M’Cheyne Bible Reading Plan
7 Ndipo Elisa anati, “Mverani mawu a Yehova. Yehova akuti, ‘Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.’ ”
2 Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?”
Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
Akhate Anayi Awulula za Kuthawa kwa Aaramu
3 Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa? 4 Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.”
5 Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe, 6 pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!” 7 Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo.
8 Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso.
9 Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”
10 Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.” 11 Alonda a pa chipata aja analengeza uthengawu kwa okhala mʼnyumba yaufumu.
12 Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’ ”
13 Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.”
14 Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.” 15 Anthuwa anawalondola mpaka ku Yorodani, ndipo taonani, mʼnjira monse munali zovala zokhazokha ndi zinthu zimene Aaramu ankazitaya pamene ankathawa mofulumira. Ndipo amithengawo anabwerera ndi kudzafotokozera mfumu. 16 Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova.
17 Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake. 18 Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.”
19 Mtsogoleriyu ananena kwa munthu wa Mulungu kuti, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Munthu wa Mulungu anamuyankha kuti, “Iwe udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.” 20 Ndipo izi ndi zomwe zinamuchitikiradi mtsogoleriyu, pakuti anthu anamupondaponda pa chipata ndipo anafa.
Malangizo kwa Timoteyo
4 Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. 2 Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. 3 Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. 4 Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, 5 pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.
6 Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. 7 Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. 8 Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.
9 Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. 10 Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.
11 Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. 13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja.
15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.
11 1 Ndipo chaka choyamba cha Dariyo Mmedi ine Mikayeli ndinabwera kumuthandiza ndi kumuteteza Gabrieli.
Mafumu a Kummwera ndi Kumpoto
2 “Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi. 3 Kenaka mfumu yamphamvu idzafika imene idzalamulira ndi ufumu waukulu ndi kuchita zimene ifuna. 4 Koma ufumu wake ukadzafika pachimake, udzawonongedwa ndi kugawidwa mʼzigawo zinayi. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa zidzukulu zake, ndipo olowa mʼmalo mwake sadzakhala ndi mphamvu monga anali nazo, chifukwa ufumu wake udzazulidwa ndi kuperekedwa kwa ena.
5 “Mfumu ya kummwera idzakhala yamphamvu, koma mmodzi mwa akalonga ake adzakhala ndi mphamvu kuposa iyo; adzalamulira ufumu wake waukulu kwambiri. 6 Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani.
7 “Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana. 8 Iye adzalandanso milungu yawo, mafano awo achitsulo, ndi ziwiya zawo zamtengowapatali zasiliva ndi golide ndi kubwerera nazo ku Igupto. Adzaleka osayithira nkhondo mfumu ya kumpoto kwa zaka zingapo. 9 Kenaka mfumu ya kumpoto idzathira nkhondo dziko la mfumu ya kummwera koma idzalephera ndi kubwerera kwawo. 10 Ana ake adzakonzekera nkhondo ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, limene lidzathira nkhondo mfumu yakummwera ngati chigumula mpaka kumalo ake otetezedwa.
11 “Kenaka mfumu yakummwera idzatuluka mokwiya ndi kumenya nkhondo ndi mfumu yakumpoto, imene idzasonkhanitsa gulu lalikulu la nkhondo, koma idzayigonjetsa. 12 Gulu la nkhondoli likadzagwidwa, mfumu yakummwera idzayamba kudzikuza ndipo idzapha anthu miyandamiyanda, koma kupambanaku sikudzapitirira. 13 Popeza mfumu ya kumpoto idzasonkhanitsa gulu lina lankhondo, lochulukirapo kuposa loyamba; ndipo patapita zaka zingapo idzabwera ndi chigulu chachikulu cha nkhondo chokonzekeratu ndi zida.
