M’Cheyne Bible Reading Plan
Makwangwala Adyetsa Eliya
17 Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”
2 Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, 3 “Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani. 4 Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”
5 Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko. 6 Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo.
Mayi Wamasiye wa ku Zarefati
7 Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo. 8 Yehova anayankhula naye kuti, 9 “Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” 10 Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” 11 Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”
12 Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”
13 Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. 14 Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
15 Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. 16 Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.
17 Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. 18 Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”
19 Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. 20 Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” 21 Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”
22 Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. 23 Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”
24 Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”
4 Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.
Malangizo Ena
2 Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. 3 Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. 4 Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. 5 Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. 6 Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.
Mawu Otsiriza
7 Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. 8 Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. 9 Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.
10 Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). 11 Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. 12 Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. 13 Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. 14 Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. 15 Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.
16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.
17 Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”
18 Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.
Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu
47 Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. 2 Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.
3 Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. 4 Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. 5 Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. 6 Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”
Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. 7 Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. 8 Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. 9 Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. 10 Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. 11 Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. 12 Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”
Malire a Dziko
13 Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. 14 Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.
15 “Malire a dzikolo adzakhala motere:
Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, 16 Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. 17 Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.
18 Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.
19 Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.
20 Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.”
21 “Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. 22 Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. 23 Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
3 Amene amakhululuka machimo ako onse
ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
4 amene awombola moyo wako ku dzenje
ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
6 Yehova amachita chilungamo
ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
7 Iye anadziwitsa Mose njira zake,
ntchito zake kwa Aisraeli.
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,
amakumbukira kuti ndife fumbi.
15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,
amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso
ndipo malo ake sakumbukirikanso.
17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
18 iwo amene amasunga pangano lake
ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba
ndipo ufumu wake umalamulira onse.
20 Tamandani Yehova, inu angelo ake,
amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,
amene mumamvera mawu ake.
21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,
inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
kulikonse mu ulamuliro wake.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.