Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 16

Davide ndi Ziba

16 Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.

Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?”

Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.”

Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?”

Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”

Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.”

Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.”

Simei Atukwana Davide

Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera. Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake. Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe! Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”

Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”

10 Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ”

11 Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero. 12 Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.”

13 Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi. 14 Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula.

Malangizo a Husai ndi Ahitofele

15 Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye. 16 Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”

17 Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?”

18 Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse. 19 Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.”

20 Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?”

21 Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.” 22 Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona.

23 Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.

2 Akorinto 9

Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu. Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu. Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera. Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo. Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.

Kupereka Mowolowamanja

Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. Paja analemba kuti,

“Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
    chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.”

10 Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. 11 Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.

12 Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. 13 Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense. 14 Ndipo iwowo adzakupemphererani mwachikondi chifukwa cha chisomo choposa chimene Ambuye wakupatsani. 15 Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!

Ezekieli 23

Za Yerusalemu ndi Samariya

23 Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba.

“Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.

“Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. 10 Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi.

11 “Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. 12 Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. 13 Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi.

14 “Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, 15 atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. 16 Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. 17 Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. 18 Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. 19 Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. 20 Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. 21 Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.

22 “Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse. 23 Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo. 24 Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire. 25 Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto. 26 Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali. 27 Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso.

28 “Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. 29 Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, 30 zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. 31 Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako.

32 “Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“Udzamwera chikho cha mkulu wako,
    chikho chachikulu ndi chakuya;
anthu adzakuseka ndi kukunyoza,
    pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.
33 Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni.
    Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu,
    chikho cha mkulu wako Samariya.
34 Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza.
    Tsono udzaphwanyaphwanya chikhocho
    ndipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake.

Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.

35 “Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.”

36 Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. 37 Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. 38 Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. 39 Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.

40 “Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. 41 Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine.

42 “Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. 43 Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ 44 Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. 45 Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.

46 “Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo. 47 Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo.

48 “Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. 49 Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”

Masalimo 70-71

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.

70 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
    Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
Iwo amene akufunafuna moyo wanga
    achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
    abwezedwe mopanda ulemu.
Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
    abwerere chifukwa cha manyazi awo.
Koma onse amene akufunafuna Inu
    akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
    nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”

Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
    bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
    Inu Yehova musachedwe.
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
    musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
    mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
    pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
    kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.

Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
    chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
    Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
    ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
    koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
    kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.

Musanditaye pamene ndakalamba;
    musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
    iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
    mutsatireni ndi kumugwira,
    pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
    bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
    iwo amene akufuna kundipweteka
    avale chitonzo ndi manyazi.

14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
    ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
    za chipulumutso chanu tsiku lonse,
    ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
    Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
    ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
    musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
    kwa mibado yonse yakutsogolo.

19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
    Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
    amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
    ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
    kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
    mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
    ndi kunditonthozanso.

22 Ndidzakutamandani ndi zeze
    chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
    Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
    pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
    amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
    tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
    achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.