Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 21

Munda Wamphesa wa Naboti

21 Zitatha izi, panachitika nkhani yokhudza Naboti wa ku Yezireeli amene anali ndi munda wamphesa ku Yezireeli, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu, mfumu ya ku Samariya. Ahabu anawuza Naboti kuti, “Patse munda wako wa mpesa kuti ukhale munda wanga wa ndiwo zamasamba, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga yaufumu. Mosinthana ndi mundawu ndidzakupatsa wina wabwino, kapena ngati ungafune, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawu.”

Koma Naboti anayankha Ahabu kuti, “Pali Yehova, sindingakupatseni cholowa cha makolo anga.”

Pamenepo Ahabu anapita ku nyumba yake, wachisoni ndi wokwiya chifukwa Naboti wa ku Yezireeli anamuwuza kuti, “Sindidzakupatsani cholowa cha makolo anga.” Ahabu anakagona pa bedi lake atayangʼana kumbali ndipo anakana chakudya.

Yezebeli mkazi wake analowa ndipo anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuoneka achisoni? Chifukwa chiyani simukufuna chakudya?”

Ahabu anayankha mkazi wake kuti, “Chifukwa chake nʼchakuti ine ndinamuwuza Naboti wa ku Yezireeli kuti, ‘Gulitse munda wako wa mpesa kapena ngati ungakonde ine ndidzakupatsa munda wina wabwino mʼmalo mwake.’ Koma iye anandiyankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wa mpesa.’ ”

Ndipo Yezebeli mkazi wake anati, “Kodi umu ndi mmene mumachitira ngati mfumu ya Israeli? Dzukani, idyani! Sangalalani. Ine ndidzakutengerani munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli.”

Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu, nawadinda chidindo cha mfumu, nawatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake. Mʼmakalatamo Yezebeli analemba kuti:

“Lengezani kuti anthu asale chakudya ndipo muyike Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. 10 Koma muyike anthu awiri oyipa mtima moyangʼanana naye ndipo iwo achitire umboni kuti watemberera Mulungu ndiponso mfumu. Ndipo mumutulutse ndi kumuponya miyala ndi kumupha.”

11 Choncho akuluakulu ndi anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake anachita monga analamulira Yezebeli mʼmakalata amene anawalembera. 12 Iwo analengeza kuti anthu asale chakudya ndipo anayika Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. 13 Ndipo anthu awiri oyipa anabwera nakhala moyangʼanana naye ndipo anamunenera zoyipa Naboti pamaso pa anthu, ponena kuti, “Naboti watemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Choncho anamutulutsira kunja kwa mzinda ndi kumuponya miyala ndi kumupha. 14 Atatero anatumiza mawu kwa Yezebeli akuti, “Naboti amuponya miyala ndipo wafa.”

15 Yezebeli atangomva kuti Naboti amuponya miyala ndipo wafa, iye anakamuwuza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli umene anawukaniza kukugulitsani. Naboti sali moyonso, koma wafa.” 16 Ahabu atamva kuti Naboti wafa, ananyamuka kukatenga munda wamphesa wa Naboti.

17 Ndipo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, 18 “Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya Israeli amene amalamulira ku Samariya. Pano ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene wapita kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake. 19 Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ”

20 Ahabu anati kwa Eliya, “Tsono wandipeza, iwe mdani wanga!”

Eliya anayankha kuti, “Inde ndakupezani chifukwa mwadzigulitsa kuti muchite zoyipa pamaso pa Yehova. 21 Iye akuti ‘Taonani, ine ndidzabweretsa mavuto pa iwe. Ndidzawononga kotheratu zidzukulu zako ndi kuchotsa mu Israeli munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu. 22 Ndidzawononga nyumba yako monga momwe ndinawonongera nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya, chifukwa wandikwiyitsa Ine ndi kuchimwitsa Israeli.’

23 “Ndipo kunena za Yezebeli, Yehova akuti, ‘Agalu adzadya Yezebeli mʼmbali mwa khoma la Yezireeli.’

24 “Agalu adzadya munthu aliyense wa nyumba ya Ahabu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya aliyense wofera ku thengo.”

25 (Kunalibe munthu ngati Ahabu, amene anadzigulitsa kuchita zoyipa pamaso pa Yehova, amene anakopedwa ndi mkazi wake Yezebeli. 26 Iye anachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga mmene ankachitira Aamori amene Yehova anawachotsa pamene Aisraeli ankafika).

27 Ahabu atamva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake, navala ziguduli ndi kusala chakudya. Anagona pa ziguduli, nayenda pangʼonopangʼono.

28 Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, 29 “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Chifukwa wadzichepetsa, sindidzabweretsa mavuto amenewa pa nthawi ya moyo wake, koma ndidzawabweretsa pa nyumba yake pa nthawi ya mwana wake.”

1 Atesalonika 4

Moyo Wokondweretsa Mulungu

Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu.

Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera.

Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. 10 Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale.

11 Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. 12 Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Kubweranso kwa Ambuye

13 Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. 14 Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. 15 Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. 16 Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. 17 Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. 18 Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa.

Danieli 3

Fano la Golide ndi Ngʼanjo ya Moto

Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija. Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati:

“Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.”

Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika.

Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda. Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 10 Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, 11 ndi kuti aliyense osalambira ndi kupembedza adzaponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.”

13 Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, 14 ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? 15 Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”

16 Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. 17 Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. 18 Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.”

19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, 20 ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. 21 Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 22 Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, 23 ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.

24 Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?”

Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.”

25 Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.”

26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!”

Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, 27 ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto.

28 Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo. 29 Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.”

30 Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni.

Masalimo 107

BUKU LACHISANU

Masalimo 107–150

107 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
    amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
    kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.

Ena anayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu,
    osapeza njira yopitira ku mzinda kumene akanakakhazikikako.
Iwo anamva njala ndi ludzu,
    ndipo miyoyo yawo inafowokeratu.
Pamenepo analirira Yehova mʼmavuto awo
    ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
Iye anawatsogolera mʼnjira yowongoka
    kupita ku mzinda umene anakakhazikikako.
Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
    ndi chifukwa cha machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
pakuti Iye wapha ludzu la munthu womva ludzu
    ndipo wakhutitsa wanjala ndi zinthu zabwino.

10 Ena anakhala mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu,
    amʼndende ovutika mʼmaunyolo achitsulo,
11 pakuti iwowo anawukira mawu a Mulungu
    ndi kunyoza uphungu wa Wammwambamwamba.
12 Kotero Iye anawapereka kuti agwire ntchito yakalavulagaga;
    anagwa pansi ndipo panalibe woti awathandize.
13 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
    ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awo.
14 Yehova anawatulutsa mu mdima ndi mʼchisoni chachikulu
    ndipo anadula maunyolo awo.
15 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
    ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu onse,
16 pakuti Iye amathyola zipata zamkuwa
    ndi kudula pakati mipiringidzo yachitsulo.

17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,
    ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse
    ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
    ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;
    anawalanditsa ku manda.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
    ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
22 Apereke nsembe yachiyamiko
    ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.

23 Ena anayenda pa nyanja mʼsitima zapamadzi;
    Iwo anali anthu amalonda pa nyanja yayikulu.
24 Anaona ntchito za Yehova,
    machitidwe ake odabwitsa mʼnyanja yakuya.
25 Pakuti Iye anayankhula ndi kuwutsa mphepo yamkuntho
    imene inabweretsa mafunde ataliatali.
26 Sitima za pamadzizo zinatukulidwa mmwamba ndi kutsikira pansi pakuya;
    pamene amawonongeka, kulimba mtima kwawo kunasungunuka.
27 Anachita chizungulire ndi kudzandira ngati anthu oledzera;
    anali pa mapeto a moyo wawo.
28 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
    ndipo Iyeyo anawapulumutsa ku masautso awo.
29 Yehova analetsa namondwe,
    mafunde a mʼnyanja anatontholetsedwa.
30 Anali osangalala pamene kunakhala bata,
    ndipo Iye anawatsogolera ku dooko limene amalifuna.
31 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
    ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
32 Akuze Iye mu msonkhano wa anthu
    ndi kumutamanda pabwalo la akuluakulu.

33 Iye anasandutsa mitsinje kukhala chipululu,
    akasupe otuluka madzi kukhala nthaka yowuma,
34 ndiponso nthaka yachonde kukhala nthaka yamchere,
    chifukwa cha kuyipa kwa amene amakhala kumeneko.
35 Anasandutsa chipululu kukhala mayiwe a madzi
    ndi nthaka yowuma kukhala akasupe a madzi oyenda;
36 kumeneko Iye anabweretsa anthu anjala kuti azikhalako,
    ndipo iwo anamanga mzinda woti akhazikikeko.
37 Anafesa mbewu mʼminda ndi kudzala mipesa
    ndipo anakolola zipatso zochuluka;
38 Yehova anawadalitsa, ndipo chiwerengero chawo chinachuluka kwambiri,
    ndipo Iye sanalole kuti ziweto zawo zithe.

39 Kenaka chiwerengero chawo chinachepa ndipo iwo anatsitsidwa
    chifukwa cha mazunzo, mavuto ndi chisoni;
40 Iye amene amakhuthulira mʼnyozo pa olemekezeka
    anawachititsa kuyendayenda mʼmalo owumawo wopanda njira.
41 Koma Iyeyo anakweza anthu osowa kuchoka ku masautso awo
    ngati magulu a nkhosa.
42 Anthu olungama mtima amaona ndi kusangalala,
    koma anthu onse oyipa amatseka pakamwa pawo.

43 Aliyense wanzeru asamalitse zinthu zimenezi
    ndi kuganizira za chikondi chachikulu cha Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.