14 “Nthawi imeneyo ambiri adzawukira mfumu ya kummwera. Anthu achisokonezo pakati panu nawonso adzawukira pokwaniritsa masomphenya, koma sadzapambana. 15 Kenaka mfumu ya kumpoto idzafika ndikuzinga mzinda powunda nthumbira za nkhondo ndipo idzagonjetsa mzinda wotetezedwa. Gulu lankhondo la kummwera lidzasowa mphamvu; ngakhale akatswiri awo ankhondo sadzakhala ndi mphamvu zogonjetsera ankhondo a kumpoto. 16 Mfumu ya kumpoto idzachita zofuna zake; palibe aliyense adzayigonjetse. Idzakhazikitsa ulamuliro wake mu Dziko Lokongola. Zonse zidzakhala mu ulamuliro wa mfumu yakumpoto ija. 17 Idzafika ndi mphamvu za ufumu wake wonse ndipo idzayesa kuchita pangano la mtendere ndi mfumu ya kummwera. Ndipo idzamupatsa mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndi cholinga cholanda ufumu, koma zolinga zake sizidzatheka kapena kumuthandiza. 18 Kenaka idzatembenukira ku mayiko a mʼmbali mwa nyanja ndi kulanda mizinda yambiri, koma mtsogoleri wina wa nkhondo adzathetsa kudzikuza kwakeko ndipo adzabwezera chipongwecho kwa iye. 19 Zikadzatha izi, mfumu idzabwerera ku malo otetezedwa a dziko la kwawo koma idzapunthwa ndi kugwa osapezekanso.
20 “Mfumu imene idzatenga malo ake idzatumiza wokhometsa msonkho kuti chuma cha ufumu wake chichuluke. Komabe mʼzaka zochepa mfumuyo idzawonongedwa osati mu mkwiyo kapena ku nkhondo.
21 “Mʼmalo mwake mudzalowa munthu wonyozeka amene si wa banja laufumu. Iye adzabwera pamene anthu akuganiza kuti ali pa mtendere, ndipo adzalanda ufumuwo mwa chinyengo. 22 Kenaka adzagonetsa gulu lalikulu lankhondo kuphatikizapo Mkulu wa Ansembe wapangano. 23 Atatha kuchita naye pangano, iye adzachita monyenga, ndipo ngakhale adzakhale ndi anthu ochepa adzakhalabe ndi mphamvu. 24 Mwadzidzidzi, iye adzazithira nkhondo zigawo zolemera kwambiri ndipo adzachita zimene makolo ake ngakhale agogo ake sanachitepo. Iye adzagawira zolanda, zofunkha ndi chuma kwa omutsatira. Adzachita chiwembu cholanda mizinda yotetezedwa koma kwa kanthawi kochepa.
25 “Mfumu ya kumpoto idzalimba mtima, ndipo idzasonkhanitsa gulu lalikulu la ankhondo kuti lithire nkhondo mfumu yakummwera. Mfumu yakummwera ndi gulu lake lankhondo lalikulu ndi lamphamvu idzathirana nkhondo ndi mfumu yakumpoto koma sidzapambana chifukwa cha ziwembu zimene adzamukonzera. 26 Amene amadya chakudya ndi mfumu adzamuukira; gulu lake lankhondo lidzagonjetsedwa, ndipo ambiri adzafera ku nkhondo. 27 Mafumu awiriwa mitima yawo idzalinga ku zoyipa. Azidzanamizana ali pa tebulo limodzi, koma zolinga zawo sizidzatheka chifukwa nthawi idzakhala isanakwane. 28 Mfumu ya kumpoto idzabwerera ku dziko la kwawo ndi chuma chambiri, koma mtima wake udzafunitsitsa pangano lopatulika. Idzawononga panganolo ndipo kenaka idzabwerera ku dziko lake.
29 “Patapita nthawi mfumu ya kumpoto idzabwereranso kummwera koma sidzapambana monga inachitira kale. 30 Sitima zapamadzi zochokera ku mayiko a ku madzulo zidzalimbana naye, ndipo adzataya mtima. Kenaka idzabwerera mopsa mtima ndi kudzalimbana ndi chipembedzo cha anthu opatulika. Idzabwerera ndi kuchitira chifundo amene sadzasunga pangano loyera.
31 “Ankhondo ake adzayipitsa linga la Nyumba ya Mulungu ndipo adzathetsa nsembe za tsiku ndi tsiku. Kenaka adzakhazikitsa chonyansa chimene chabweretsa chiwonongeko. 32 Ndi mawu oshashalika mfumuyo idzakopa amene anaphwanya pangano, koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzalimbika ndipo adzayikana mfumuyo kwathunthu.
