M’Cheyne Bible Reading Plan
Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Yuda
2 Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?”
Yehova anayankha kuti, “Pita.”
Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?”
Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.”
2 Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli. 3 Davide anatenganso anthu amene anali nawo aliyense ndi banja lake, ndipo anakakhala ku midzi ya ku Hebroni. 4 Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda.
Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli, 5 iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda. 6 Tsopano Yehova akuonetseni kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake ndipo inenso ndidzakukomerani mtima chifukwa munachita zimenezi. 7 Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.”
Nkhondo Pakati pa Otsatira Davide ndi Otsatira Sauli
8 Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu. 9 Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense.
10 Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide. 11 Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.
12 Abineri mwana wa Neri, pamodzi ndi ankhondo a Isi-Boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu ndi kupita ku Gibiyoni. 13 Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo.
14 Kenaka Abineri anati kwa Yowabu, “Tiye tibweretse ena mwa anyamata athu kuti amenyane patsogolo pathupa.”
Yowabu anayankha, “Chabwino, amenyane.”
15 Kotero anayimirira ndipo anawawerenga: anyamata khumi ndi awiri a fuko la Benjamini ndi Isi-Boseti mwana wa Sauli ndiponso anyamata khumi ndi awiri a Davide. 16 Tsono aliyense anagwira mutu wa mnzake namubaya mnzakeyo mʼnthiti ndi mpeni ndipo onse anagwera pansi limodzi. Kotero malo amenewo ku Gibiyoni amatchedwa Helikati Hazurimu.
17 Tsiku limeneli nkhondo yake inali yoopsa kwambiri, ndipo Abineri ndi ankhondo a Israeli anagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide.
18 Ana atatu aamuna a Zeruya, Yowabu, Abisai ndi Asaheli anali komweko. Koma Asaheli anali waliwiro ngati insa. 19 Iye anathamangitsa Abineri ndipo sanakhotere kumanja kapena kumanzere pamene amamutsatira. 20 Abineri anayangʼana mʼmbuyo ndipo anafunsa, “Kodi ndiwe Asaheli?”
Iye anayankha kuti, “Ndine.”
21 Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa.
22 Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?”
23 Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa.
24 Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni. 25 Pamenepo anthu a fuko la Benjamini anasonkhana kudzathandiza Abineri. Iwo anapanga gulu ndipo anayima pamwamba pa phiri.
26 Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?”
27 Yowabu anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, ukanapanda kuyankhula, ankhondo anga akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mmawa.”
28 Chomwecho Yowabu analiza lipenga, ndipo ankhondo onse anayima. Iwo analeka kuthamangitsa Aisraeli kapena kumenyana nawo.
29 Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu.
30 Choncho Yowabu anabwerera kuchokera kothamangitsa Abineri ndipo anasonkhanitsa ankhondo ake onse. Kupatula Asaheli, panali ankhondo khumi ndi anayi a Davide amene anasowa. 31 Koma ankhondo a Davide anapha ankhondo a fuko la Benjamini 360 amene anali ndi Abineri. 32 Iwo anatenga Asaheli ndi kukamuyika mʼmanda a abambo ake ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi ankhondo ake anayenda usiku wonse ndi kufika ku Hebroni kukucha.
Kupambana kwa Chikondi
13 Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera. 2 Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu. 3 Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.
4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira. 5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa. 6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi. 7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
8 Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha. 9 Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe. 10 Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha. 11 Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya. 12 Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.
13 Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
Chiweruzo pa Atsogoleri a Israeli
11 Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. 2 Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. 3 Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. 4 Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ”
5 Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ 6 Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.
7 “Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. 8 Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. 9 Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. 10 Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 11 Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. 12 Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ”
13 Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”
14 Yehova anayankhula nane kuti, 15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”
Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli
16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’
17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.
18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.
Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.
Salimo la Asafu.
50 Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
2 Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
Mulungu akuwala.
3 Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
moto ukunyeketsa patsogolo pake,
ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
4 Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
5 Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
6 Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
7 Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
ndine Mulungu, Mulungu wako.
8 Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
9 Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako
kapena mbuzi za mʼkhola lako,
10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga
ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
11 Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri
ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
12 Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,
pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
13 Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna
kapena kumwa magazi a mbuzi?
14 “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,
kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
15 Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;
Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,
“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga
kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
17 Iwe umadana ndi malangizo anga
ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
18 Ukaona wakuba umamutsatira,
umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa
ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
20 Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako
ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
21 Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;
umaganiza kuti ndine wofanana nawe
koma ndidzakudzudzula
ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
chipulumutso cha Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.