Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Mafumu 2

Eliya Atengedwa Kupita Kumwamba

Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala. Eliya anawuza Elisa kuti, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Beteli.”

Koma Elisa anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Beteli.

Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”

Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.”

Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.”

Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko.

Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”

Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.”

Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.”

Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.

Anthu makumi asanu mwa ana a aneneri anawatsatira nayima chapatali moyangʼanana nawo ndipo Eliya ndi Elisa anayima mʼmphepete mwa Yorodani. Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma.

Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”

Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.”

10 Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.”

11 Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. 12 Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.

13 Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani. 14 Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka.

15 Ndipo ana a aneneri ochokera ku Yeriko atamuona anati, “Mzimu wa Eliya wakhazikika pa Elisa.” Ndipo anapita kukakumana naye nagwada ndi kuweramitsa mitu yawo pansi pamaso pake. 16 Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.”

Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.”

17 Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze. 18 Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?”

Kuchiritsidwa kwa Madzi

19 Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.”

20 Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye.

21 Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ” 22 Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula.

Kusekedwa kwa Elisa

23 Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi” 24 Iye anatembenuka nawayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Nthawi yomweyo panatulukira zimbalangondo ziwiri kuchokera kuthengo, ndi kuphapo anyamata 42. 25 Ndipo iye anapita ku phiri la Karimeli. Pochoka kumeneko anabwerera ku Samariya.

2 Atesalonika 2

Kubwera kwa Munthu Woyipitsitsa

Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale. Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo. Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi? Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera. Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe. Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake. Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo. 10 Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe. 11 Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza. 12 Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa.

Imani Mwamphamvu

13 Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi. 14 Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. 15 Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata.

16 Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, 17 akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse.

Danieli 6

Danieli Mʼdzenje la Mikango

Kunamukomera Dariyo kusankha akalonga 120 kuti alamulire mu ufumu wonse, ndikusankha nduna zazikulu zitatu kuti ziwayangʼanire ndipo imodzi mwa ndunazo anali Danieli. Akalongawo amayangʼaniridwa ndi nduna zazikuluzo kuti zinthu za mfumu zisawonongeke. Tsono Danieli anadzionetsa kuti akhoza kugwira ntchito bwino kopambana nduna zinzake chifukwa anali wanzeru kwambiri. Ndiye mfumu inaganiza zomuyika kuti akhale woyangʼanira ufumu wonse. Chifukwa cha ichi, anzake ndi akalonga anayesa kupeza zifukwa zomutsutsira Danieli pa kayendetsedwe ka ntchito za dzikolo, koma sanapeze cholakwa chilichonse. Iwo sanapeze chinyengo mwa iye, chifukwa anali wokhulupirika ndipo sankachita chinyengo kapena kutayirira ntchito. Pomaliza, anthu awa ananena kuti, “Sitidzapeza cholakwa chilichonse chomutsutsira Danieli kupatula chokhacho chimene chikhudza chipembedzo cha Mulungu wake.”

Choncho akalonga ndi nduna pamodzi anapita kwa mfumu ndipo anati: “Inu mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo wautali! Nduna zoyendetsa ufumu wanu, aphungu, akalonga ndi abwanamkubwa tonse tagwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo ndi kulisindikiza kuti aliyense amene apemphera kwa mulungu wina kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, pa masiku makumi atatu otsatirawa, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango. Tsopano inu mfumu khazikitsani lamulo limeneli ndipo musindikizepo dzina lanu kuti lisasinthike monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sasinthidwa.” Choncho mfumu Dariyo anasindikizapo dzina lake pa lamuloli.

10 Danieli atamva kuti lamulo lasindikizidwa, anapita ku nyumba kwake nalowa mʼchipinda chapamwamba chimene mazenera ake anali otsekula kuloza ku Yerusalemu. Katatu pa tsiku iye ankagwada pansi pa mawondo ndipo amapemphera, kuyamika Mulungu wake, monga momwe ankachitira kale. 11 Ndipo anthu awa anapita pamodzi ndi kukapeza Danieli akupemphera ndi kupempha Mulungu wake kuti amuthandize. 12 Kotero iwo anapita kwa mfumu ndipo anayankhula naye za lamulo lake kuti, “Kodi simunasindikize lamulo lakuti pa masiku makumi atatu otsatirawa aliyense amene apemphera kwa mulungu wina aliyense kapena kwa munthu kupatula kwa inu mfumu, adzaponyedwa mʼdzenje la mikango?”

Mfumu inayankha kuti, “Lamulo lilipobe monga mwa malamulo a Amedi ndi Aperezi, amene sangathe kusinthika.”

