M’Cheyne Bible Reading Plan
Mikaya Anenera Motsutsa Ahabu
22 Kwa zaka zitatu panalibe nkhondo pakati pa Aramu ndi Israeli. 2 Koma pa chaka chachitatu, Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita kukacheza ndi mfumu ya ku Israeli. 3 Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?”
4 Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?”
Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.” 5 Koma Yehosafati anawuzanso mfumu ya ku Israeli kuti, “Poyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
6 Choncho mfumu ya Israeli inasonkhanitsa pamodzi aneneri okwanira 400, ndipo inawafunsa kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena ndileke?”
Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Ambuye waupereka mzindawo mʼmanja mwa mfumu.”
7 Koma Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi kuno kulibenso mneneri wina wa Yehova kumene ife tingakafunsireko nzeru?”
8 Mfumu ya ku Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife tingakafunsire kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa iyeyo samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa nthawi zonse. Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.”
Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu musatero.”
9 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa atumiki ake ndipo inati, “Kayitane Mikaya mwana wa Imula msangamsanga.”
10 Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo. 11 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ”
12 Aneneri ena onse ananenera zomwezonso. Iwo anati, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
13 Wamthenga amene anapita kukayitana Mikaya anamuwuza kuti, “Taonani, aneneri onse monga munthu mmodzi akunenera za kupambana kwa mfumu. Mawu anunso akhale ogwirizana ndi mawu awo, ndipo mukayankhule zabwino.”
14 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndikawawuza zokhazo zimene Yehova akandiwuze.”
15 Atafika, Ahabu anamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena tileke?”
Iye anayankha kuti, “Pitani ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
16 Ahabu anati kwa iye, “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti undiwuze zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?”
17 Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’ ”
18 Mfumu ya ku Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti ameneyu samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa zokhazokha?”
19 Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere. 20 Ndipo Yehova anati, ‘Kodi ndani amene akamukope Ahabu kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi, nʼkukafera komweko?’ ”
“Wina anapereka maganizo ena ndipo winanso maganizo ena. 21 Potsirizira, mzimu wina unabwera ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, ‘Ine ndidzamukopa.’ ”
22 Yehova anafunsa kuti, “Ukamukopa bwanji?”
Mzimuwo unati, “Ndidzapita ndi kukakhala mzimu wabodza pakamwa pa aneneri ake onse.”
Yehova anati, “ ‘Iwe udzamukopadi. Pita kachite zomwezo.’
23 “Ndipo tsopano taonani, Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa. Yehova waneneratu kuti mukaona mavuto.”
24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi namenya Mikaya patsaya. Iye anafunsa Mikaya kuti, “Kodi mzimu wa Yehova unadzera njira iti pamene umatuluka mwa ine kuti uziyankhula ndi iwe?”
25 Mikaya anayankha kuti, “Udzaona pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
26 Pamenepo mfumu ya ku Israeli inalamula kuti, “Mugwireni Mikaya ndipo mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu 27 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyikeni mʼndende munthu uyu ndipo musamupatse chakudya china koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwerera mwamtendere.’ ”
28 Mikaya ananena kuti, “Ngati mudzabwerera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo iye anapitiriza kunena kuti, “Gwiritsitsani mawu angawa, anthu inu nonse!”
Ahabu Aphedwa ku Ramoti Giliyadi
29 Choncho mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. 30 Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo.
31 Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.” 32 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula, 33 olamulira akavalo anaona kuti sanali mfumu ya ku Israeli ndipo analeka kumuthamangitsa.
34 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.” 35 Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira. 36 Pamene dzuwa linkalowa, kunamveka mfuwu wa nkhondo kuti, “Munthu aliyense apite ku mzinda wa kwawo, aliyense apite ku dziko la kwawo!”
37 Ndipo mfumu ija inafa, nabwera nayo ku Samariya, ndipo anayika mʼmanda kumeneko. 38 Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera.
