Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 2

Davide Alangiza Solomoni

Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti:

“Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’

“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.

“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.

“Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ Koma tsopano usamuyese ngati munthu wosalakwa. Iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziwa choti uchite naye. Ngakhale ndi wokalamba, aphedwe ndithu.”

10 Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. 11 Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33. 12 Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.

Kukhazikika kwa Ufumu wa Solomoni

13 Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, anapita kwa Batiseba, amayi ake a Solomoni. Batiseba anamufunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere?”

Iye anayakha kuti, “Eya, ndi zamtendere.” 14 Ndipo iye anawonjezera kunena kuti, “Ndili ndi mawu oti ndiyankhule nanu.”

Batiseba anayankha kuti, “Yankhula.”

15 Tsono Adoniya anati, “Monga inu mukudziwa, ufumu unali wanga. Aisraeli onse ankayembekezera kuti ine ndidzakhala mfumu yawo. Koma zinthu zinasintha ndipo ufumu wapita kwa mʼbale wanga; pakuti wapatsa iye ufumuwu ndi Yehova. 16 Tsono ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanize ayi.”

Batiseba anati, “Nena.”

17 Adoniya anapitiriza kunena kuti, “Chonde, inu mupemphe mfumu Solomoni kuti andipatse Abisagi wa ku Sunemu kuti akhale mkazi wanga pakuti mukapempha inu sadzakukanizani.”

18 Batiseba anayankha kuti, “Chabwino. Ndidzakuyankhulira kwa mfumu.”

19 Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.

20 Amayi akewo anati, “Ndikufuna ndikupempheni kanthu kakangʼono. Chonde musandikanize.”

Mfumu inayankha kuti, “Pemphani amayi, ine sindikukanizani.”

21 Ndipo amayiwo anati, “Mulole kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa mʼbale wanu Adoniya.”

22 Koma Mfumu Solomoni inayankha amayi ake aja kuti, “Chifukwa chiyani mukupemphera Adoniya Abisagi wa ku Sunemu? Mungathenso kumupemphera ufumu pakuti iyeyu ndi mkulu wanga ndipo mupemphereninso wansembe Abiatara ndi Yowabu mwana wa Zeruya!”

23 Pamenepo Mfumu Solomoni inalumbira mʼdzina la Yehova kuti, “Mulungu andilange ine koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha pempho lakeli! 24 Tsono pali Yehova wamoyo, amene anandikhazikitsa ine pa mpando waufumu wa abambo anga Davide ndi kundipatsa ufumu monga analonjezera, Adoniya aphedwa lero lomwe lino!” 25 Choncho Mfumu Solomoni inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo anakantha Adoniyayo, nafa.

26 Ndipo mfumu inati kwa Abiatara wansembe, “Pita ku Anatoti ku minda yako chifukwa ndiwe woyenera kufa, koma sindikupha tsopano, chifukwa unkanyamula Bokosi la Chipangano la Ambuye Yehova pamaso pa abambo anga Davide ndipo unazunzika limodzi ndi abambo angawo.” 27 Kotero Solomoni anachotsa Abiatara pa udindo wokhala wansembe wa Yehova, kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula za nyumba ya Eli ku Silo.

28 Yowabu atamva zimenezi anathawira ku tenti ya Yehova ndipo anakagwira msonga za guwa lansembe, popeza Yowabu ndiye anathandiza Adoniya kuwukira koma sanathandize Abisalomu. 29 Mfumu Solomoni inawuzidwa kuti Yowabu wathawira ku tenti ya Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe. Tsono Solomoni analamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti, “Pita, kamukanthe!”

30 Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ”

Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.”

Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”

31 Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha. 32 Yehova adzamubwezera zomwe anachita pokhetsa magazi, chifukwa iye anakantha ndi lupanga anthu awiri abwino ndi olungama kuposa iye, nawapha, abambo anga Davide osadziwa. Anthu awiriwo ndi Abineri mwana wa Neri, wolamulira gulu lankhondo la Israeli ndi Amasa mwana wa Yeteri, wolamulira gulu lankhondo la Yuda. 33 Magazi amene Yowabu anakhetsa akhale pamutu pake ndi pa zidzukulu zake kwamuyaya. Koma pa Davide ndi zidzukulu zake, nyumba yake ndi mpando wake waufumu pakhale mtendere wochokera kwa Yehova kwamuyaya.”

34 Choncho Benaya mwana wa Yehoyada anapita kukakantha Yowabu nʼkumupha ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yakeyake ya ku chipululu. 35 Mfumu inayika Benaya mwana wa Yehoyada kuti akhale woyangʼanira gulu lankhondo mʼmalo mwa Yowabu ndipo inayika Zadoki kuti akhale wansembe mʼmalo mwa Abiatara.

36 Kenaka mfumu inatuma anthu kukayitana Simei ndipo inamuwuza kuti, “Udzimangire nyumba mu Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko, koma usatuluke mu mzinda kupita kwina kulikonse. 37 Tsiku lomwe udzatulukemo ndi kuwoloka Chigwa cha Kidroni, udziwiretu kuti udzafa ndipo magazi ako adzakhala pamutu pako.”

38 Simei anayankha mfumu kuti, “Zimene mwanenazi nʼzabwino. Kapolo wanu adzachita monga mbuye wanga mfumu mwanenera.” Choncho Simei anakhala mu Yerusalemu nthawi yayitali.

39 Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati, ndipo Simei anawuzidwa kuti, “Akapolo anu ali ku Gati.” 40 Atamva zimenezi, anakwera bulu wake ndipo anapita kwa Akisi ku Gati kukafunafuna akapolo ake. Choncho Simei anapita ndi kukatenga akapolo ake ku Gati ndipo anabwera nawo.