13 Kenaka iwo anati kwa mfumu, “Danieli, amene ndi mmodzi mwa akapolo ochokera ku Yuda, sakulabadira inu mfumu, kapena lamulo limene munasindikizapo dzina lanu lija. Iye akupempherabe katatu pa tsiku.” 14 Mfumu itamva izi, inavutika kwambiri mu mtima mwake. Iyo inayesa kupeza njira yopulumutsira Danieli. Iyo inachita chotheka chilichonse kufikira kulowa kwa dzuwa kuti imupulumutse.

15 Ndipo anthuwo anapita pamodzi kwa mfumu ndipo anati kwa iye, “Kumbukirani, inu mfumu kuti monga mwa lamulo la Amedi ndi Aperezi, palibe chimene mfumu inalamulira kapena kukhazikitsa chimasinthidwa.”

16 Choncho mfumu inalamula, ndipo anabwera naye Danieli ndi kukamuponya mʼdzenje la mikango. Mfumu inati kwa Danieli, “Mulungu wako amene umutumikira nthawi zonse, akupulumutse!”

17 Anatenga mwala natseka pa khoma pa dzenje la mikango, ndipo mfumu inadindapo chizindikiro chake ndi cha nduna zake kuti wina asasinthepo kanthu pa za Danieli. 18 Kenaka mfumu inabwerera ku nyumba yake ndipo inakhala usiku wonse osadya kanthu, osalola chosangalatsa chilichonse. Ndipo sinagone tulo.

19 Mʼbandakucha, mfumu inanyamuka ndi kufulumira kupita ku dzenje la mikango lija. 20 Itayandikira pa dzenjelo, inayitana Danieli moonetsa nkhawa, “Danieli, mtumiki wa Mulungu wa moyo! Kodi Mulungu wako, amene umutumikira nthawi zonse, wakulanditsa ku mikango?”

21 Danieli anayankha kuti, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 22 Mulungu wanga anatumiza mngelo wake, ndipo anatseka pakamwa pa mikango. Iyo sinandivulaze chifukwa Mulungu anaona kuti ndine wosalakwa ndi kutinso sindinakulakwireni inu mfumu.”

23 Mfumu inali ndi chimwemwe chopambana ndipo inalamulira kuti amutulutse Danieli mʼdzenjemo. Ndipo atamutulutsa Danieli mʼdzenjemo, sanapezeke ndi chilonda chilichonse pa thupi lake, chifukwa iye anadalira Mulungu wake.

24 Mwa lamulo la mfumu, anthu onse amene ananeneza Danieli aja anagwidwa ndi kukaponyedwa mʼdzenje la mikango, pamodzi ndi akazi awo ndi ana awo. Ndipo asanafike pansi pa dzenjelo, mikango inawawakha ndi mphamvu ndi kuteketa mafupa awo onse.

25 Kenaka mfumu Dariyo inalembera anthu a mitundu yonse, ndi anthu a ziyankhulo zosiyanasiyana a mʼdziko lonse kuti,

“Mtendere uchuluke pakati panu!

26 “Ndikukhazikitsa lamulo kuti paliponse mʼdziko langa anthu ayenera kuopa ndi kuchitira ulemu Mulungu wa Danieli.

“Popeza Iye ndi Mulungu wamoyo
    ndi wamuyaya;
ufumu wake sudzawonongeka,
    ulamuliro wake sudzatha.
27 Iye amalanditsa ndipo amapulumutsa,
    amachita zizindikiro ndi zozizwitsa
    kumwamba ndi pa dziko lapansi.
Iye walanditsa Danieli
    ku mphamvu ya mikango.”

28 Choncho Danieli anapeza ufulu pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo ndi ulamuliro wa Koresi wa ku Perisiya.

Masalimo 112-113

112 Tamandani Yehova.

Wodala munthu amene amaopa Yehova,
    amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.

Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
    mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,
    ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;
    wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
    amene amachita ntchito yake mwachilungamo.

Ndithu sadzagwedezeka;
    munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;
    mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;
    potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
    chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;
    nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.

10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;
    adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.
    Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
113 Tamandani Yehova.

Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
    tamandani dzina la Yehova.
Yehova atamandidwe,
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake,
    dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.

Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse,
    ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.
Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,
    Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?
amene amawerama pansi kuyangʼana
    miyamba ndi dziko lapansi?

Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi
    ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
amawakhazika pamodzi ndi mafumu,
    pamodzi ndi mafumu a anthu ake.
Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake
    monga mayi wa ana wosangalala.

Tamandani Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.