Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 26

Davide Apewa Kupha Sauli Kachiwiri

26 Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya nati, “Davide akubisala ku phiri la Hakila, limene limayangʼanana ndi Yesimoni.”

Choncho Sauli ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake 3,000 napita ku chipululu cha Zifi kukafunafuna Davide ku chipululuko. Sauli anamanga msasa wake mʼmbali mwa njira yopita ku phiri la Hakila moyangʼanana ndi Yesimoni. Koma Davide anali mʼchipululumo. Davide ataona kuti Sauli amamulondola mpaka kumeneko, iye anatumiza anthu okazonda ndipo anapeza kuti Sauli wafikadi ndithu.

Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira.

Ndipo Davide anafunsa Ahimeleki Mhiti ndi Abisai mwana wa Zeruya, mʼbale wa Yowabu kuti, “Ndani adzapita nane ku msasa kwa Sauli?”

Abisai anayankha kuti, “Ine ndidzapita nanu.”

Choncho Davide ndi Abisai anapita ku misasa ya ankhondowo usiku. Atafika anangopeza Sauli ali gone mu msasa wake mkondo wake atawuzika pansi pafupi ndi mutu wake, Abineri ndi ankhondo onse anali atagona momuzungulira.

Abisai anawuza Davide kuti, “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu. Tsopano ndiloleni ndimukhomere pansi ndi mkondo wangawu kamodzinʼkamodzi. Sindimulasa kawiri.”

Koma Davide anamuyankha Abisai kuti, “Usamuphe! Ndani adzapha wodzozedwa wa Yehova ndi kupezeka wosalakwa? 10 Davide anati, Pali Yehova wamoyo, Yehova mwini ndiye adzamukanthe, mwina tsiku lake lomwalira lidzafika, kapena adzapita ku nkhondo nakaphedwa komweko. 11 Koma Yehova andiletse kuti ndisapweteke wodzozedwa wa Yehova. Tsopano tingotenga mkondo umene uli ku mutu kwakewo ndi botolo la madzilo ndipo tizipita.”

12 Motero Davide anatenga mkondo ndi botolo lamadzi zimene zinali ku mutu kwa Sauli ndipo anachoka. Palibe amene anaona zimenezi kapena kudziwa, ndipo palibenso amene anadzuka. Onse anali mʼtulo, chifukwa Yehova anawagonetsa tulo tofa nato.

13 Pambuyo pake Davide anadutsa nakakwerera mbali ina ya phiri, ndi kuyimirira pamwamba pa phiri patali. Pakati pawo panali mpata waukulu. 14 Davide anayitana gulu lankhondo ndi Abineri mwana wa Neri nawafunsa kuti, “Kodi sundiyankha ine Abineri?”

Abineri anayankha kuti, “Ndiwe yani amene ukuyitana mfumu?”

15 Davide anamufunsa Abineri kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndipo wofanana nawe ndani mu Israeli? Nʼchifukwa chiyani sunateteze mbuye wako mfumu? Munthu wina anabwera kumeneko. 16 Chimene wachita iwe si chabwino. Pali Yehova wamoyo iwe ndi asilikali ako muyenera kufa chifukwa simunateteze mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Tayangʼanayangʼana. Uli kuti mkondo wa mfumu ndi botolo lamadzi zimene zinali kumutu kwa mfumu?”

17 Sauli anazindikira mawu a Davide ndipo anafunsa kuti, “Kodi amenewa ndi mawu ako Davide mwana wanga?”

Davide anayankha, “Inde ndi anga, mbuye wanga mfumu. 18 Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukundilonda ine mtumiki wanu? Kodi ine ndachita chiyani ndipo ndapezeka ndi cholakwa chotani? 19 Tsopano mbuye wanga mfumu tamverani mawu a mtumiki wanu. Ngati ndi Yehova wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, ndiye alandire chipepeso. Koma ngati ndi anthu amene achita zimene, ndiye Yehova awatemberere popeza andipirikitsa lero kundichotsa mʼdziko la Yehova, namati, ‘Pita kapembedze milungu ina.’ 20 Tsopano musalole kuti magazi anga akhetsedwe kutali ndi Yehova pakuti mfumu ya Israeli yatuluka kudzafunafuna ine nsabwe, monga mmene munthu asakira nkhwali ku mapiri.”