39 Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli? 40 Ahabu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehosafati Mfumu ya ku Yuda
41 Yehosafati, mwana wa Asa anakhala mfumu ya ku Yuda chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya ku Israeli. 42 Yehosafati anali wa zaka 35 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Amayi ake anali Azuba mwana wa Silihi. 43 Pa zinthu zonse, Yehosafati anayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanachite zotsutsana ndi machitidwe a abambo ake. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova. Komabe, malo azipembedzo sanawawononge, ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko. 44 Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya ku Israeli.
45 Ntchito zake zina za Yehosafati, zinthu zimene anachita ndi zamphamvu zimene anaonetsa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Yuda? 46 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake. 47 Nthawi imeneyo kunalibe mfumu ku Edomu, amene ankalamulira anali munthu woyikidwa ndi mfumu ya ku Yuda.
48 Yehosafati anapanga sitima zapamadzi zopita ku Ofiri kukatenga golide, koma sitimazo sizinayende chifukwa zinawonongeka ku Ezioni Geberi. 49 Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana.
50 Ndipo Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahaziya Mfumu ya ku Israeli
51 Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 52 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli. 53 Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.
Tsiku la Ambuye
5 Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, 2 chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. 3 Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa.
4 Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. 5 Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. 6 Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. 7 Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. 8 Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. 9 Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. 10 Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. 11 Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira.
Malangizo Otsiriza
12 Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. 13 Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. 14 Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. 15 Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse.
16 Kondwerani nthawi zonse. 17 Pempherani kosalekeza. 18 Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu.
19 Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. 20 Musanyoze mawu a uneneri. 21 Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. 22 Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse.
23 Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. 24 Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi.
25 Abale, mutipempherere. 26 Perekani moni wachikondi kwa onse. 27 Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.
28 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.
Maloto Achiwiri a Nebukadinezara
4 Mfumu Nebukadinezara anatumiza mawu awa kwa anthu a mitundu yonse, ndi chiyankhulo chilichonse, amene amakhala pa dziko lonse lapansi:
Mtendere uchuluke pakati panu!
2 Chandikomera kukuwuzani zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wammwambamwamba wandichitira.
3 Zizindikiro zake ndi zazikulu,
zozizwitsa zake ndi zamphamvu!
Ufumu wake ndi wamuyaya;
ulamuliro wake ndi wa mibadomibado.
4 Ine Nebukadinezara, ndinali kwathu mʼnyumba yanga yaufumu, mwa mtendere ndipo ndinali wokhutitsidwa. 5 Ndili chigonere pa bedi langa, ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Zinthu ndi masomphenya zimene ndinaziona zinandiopsa. 6 Choncho ndinalamula kuti anthu onse a nzeru a ku Babuloni abwere pa maso panga kunditanthauzira malotowo. 7 Pamene amatsenga, owombeza, alawuli ndi amawula anabwera, ndinawafotokozera maloto, koma sanathe kunditanthauzira. 8 Potsiriza, anabwera Danieli uja amatchedwa Belitesezara, potsata dzina la mulungu wanga, ndipo mzimu wa milungu yoyera uli mwa iye. Iyeyu ndinamufotokozera malotowo.
9 Ndinati, “Belitesezara, mkulu wa amatsenga, ndikudziwa kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe, ndipo palibe chinsinsi chomwe sungachidziwe. Awa ndi maloto anga; unditanthauzire. 10 Awa ndi masomphenya amene ine ndinaona pamene ndinali kugona pa bedi: Ndinaona, mtengo wautali kwambiri utayima pakati pa dziko lapansi. 11 Mtengowo unakula ndi kulimba ndipo msonga yake inafika mpaka mlengalenga; umaonekera pa dziko lonse lapansi. 12 Masamba ake anali okongola, zipatso zinali zochuluka, ndipo mu mtengomo munali chakudya chokwanira anthu onse. Zirombo zakuthengo zimapeza mthunzi mʼmunsi mwake, ndipo mbalame zamlengalenga zimakhala pa nthambi zake: Cholengedwa chilichonse chinkadya za mu mtengowu.