41 Solomoni atawuzidwa kuti Simei anatuluka mu Yerusalemu ndi kupita ku Gati ndipo kuti wabwerako, 42 mfumu inamuyitanitsa Simei ndipo inamufunsa kuti, “Kodi sindinakulumbiritse mʼdzina la Yehova ndi kukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluka kupita kwina kulikonse, udziwe kuti udzafa’? Nthawi imeneyo iwe unandiwuza kuti, ‘Zimene mwanena nʼzabwino. Ine ndidzamvera.’ 43 Chifukwa chiyani tsono sunasunge lumbiro lako kwa Yehova? Bwanji nanga sunamvere lamulo limene ndinakuwuza?”

44 Mfumuyo inawuzanso Simei kuti, “Ukudziwa mu mtima mwakomo zoyipa zonse zimene unachitira abambo anga Davide. Tsopano Yehova akubwezera zoyipa zakozo. 45 Koma Mfumu Solomoni idzadalitsidwa ndipo mpando waufumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova kwamuyaya.”

46 Pamenepo mfumu inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo iye anapita kukakantha Simei ndi kumupha.

Tsono ufumu unakhazikika mʼdzanja la Solomoni.

Agalatiya 6

Kuchita Zabwino kwa Onse

Abale, ngati munthu agwa mʼtchimo lililonse, inu amene Mzimu amakutsogolerani, mumuthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe. Thandizanani kusenza zolemetsa zanu, ndipo mʼnjira imeneyi mudzakwanitsa lamulo la Khristu. Ngati wina adziyesa kanthu pamene iyeyo sali kanthu konse, akudzinamiza yekha. Munthu aliyense aziyesa yekha ntchito zake mmene zilili. Ngati zili bwino, adzatha kunyadira chifukwa cha ntchito zake zokhazo, iyeyo asadzifanizire ndi munthu wina wake, pakuti aliyense ayenera kusenza katundu wake.

Koma munthu amene akuphunzira mawu, agawireko mphunzitsi wake zinthu zonse zabwino zimene iye ali nazo.

Musanamizidwe: nʼkosatheka kupusitsa Mulungu. Munthu amakolola zimene wafesa. Pakuti amene amafesa zokondweretsa thupi lake la uchimo, kuchokera ku khalidwe limenelo adzakolola chiwonongeko; amene amafesa zokondweretsa Mzimu, kuchokera kwa Mzimu adzakolola moyo wosatha. Tisatope nʼkuchita zabwino, pakuti pa nthawi yoyenera tidzakolola ngati sititopa. 10 Nʼchifukwa chake ngati tapeza mpata, tiyenera kuchitira zabwino anthu onse, makamaka amene ndi a banja la okhulupirira.

Osati Mdulidwe koma Kulengedwa Mwatsopano

11 Onani zilembo zazikulu zimene ine ndikulemba ndi dzanja langa.

12 Onse amene akufuna kuoneka abwino pamaso pa anthu akukukakamizani kuti muchite mdulidwe. Akuchita izi ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti apewe kuzunzidwa chifukwa cha mtanda wa Khristu. 13 Pakuti ngakhale iwowa amene anachita mdulidwe satsata Malamulo, komabe akufuna kuti muchite mdulidwe kuti anyadire mdulidwe wanuwo. 14 Ine sindingathe kunyadira kanthu kena koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu, kudzera mwa mtandawo dziko lapansi linapachikidwa kwa ine ndi ine ku dziko lapansi. 15 Pakuti kaya mdulidwe kapena kusachita mdulidwe, sizitanthauza kanthu; chofunika ndi kulengedwa mwatsopano. 16 Mtendere ndi chifundo zikhale kwa onse amene amatsata chiphunzitso ichi, ndi pa Israeli wa Mulungu.

17 Pomaliza wina asandivutitse, pakuti mʼthupi mwanga muli zizindikiro za Yesu.

18 Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu zikhale ndi mzimu wanu abale. Ameni.

Ezekieli 33

Ezekieli Akhala Mlonda

33 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda. Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo. Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha. Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka. Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’

“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze. Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako.

10 “Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” 11 Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?

12 “Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ 13 Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. 14 Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, 15 monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. 16 Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.

17 “Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama. 18 Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo. 19 Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo. 20 Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.”

Mbiri ya Kuwonongeka kwa Yerusalemu

21 Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!” 22 Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.

23 Ndipo Yehova anandiyankhula kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’ 25 Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli? 26 Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’

27 “Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri. 28 Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako. 29 Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’

30 “Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’ 31 Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo. 32 Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.

33 “Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”

Masalimo 81-82

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu.

81 Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu;
    Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!
Yambani nyimbo, imbani tambolini
    imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.

Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano,
    ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;
ili ndi lamulo kwa Israeli,
    langizo la Mulungu wa Yakobo.
Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe
    pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto,
    kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.

Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo;
    Manja awo anamasulidwa mʼdengu.
Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani,
    ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu;
    ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba.
            Sela

“Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani
    ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!
Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu;
    musadzagwadire mulungu wina.
10 Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.
    Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.

11 “Koma anthu anga sanandimvere;
    Israeli sanandigonjere.
12 Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo
    kuti atsate zimene ankafuna.

13 “Anthu anga akanangondimvera,
    Israeli akanatsatira njira zanga,
14 nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo
    ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
15 Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake,
    ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
16 Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri;
    ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”

Salimo la Asafu.

82 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;
    Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

“Mudzateteza osalungama mpaka liti,
    ndi kukondera anthu oyipa?
Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
    mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;
    apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.
    Amayendayenda mu mdima;
    maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,
    nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
Koma mudzafa ngati anthu wamba;
    mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”

Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
    pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.