33 “Amene ndi anzeru adzalangiza ambiri. Koma patapita kanthawi adzaphedwa ndi lupanga kapena kutenthedwa, kapena kugwidwa kapena kulandidwa katundu. 34 Pa nthawi yozunzikayi ena adzawathandiza pangʼono, koma ambiri othandizawo adzakhala achinyengo. 35 Ena mwa anzeruwo adzaphedwa ndi cholinga chakuti ayengedwe, otsala mwa iwo ayeretsedwe ndi kukhala wopanda banga kufikira nthawi yomaliza, popeza idzafika ndithu nthawi imene Mulungu wayika.
Mfumu Yodzikweza
36 “Mfumu ya kumpoto idzachita zimene ikufuna. Idzadzikweza ndi kudziyesa yopambana mulungu aliyense ndipo idzanenera za mwano Mulungu wa milungu. Iyo idzapambana mpaka nthawi yoti Mulungu ayilange mwa mkwiyo itakwana popeza chimene chatsimikizika chiyenera kuchitika. 37 Mfumuyo idzanyoza milungu ya makolo ake ndiponso mulungu wokondedwa ndi akazi, sidzachitiranso ulemu mulungu aliyense, koma idzadzikweza yokha pamwamba pa onse. 38 Mʼmalo mwa onsewo, idzachitira ulemu mulungu wachitetezo; mulungu wosadziwika ndi makolo ake. Iyo idzapereka kwa mulunguyo golide ndi siliva, ndi miyala yokongola, ndiponso mphatso za pamwamba kwambiri. 39 Anthu opembedza mulungu wachilendo adzakhala ngati linga lake. Idzalemekeza iwowa kwambiri, ndipo idzawayika kuti alamulire anthu ambiri. Idzawagawira dziko ngati malipiro awo.
40 “Pa nthawi yomaliza mfumu yakummwera idzachita nkhondo ndi mfumu yakumpoto. Koma mfumu yakumpotoyi idzayikantha ndi magaleta ndi akavalo ndi sitima zapamadzi zambiri ngati mphepo yamkokomo. Idzalowa mʼmayiko ambiri ndikuwakokolola onse ngati madzi osefukira. 41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola ndipo anthu ambiri adzaphedwa. Koma Edomu, Mowabu ndi olamulira a Amoni adzapulumuka. 42 Idzathira nkhondo mayiko ambiri ndipo ngakhale Igupto sadzapulumuka. 43 Idzalanda chuma cha golide, siliva, ndi zonse za mtengowapatali za ku Igupto, ndiponso anthu a ku Libiya ndi Akusi adzagonja kwa iwo. 44 Koma uthenga wochokera kummawa ndi kumpoto udzayiopsa, ndipo idzapita ndi ukali kukawononga ndi kutheratu anthu ambiri. 45 Mfumuyo idzayimika matenti ake aufumu, pakati pa nyanja ndi phiri lokongola. Komabe mapeto ake mfumuyo idzaphedwa, ndipo palibe amene adzayithandize.”
Daleti
25 Moyo wanga wakangamira fumbi;
tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.
26 Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha;
phunzitseni malamulo anu.
27 Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu;
pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.
28 Moyo wanga wafowoka ndi chisoni;
limbikitseni monga mwa mawu anu.
29 Mundichotse mʼnjira zachinyengo;
mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
30 Ndasankha njira ya choonadi;
ndayika malamulo anu pa mtima panga.
31 Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
32 Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu,
pakuti Inu mwamasula mtima wanga.
He
33 Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu;
ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
34 Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu
ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
35 Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu,
pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
36 Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu,
osati chuma.
37 Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe;
sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
38 Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu,
kuti Inu muopedwe.
39 Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa,
pakuti malamulo anu ndi abwino.
40 Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu!
Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.
Wawi
41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,
chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,
popeza ndimadalira mawu anu.
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,
pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,
ku nthawi za nthawi.
45 Ndidzayendayenda mwaufulu,
chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu
ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu
chifukwa ndimawakonda.
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,
ndipo ndimalingalira malangizo anu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.