13 “Ndikanali chigonere ndinaona mʼmasomphenya mngelo atayima pamaso panga, woyera, atatsika kuchokera kumwamba. 14 Anayankhula mofuwula kuti, ‘Gwetsa mtengo ndi kusadza nthambi zake; yoyola masamba ake kuti nyama zakuthengo zithawe pa mthunzi pake ndi mbalame zithawe pa nthambi zake. 15 Koma musiye tsinde ndi mizu yake mʼnthaka. Tsindelo mulimange maunyolo a chitsulo ndi mkuwa, zikhalebe mʼnthaka, nʼkudya udzu mʼmunda.
“ ‘Mumulole iye anyowe ndi mame akumwamba, ndipo iye akhale ndi nyama pakati pa zomera za mʼnthaka. 16 Maganizo ake a umunthu asinthidwe ndipo apatsidwe maganizo a nyama ya kuthengo, mpaka zaka zisanu ndi ziwiri zitadutsa.
17 “ ‘Angelo oyera ndiwo akutsimikiza chilangochi. Tsono anthu adziwe kuti Mulungu Wammwambamwamba ali ndi mphamvu yolamulira maufumu onse, ndipo amawapereka kwa aliyense akumufuna, ngakhale munthu wamba kuti alamulire.’
18 “Amenewa ndi maloto amene ine, mfumu Nebukadinezara, ndinalota. Tsopano Belitesezara, undifotokozere tanthauzo lake, popeza palibe mwa anthu anzeru a mu ufumu wanga amene angathe kunditanthauzira. Koma iwe ukhoza, chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.”
Danieli Atanthauzira Maloto
19 Pamenepo Danieli, amene amatchedwa Belitesezara, anavutika mu mtima kwambiri kwa kanthawi, ndipo anasautsidwa mʼmaganizo ake. Choncho mfumu inati, “Belitesezara usalole malotowa kapena tanthauzo lake likuopse.”
Belitesezara anayankha kuti, “Mbuye wanga, ndikanakonda malotowa akanakhudza adani anu okha, ndi tanthauzo lake kwa iwo okusautsani! 20 Mtengo munawuona uja, umene unkakulirakulira kwambiri ndi kulimba, ndi msonga yake inafika mlengalenga, ndi kuonekera ku dziko lonse lapansi, 21 mtengo umene masamba ake anali okongola ndiponso unali ndi zipatso zochuluka zokwanira kudya anthu onse a dziko lapansi. Mtengowu unkapereka mthunzi ku zirombo zonse zakuthengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinayika zisa pa nthambi zake. 22 Inu mfumu, ndinu mtengo umenewo! Inu mwakhala wamkulu ndi wamphamvu; ukulu wanu wakula mpaka wakhudza mlengalenga, ndipo ufumu wanu wafika mpaka ku malo akutali a dziko lapansi.
23 “Inu mfumu munaona mthenga woyera, akuchokera kumwamba ndipo anati, ‘Gwetsani mtengo ndipo muwuwononge, koma musiye tsinde ndi mizu yake. Tsindelo mulimange ndi unyolo wa chitsulo ndi mkuwa ndipo mulisiye pakati pa udzu wa mʼmunda. Mulole kuti linyowe ndi mame akumwamba. Likhale ngati nyama zakuthengo, mpaka zaka zidutse zisanu ndi ziwiri.’
24 “Tanthauzo lake ndi ili mfumu, izi ndi zimene Mulungu Wammwambamwamba watsimikiza kuti zikugwereni mbuye wanga mfumu: 25 Inu mudzachotsedwa pakati pa anthu ndipo mudzakhala ndi nyama zakuthengo; mudzadya udzu monga ngʼombe ndi kunyowa ndi mame akumwamba. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka mudzavomereze kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa ma ufumu a anthu, ndipo amawapereka kwa aliyense amene Iye wafuna. 26 Lamulo losiya tsinde la mtengo ndi mizu yake litanthauza kuti ufumu wanu udzabwezeredwa kwa inu mukadzavomereza kuti Mulungu ndiye amalamulira. 27 Nʼchifukwa chake mfumu, chikukomereni kulandira malangizo anga: Lekani machimo ndipo muzichita zabwino, lekani mphulupulu zanu ndipo muzikomera mtima anthu opsinjika. Nʼkutheka kuti mtendere wanu udzapitirira.”
