Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 31

Imfa ya Sauli ndi Ana Ake

31 Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza kwambiri.

Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.”

Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa naye limodzi. Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.

Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.

Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa. Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. 10 Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba yopembedzera Asitoreti, ndipo thupi lake analikhomera pa khoma la mzinda wa Beti-Sani.

11 Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, 12 anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto. 13 Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.

1 Akorinto 11

11 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.

Makhalidwe Oyenera pa Mapemphero

Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani. Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo. Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake. Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.

Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna. Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna. 10 Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake. 11 Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. 12 Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.

13 Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu? 14 Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali, 15 koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu. 16 Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.

Mgonero wa Ambuye

17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino. 18 Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. 19 Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. 20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. 21 Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. 22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.

23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi. 24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.” 26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.

27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi. 29 Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe. 30 Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo. 31 Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso. 32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

33 Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane. 34 Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo.

Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.

Ezekieli 9

Opembedza Mafano Aphedwa

Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.” Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.

Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”

Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo. Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.

Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse. Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”

Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’ 10 Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”

11 Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”

Masalimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.