Indedi, inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe.

Danieli 1

Maphunziro a Danieli ku Babuloni

Chaka chachitatu cha ufumu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inabwera ndi kuzinga mzinda wa Yerusalemu ndi kuwuthira nkhondo. Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.

Tsono mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zake kuti abwere nawo ena mwa Aisraeli ochokera mʼbanja laufumu ndi la olemekezeka, achinyamata wopanda chilema, okongola, aluso mu nzeru zonse, okhala ndi chidziwitso, achangu pophunzira, odziwa kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Ndipo anati awaphunzitsenso kuwerenga chiyankhulo cha Ababuloni. Ndipo mfumu imawapatsa tsiku ndi tsiku gawo la chakudya ndi vinyo wa ku nyumba yaufumu, ndi kuti awaphunzitse kwa zaka zitatu, ndipo kenaka adzayambe kutumikira mfumu.

Pakati pa amenewa panali ena ochokera ku Yuda: Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya. Mkulu wa nduna za mfumu anawapatsa mayina atsopano: Danieli anamutcha Belitesezara; Hananiya anamutcha Sadirake; Misaeli anamutcha Mesaki; ndi Azariya anamutcha Abedenego.

Koma Danieli anatsimikiza mtima kuti asadzidetse ndi chakudya ndi vinyo wa mfumu, ndipo anapempha chilolezo kwa mkulu wa nduna za mfumu kuti asadzidetse mwa njira imeneyi. Ndipo Mulungu anafewetsa mtima wa ndunayo kuti amukomere mtima ndi kumuchitira chifundo Danieli, 10 koma ndunayo inamuwuza Danieli kuti, “Ine ndikuchita mantha ndi mbuye wanga mfumu, amene wapereka chakudya ndi chakumwa chanu. Kodi akuoneni inu owonda kuposa anzanu a misinkhu yanu pa chifukwa chanji? Mfumu ikhoza kundidula mutu chifukwa cha iwe.”

11 Ndipo Danieli anati kwa kapitawo amene anali mkulu wa nduna za mfumu amene anamuyika kuti ayangʼanire Danieli, Hananiya, Misaeli ndi Azariya, 12 “Chonde mutiyese ife akapolo anu pa masiku khumi: mutipatse masamba okha kuti tidye ndi madzi akumwa. 13 Ndipo mudzafananize maonekedwe athu ndi a anyamata amene akudya chakudya cha mfumu, ndi kuti mudzachite ndi anyamata anu monga momwe mudzawaonere.” 14 Choncho anawavomera ndipo anawayesa pa masiku khumi.

15 Pakutha pa masiku khumi iwo anaoneka athanzi ndi odya bwino kuposa aliyense wa anyamata amene ankadya chakudya cha mfumu aja. 16 Choncho kapitawo anawachotsera chakudya ndi vinyo za ku nyumba yaufumu zija nawapatsa ndiwo zamasamba basi.

17 Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.

18 Ndipo kumapeto kwa masiku amene mfumu inayika kuti adzaonetse anyamatawa ku nyumba yake, mkulu wa nduna za mfumu uja anawapereka iwo kwa Nebukadinezara. 19 Mfumu inayankhula nawo, ndipo panalibe wofanana ndi Danieli; Hananiya Misaeli ndi Azariya; Choncho analowa ndi kukhala otumikira mfumu. 20 Nthawi zonse mfumu ikawafunsa zonse zofuna nzeru ndi chidziwitso, inkapeza kuti iwo anali oposa amatsenga ndi owombeza onse a mu ufumu wake wonse mopitirira muyeso.

21 Ndipo Danieli anali kumeneko mpaka chaka choyamba cha ufumu wa Koresi.

Masalimo 105

105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
    maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
    mawu amene analamula kwa mibado yonse,
pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
    lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
    kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
    ngati gawo la cholowa chako.”

12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,
    ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,
    kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;
    anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
15 “Musakhudze odzozedwa anga;
    musachitire choyipa aneneri anga.”

16 Iye anabweretsa njala pa dziko
    ndipo anawononga chakudya chonse;
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,
    Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,
    khosi lake analiyika mʼzitsulo,
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,
    mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,
    wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,
    wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira
    ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.

23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;
    Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
24 Yehova anachulukitsa anthu ake;
    ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,
    kukonzera chiwembu atumiki ake.
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,
    ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,
    zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.
    Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,
    kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule
    amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka
    ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,
    ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,
    nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,
    ziwala zosawerengeka;
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,
    zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,
    zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.

37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
    ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
    pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
    ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
    ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
    ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
    linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
    osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
    ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.