21 Ndipo Sauli anati, “Ine ndachimwa. Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakuchitanso choyipa popeza lero wauwona moyo wanga ngati wamtengowapatali. Taona, ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.”

22 Davide anayankha kuti, “Nawu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi wa anyamata anu abwere adzatenge. 23 Yehova amadalitsa munthu aliyense wolungama ndi wokhulupirika. Yehova anakuperekani lero mʼmanja mwanga, koma ine sindinakhudze wodzozedwa wa Yehova. 24 Monga momwe ine lero ndachitira kuwuyesa moyo wanu ngati wamtengowapatali, momwemonso Yehova awuyese moyo wanga wamtengowapatali ndipo andipulumutse mʼmavuto anga onse.”

25 Ndipo Sauli anawuza Davide kuti, “Yehova akudalitse iwe Davide mwana wanga. Udzachita zinthu zazikulu ndipo udzapambana.”

Choncho Davide anayenda njira yake ndipo Sauli anabwerera kwawo.

1 Akorinto 7

Ukwati

Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire. Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake. Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake. Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso. Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa. Ndikunena zimenezi mokulolani chabe osati mokulamulani. Ine ndikanakonda anthu akanakhala ngati ine. Koma poti munthu aliyense ali ndi mphatso yakeyake yochokera kwa Mulungu, wina mphatso yake, wina yakenso.

Tsono kwa osakwatira onse, ndi akazi amasiye ndikuti, ndi bwino kwa iwo kukhala osakwatira monga mmene ndilili inemu. Koma ngati sangathe kudziretsa, akwatire, popeza ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kudzizunza ndi chilakolako.

10 Kwa amene ali pa banja ndikupatsani lamulo ili (osati langa koma la Ambuye): Mkazi asalekane ndi mwamuna wake. 11 Koma ngati atatero, asakwatiwenso, apo ayi, abwerere kwa mwamuna wakeyo. Ndipo mwamuna asaleke mkazi wake.

12 Kwa ena onse ndikunena izi (ineyo osati Ambuye); ngati mʼbale wina ali ndi mkazi wosakhulupirira ndipo mkaziyo walola kukhala pa banja ndi mʼbaleyo, ameneyo asamuleke. 13 Ngati mayi wina ali ndi mwamuna wosakhulupirira ndipo mwamunayo walola kukhala pa banja ndi mayiyo, ameneyo asamuleke. 14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wakeyo, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mwamuna wokhulupirirayo. Kupanda apo ana anu akanakhala odetsedwa, koma mmene zililimu ndi oyeretsedwa.

15 Koma ngati wosakhulupirira achoka, mulekeni achoke. Zikatero ndiye kuti mwamuna kapena mkazi wokhulupirirayo sali womangikanso. Mulungu anatiyitana kuti tikhale mu mtendere. 16 Kodi iwe, mkazi, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mwamuna wako? Kapena iwe, mwamuna, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mkazi wako?

Kukhala Moyo Wosinthika

17 Koma aliyense akhale moyo umene Ambuye anamupatsa, umene Mulungu anamuyitanira. Ili ndiye lamulo limene ndalikhazikitsa mʼmipingo yonse. 18 Ngati pamene munthu amayitanidwa anali atachita mdulidwe, asavutike nʼkubisa za mdulidwe wakewo. Ngatinso pamene munthu amayitanidwa nʼkuti asanachite mdulidwe, asachite mdulidwe. 19 Mdulidwe si kanthu, kusachita mdulidwe si kanthunso. Chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu. 20 Aliyense akhale monga analili pamene Mulungu anamuyitana.

