Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 1

Adoniya Adziyika Kukhala Mfumu

Mfumu Davide atakalamba sankamva kufunda ngakhale akamufunditsa mabulangeti. Choncho nduna zake zinamuwuza kuti, “Tiloleni tifune namwali woti azikhala nanu ndi kumakusamalirani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti mbuye wathu mfumu muzimva kufundira.”

Kotero anafunafuna mʼdziko lonse la Israeli mtsikana wokongola ndipo anapeza Abisagi wa ku Sunemu, nabwera naye kwa mfumu. Mtsikanayo anali wokongola kwambiri ndipo ankasamalira mfumu ndi kumayitumikira, koma mfumuyo sinakhale naye malo amodzi.

Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake. (Abambo ake sanalowererepo nʼkamodzi komwe ndipo sanafunsepo kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Adoniyayo anali wokongola kwambiri ndipo anali wopondana ndi Abisalomu).

Adoniya anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya ndiponso Abiatara wansembe, ndipo iwowa anamuthandiza. Koma Zadoki wansembe, Benaya mwana wa Yehoyada, mneneri Natani, Simei ndi Rei ndiponso asilikali amphamvu a Davide sanamutsate Adoniya uja.

Kenaka Adoniya anapereka nsembe za nkhosa ndi ngʼombe ndiponso ana angʼombe onenepa ku Mwala wa Zohereti kufupi ndi Eni Rogeli. Iye anayitana abale ake onse, ana aamuna a mfumu ndiponso akuluakulu onse a ku Yuda, 10 koma sanayitane mneneri Natani kapena Benaya kapenanso asilikali amphamvu a Davide ngakhalenso mʼbale wake Solomoni.

11 Pamenepo Natani anafunsa Batiseba, amayi ake a Solomoni, kuti, “Kodi simunamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, walowa ufumu popanda Davide mbuye wathu kudziwa? 12 Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. 13 Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’ 14 Pamene inu muzikayankhula ndi mfumu, ine ndidzalowa ndi kuchitira umboni mawu anuwo.”

15 Choncho Batiseba anapita nakalowa ku chipinda kukaonana ndi mfumu imene inali itakalamba kwambiri, kumene Abisagi wa ku Sunemu uja ankayisamalira. 16 Batiseba anagwada nalambira mfumu.

Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi nʼchiyani chimene ukufuna?”

17 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’ 18 Koma tsopano Adoniya ndiye walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu, simukuzidziwa zimenezi. 19 Ndipo wapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndi nkhosa ndi mbuzi ndipo wayitana ana anu onse, wansembe Abiatara ndiponso Yowabu mkulu wa ankhondo, koma sanayitane kapolo wanu Solomoni. 20 Mbuye wanga mfumu, maso a Aisraeli onse ali pa inu, kuti adziwe kuchokera kwa inu amene adzakhala pa mpando waufumu wa mbuye wanga mʼmalo mwanu. 21 Mukapanda kutero, mbuye wanga, mukadzangotisiya nʼkulondola kumene kunapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wangayu Solomoni adzatiyesa owukira.”

22 Pamene Batiseba amayankhula ndi mfumu, mneneri Natani analowa. 23 Ndipo anthu anawuza mfumu kuti, “Kwabwera mneneri Natani.” Kotero iye anafika pamaso pa mfumu ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.

24 Natani anafunsa kuti, “Mbuye wanga mfumu, kodi mwalengeza kuti Adoniya adzakhala mfumu mʼmalo mwanu, ndi kuti adzakhala pa mpando wanu waufumu? 25 Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’ 26 Koma ine kapolo wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso kapolo wanu Solomoni sanatiyitane. 27 Kodi zimenezi mbuye wanga mfumu mwazichita ndinu, osawawuza atumiki anu kuti adziwe amene adzakhale pa mpando waufumu mʼmalo mwanu?”

Davide Alonga Ufumu Solomoni

28 Pamenepo mfumu Davide anati, “Muyitaneni Batiseba.” Kotero Batiseba analowa ndipo anayimirira pamaso pa mfumu.

29 Tsono mfumu inalumbira kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene anandipulumutsa ine ku mavuto onse, 30 ndithu ine lero ndichita zonse zimene ndinalumbira kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, mwana wako Solomoni adzakhala mfumu mʼmalo mwanga ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.”

31 Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”

32 Mfumu Davide anati, “Ndiyitanireni wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Atafika pamaso pa mfumu, 33 mfumuyo inati kwa iwo, “Tengani atumiki anga ndipo mukweze mwana wanga Solomoni pa bulu wanga ndipo mupite naye ku Gihoni. Mukalize lipenga ndi kufuwula kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Solomoni!’ 34 Kumeneko Zadoki wansembe ndi mneneri Natani akamudzoze kuti akhale mfumu ya Israeli. Kenaka mukalize lipenga ndi kumanena kuti ‘Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni.’ 35 Ndipo pobwera muzikamutsata pambuyo. Iyeyo akabwere kuno ndi kudzakhala pa mpando wanga waufumu ndi kudzalamulira mʼmalo mwanga. Ndamusankha kukhala wolamulira Israeli ndi Yuda.”

36 Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, “Ameni! Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu akhazikitse kuti zichitike motero. 37 Monga momwe Yehova wakhalira ndi inu mbuye wanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni ndi kukhazikitsa ufumu wake kuti ukhale waukulu kuposa ufumu wa mbuye wanga Mfumu Davide!”