Maloto Akwaniritsidwa
28 Zonsezi zinamuchitikira mfumu Nebukadinezara. 29 Itapita miyezi khumi ndi iwiri, pamene mfumu inkayenda pa denga la nyumba ya ufumu ya ku Babuloni, 30 iye anati, “Kodi Babuloni si mzinda wamphamvu ndi wokongola umene ndinamanga ndi mphamvu zanga ngati nyumba yanga yaufumu, kuonetsera ulemerero wa ufumu wanga?”
31 Akuyankhulabe izi mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Imvani izi, mfumu Nebukadinezara: Ufumu wako wachotsedwa. 32 Udzachotsedwa pakati pa anthu ndipo udzakhala ndi zirombo zakuthengo; udzadya udzu monga ngʼombe. Zaka zisanu ndi ziwiri zidzadutsa mpaka iwe utavomereza kuti Wammwambamwamba ndiye mwini ulamuliro pa maufumu a anthu ndipo amawupereka kwa aliyense amene iye afuna.”
33 Nthawi yomweyo zonse zimene zinanenedwa zokhudza Nebukadinezara zinakwaniritsidwa. Iye anachotsedwa pakati pa anthu ndipo ankadya udzu ngati ngʼombe. Thupi lake linanyowa ndi mame akumwamba mpaka tsitsi lake linakula ngati nthenga za chiwombankhanga ndi zikhadabo ngati zikhadabo za mbalame.
34 Pomaliza pa zaka zimenezo ine, Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndipo nzeru zanga zinabwereramo. Kenaka ndinatamanda Wammwambamwamba; ndinamupatsa ulemu ndi kumulemekeza Iye amene akhala nthawi zonse.
Ulamuliro wake ndi ulamuliro wa nthawi zonse;
ufumu wake udzakhala ku mibadomibado.
35 Anthu onse a dziko lapansi
ali chabe pamaso pake.
Pakati pa angelo akumwamba
ndi anthu a dziko lapansi
palibe amene akhoza kumuletsa
Mulungu kuchita zimene afuna.
Kapena kunena kwa Iye kuti, “Kodi mwachita chiyani?”
36 Pa nthawi yomweyo nzeru zanga zinabwereramo. Ndinalandiranso ulemu wanga ndi ufumu wanga. Nduna ndi akalonga anga anandilandiranso. Ndipo anandibwezera ufumu wanga ndi kukhalanso wamphamvu kuposa kale. 37 Tsopano ine Nebukadinezara, ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba chifukwa zonse zimene amachita ndi zoyenera ndipo njira zake zonse ndi zachilungamo. Ndipo onse amene amayenda modzikuza adzawatsitsa.
Nyimbo. Salimo la Davide.
108 Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu;
ndidzayimba nyimbo, inde ndidzayimba nyimbo zotamanda ndi moyo wanga wonse.
2 Dzukani, zeze ndi pangwe!
Ine ndidzadzutsa mʼbandakucha.
3 Ndidzakutamandani Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;
ndidzayimba za Inu pakati pa anthu a mitundu ina.
4 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kutalika kwake kuposa kumwamba;
kukhulupirika kwanu kumafika mlengalenga.
5 Kwezekani Inu Mulungu, kuposa mayiko akumwamba,
ndipo ulemerero wanu uphimbe dziko lonse lapansi.
6 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja
kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
7 Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
“Mwachipambano Ine ndidzagawa Sekemu
ndipo ndidzayesa chigwa cha Sukoti.
8 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
Yuda ndi ndodo yanga yaufumu.
9 Mowabu ndi mbale yanga yosambiramo
ndidzaponya nsapato zanga pa Edomu;
ndidzafuwula mopambana pa Filisitiya.”
10 Ndani adzandifikitsa ku mzinda wotetezedwa?
Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
11 Kodi sindinu Mulungu, Inu amene mwatikana
ndipo simuperekezanso magulu athu ankhondo?