21 Kodi munali kapolo pamene Mulungu anakuyitanani? Musavutike nazo zimenezi. Koma ngati mutapeza mwayi woti mulandire ufulu, ugwiritseni ntchito mwayiwo. 22 Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu. 23 Munagulidwa ndi mtengowapatali, choncho musakhalenso akapolo a anthu. 24 Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analili pamene Mulungu anamuyitana.

Osakwatiwa

25 Tsopano za anamwali: Ine ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye, koma ndipereka maganizo anga monga ngati munthu amene mwachifundo cha Ambuye ndine wodalirika. 26 Chifukwa cha masautso a masiku ano, ndikuganiza kuti nʼkwabwino kuti munthu akhale monga mmene alili. 27 Kodi ndinu wokwatira? Musalekane. Kodi ndinu wosakwatira? Musafunefune mkazi. 28 Komabe ngati mukwatira simunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa sanachimwenso. Koma amene walowa mʼbanja adzakumana ndi zovuta zambiri mʼmoyo uno, ndipo sindikufuna kuti inu mukumane ndi zovutazi.

29 Abale, chimene ndikutanthauza nʼchakuti nthawi yatha. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale ngati sanakwatire. 30 Amene akulira akhale monga ngati sakulira. Amene akukondwa akhale ngati sakukondwa. Amene akugula zinthu akhale ngati alibe zinthuzo. 31 Amene akugwiritsa ntchito zinthu za dziko lapansi lino, akhale ngati sizikuwakhudza. Pakuti dziko lapansi lino mmene lilirimu, likupita.

32 Ine ndikufuna kuti mumasuke ku nkhawa zanu. Munthu wosakwatira amangolabadira za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuyewo. 33 Koma wa pa banja amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mkazi wake, 34 ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake. 35 Ndikunena izi kufuna kuthandiza inu nomwe osati kukupanikizani. Ine ndikufuna mukhale moyenera mosadzigawa pa kudzipereka kwanu kwa Ambuye.

36 Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi. 37 Koma ngati wina motsimikiza mtima wake, popanda womukakamiza, koma akuchita mwa chifuniro chake, ndipo watsimikiza mtima kuti samukwatira namwaliyo, munthuyu akuchitanso chokhoza. 38 Choncho amene akukwatira namwali amene ali naye pa ubwenzi, akuchita bwino, koma amene sangakwatire namwaliyo akuchita bwino koposa.

39 Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati nthawi zonse pamene mwamuna wake ali ndi moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi wina aliyense amene akumufuna, koma mwamunayo akhale wa mwa Ambuye. 40 Mʼmaganizo anga, mkaziyo adzakhala wokondwa koposa ngati atangokhala wosakwatiwa. Ndipo ndikuganiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.

Ezekieli 5

Chizindikiro cha Chiweruzo

Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu. Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako. Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.”

Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira. Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.

“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.

“Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona. Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo. 10 Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi. 11 Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni. 12 Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.

13 “Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.

14 “Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo 15 Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula. 16 Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. 17 Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”

Masalimo 42-43

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
    kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
    Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
Misozi yanga yakhala chakudya changa
    usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”
Zinthu izi ndimazikumbukira
    pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
    kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
    pakati pa anthu a pa chikondwerero.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
    pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi     Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
    kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
    ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
Madzi akuya akuyitana madzi akuya
    mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
    andimiza.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
    nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
    pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
    “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
    pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”

11 Bwanji ukumva chisoni,
    iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
    Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
    Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
43 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;
    ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;
    mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.
    Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?
Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu
    kuti zinditsogolere;
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,
    kumalo kumene inu mumakhala.
Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
    kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.
Ndidzakutamandani ndi zeze,
    Inu Mulungu wanga.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu,
    pakuti ndidzamutamandabe Iye,
    Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.