38 Kotero Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndiponso Apeleti, anthu oteteza mfumu, anapita kukamukweza Solomoni pa bulu wa Mfumu Davide ndi kupita naye ku Gihoni. 39 Wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta yochokera ku malo opatulika ndi kumudzoza Solomoni. Kenaka analiza lipenga ndipo anthu onse anafuwula kuti, “Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni!” 40 Ndipo anthu onsewo anapita namutsatira pambuyo akuyimba zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero nthaka inagwedezeka chifukwa cha phokoso lawo.

41 Adoniya pamodzi ndi anthu onse oyitanidwa amene anali naye anamva zimenezi pamene ankamaliza madyerero awo. Atamva kulira kwa malipenga, Yowabu anafunsa kuti, “Kodi phokoso lonselo mu mzindamo likutanthauza chiyani?”

42 Iye akuyankhula, Yonatani mwana wa wansembe Abiatara anafika. Adoniya anati, “Lowa. Munthu wabwino ngati iwe ayenera kubweretsa nkhani yabwino.”

43 Yonatani anayankha Adoniya kuti, “Ayi ndithu, zinthu sizili bwino! Mbuye wathu Mfumu Davide walonga Solomoni ufumu. 44 Mfumu yatuma Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ku Gihoni ndipo iwo amukweza pa bulu wa mfumu, 45 ndipo Zadoki wansembe ndi mneneri Natani adzoza Solomoni ku Gihoni kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akululutira, kotero kuti mu mzinda monse muli phokoso lokhalokha. Ndiyetu phokoso limene mukulimvalo. 46 Ndipo Solomoni wakhala kale pa mpando wake waufumu. 47 Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake, 48 inati, ‘Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wasankha wolowa mʼmalo mwanga ine ndikanali ndi moyo lero lino.’ ”

49 Anthu onse amene Adoniya anawayitana ananjenjemera ndi mantha, ndipo anayimirira, kenaka anamwazikana. 50 Koma Adoniya, poopa Solomoni, anapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira msonga za guwa lansembe. 51 Tsono Solomoni anawuzidwa kuti, “Adoniya akukuopani inu Mfumu Solomoni ndipo wagwira msonga za guwa lansembe. Iye akuti, ‘Mfumu Solomoni alumbire kuti sadzapha kapolo wake ndi lupanga.’ ”

52 Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.” 53 Pamenepo Mfumu Solomoni inatuma anthu ndipo anakamutenga paguwa paja. Adoniya anabwera ndi kudzalambira Mfumu Solomoni, ndipo Solomoni anati, “Pita ku nyumba yako.”

Agalatiya 5

Ufulu mwa Khristu

Khristu anatimasula kuti tikhale mfulu. Tsono chirimikani, ndipo musakodwenso mʼgoli la ukapolo.

Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse. Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse. Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo. Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza. Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.

Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi? Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani. “Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.” 10 Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani. 11 Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa. 12 Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha!

Moyo mwa Mzimu Woyera

13 Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi. 14 Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 15 Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane.

16 Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. 17 Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna. 18 Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.

19 Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; 20 kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko 21 ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.

22 Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, 23 kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi. 24 Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo. 25 Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera. 26 Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.

Ezekieli 32

Nyimbo ya Maliro a Farao

32 Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,

“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.
    Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.
Umakhuvula mʼmitsinje yako,
    kuvundula madzi ndi mapazi ako
    ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.

“Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,
    ndidzakuponyera khoka langa
    ndi kukugwira mu ukonde wanga.
Ndidzakuponya ku mtunda
    ndi kukutayira pansi.
Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,
    ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri
    ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,
    mpaka kumapiri komwe,
    ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba
    ndikudetsa nyenyezi zake.
Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,
    ndipo mwezi sudzawala.
Zowala zonse zamumlengalenga
    ndidzazizimitsa;
    ndidzachititsa mdima pa dziko lako,
            akutero Ambuye Yehova.
Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri
    pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
    ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
10 Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,
    ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe
    pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.
Pa nthawi ya kugwa kwako,
    aliyense wa iwo adzanjenjemera
    moyo wake wonse.

11 “ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,

“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni
    lidzabwera kudzalimbana nawe.
12 Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe
    ndi lupanga la anthu amphamvu,
    anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzathetsa kunyada kwa Igupto,
    ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse
    zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.
Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu
    kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
14 Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake
    ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,
            akutero Ambuye Yehova.
15 Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;
    ndikadzawononga dziko lonse
ndi kukantha onse okhala kumeneko,
    adzadziwa kuti ndine Yehova.’

16 “Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”

17 Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. 19 Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ 20 Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. 21 Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’

22 “Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. 23 Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.

24 “Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. 25 Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.

26 “Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. 27 Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.

28 “Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.

29 “Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.

30 “Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.

31 “Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. 32 Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

Masalimo 80

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.

80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
    Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
    kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
    bwerani ndi kutipulumutsa.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
    kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
Mwawadyetsa buledi wa misozi;
    mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
    ndipo adani athu akutinyoza.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto;
    munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
Munawulimira munda wamphesawo,
    ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
10 Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake,
    mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
11 Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja,
    mphukira zake mpaka ku mtsinje.

12 Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake
    kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
13 Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga
    ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse!
    Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone!
Uyangʼanireni mpesa umenewu,
15     muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala,
    mwana amene inu munamukuza nokha.

16 Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto;
    pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
    mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
    titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.