12 Tithandizeni ife kulimbana ndi mdani,
pakuti thandizo la munthu ndi lopanda pake.
13 Chifukwa cha Mulungu wathu, ife tidzapeza chipambano,
ndipo adzapondereza pansi adani athu.
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Salimo la Davide.
109 Mulungu amene ndimakutamandani,
musakhale chete,
2 pakuti anthu oyipa ndi achinyengo
atsekula pakamwa pawo kutsutsana nane;
iwo ayankhula motsutsana nane ndi malilime abodza.
3 Andizungulira ndi mawu audani,
amandinena popanda chifukwa.
4 Mʼmalo mwa chikondi changa amandineneza,
koma ine ndine munthu wapemphero.
5 Iwo amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino,
ndi udani mʼmalo mwa chikondi changa.
6 Sankhani munthu woyipa kuti amutsutse iye;
lolani wotsutsa ayime ku dzanja lake lamanja.
7 Pamene aweruzidwa, apezeke kuti ndi wolakwa,
ndipo mapemphero ake amutsutse.
8 Masiku ake akhale owerengeka;
munthu wina atenge malo ake a utsogoleri.
9 Ana ake akhale amasiye
ndipo mkazi wake akhale wopanda mwamuna.
10 Ana ake akhale oyendayenda ndi opemphapempha;
apirikitsidwe kuchoka pa mabwinja a nyumba zawo.
11 Wokongoza alande zonse zimene ali nazo;
alendo afunkhe ntchito za manja ake.
12 Pasapezeke ndi mmodzi yemwe womukomera mtima
kapena kumvera chisoni ana ake amasiye.
13 Zidzukulu zake zithe nʼkufa,
mayina awo afafanizidwe mu mʼbado wotsatirawo.
14 Mphulupulu za makolo ake zikumbukiridwe pamaso pa Yehova;
tchimo la amayi ake lisadzafafanizidwe.
15 Machimo awo akhale pamaso pa Yehova nthawi zonse,
kuti Iye achotse chikumbutso chawo pa dziko lapansi.
16 Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo,
koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka
ndi osweka mtima.
17 Anakonda kutemberera,
matembererowo abwerere kwa iye;
sanakondwe nʼkudalitsa anthu ena,
choncho madalitso akhale kutali naye.
18 Anavala kutemberera ngati chovala;
kutemberera kunalowa mʼthupi lake ngati madzi,
kulowa mʼmafupa ake ngati mafuta.
19 Matemberero akhale ngati chofunda chodzikutira nacho,
ngati lamba wovala tsiku ndi tsiku.
20 Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga,
kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.
21 Koma Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
muchite nane molingana ndi dzina lanu,
chifukwa cha ubwino wa chikondi chanu, pulumutseni.
22 Pakuti ndine wosauka ndi wosowa,
ndipo mtima wanga ukuwawa mʼkati mwanga.
23 Ndikuzimirira ngati mthunzi wa kumadzulo,
ndapirikitsidwa ngati dzombe.
24 Mawondo anga afowoka chifukwa cha kusala zakudya,
thupi langa lawonda ndi mutu wanga womwe.
25 Ndine chinthu chotonzedwa kwa otsutsana nane;
akandiona, amapukusa mitu yawo.
26 Thandizeni Inu Yehova Mulungu wanga;
pulumutseni molingana ndi chikondi chanu.
27 Adaniwo adziwe kuti limeneli ndi dzanja lanu,
kuti Inu Yehova mwachita zimenezi.
28 Angathe kutemberera, koma Inu mudzadalitsa;
pamene iwo andiputa adzachititsidwa manyazi,
koma mtumiki wanu adzasangalala.
29 Onditsutsa adzavekedwa mnyozo,
ndipo adzadzifunditsa manyazi ngati chovala.
30 Ndi pakamwa panga ndidzathokoza Yehova kwambiri;
ndidzamutamanda mʼgulu lalikulu la anthu.
31 Popeza Iye amayima ku dzanja lamanja la munthu wosowayo,
kupulumutsa moyo wake kwa iwo amene agamula molakwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.