M’Cheyne Bible Reading Plan
Agibiyoni Abwezera
21 Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.”
2 Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu). 3 Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?”
4 Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.”
Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”
5 Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli, 6 mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.”
Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.”
7 Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova. 8 Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati. 9 Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele.
10 Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku. 11 Davide atawuzidwa zimene Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa, mzikazi wa Sauli anachita, 12 anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa). 13 Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi.
14 Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo.
Nkhondo ndi Afilisti
15 Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri. 16 Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide. 17 Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.”
18 Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai.
19 Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu.
20 Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. 21 Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha.
22 Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake.
1 Paulo mtumwi, osati wosankhidwa ndi anthu kapena kutumidwa ndi munthu ayi, koma Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate amene anamuukitsa Yesuyo kwa akufa, 2 pamodzi ndi abale onse amene ali nane,
Kulembera mipingo ya ku Galatiya:
3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu. 4 Yesuyo anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu kuti atipulumutse ku njira za moyo woyipa uno, molingana ndi chifuniro cha Mulungu ndi Atate athu. 5 Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ameni.
Uthenga Wabwino ndi Umodzi Wokha
6 Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana, 7 umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. 8 Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! 9 Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”
10 Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu.
Paulo Woyitanidwa ndi Mulungu
11 Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi. 12 Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu.
13 Pakuti inu munamva za moyo wanga wakale mʼChiyuda, mmene ndinkazunzira mpingo wa Mulungu koopsa ndi kuyesetsa kuwuwononga. 14 Ine ndinkapambana Ayuda ambiri a msinkhu wanga pochita za Chiyuda, ndipo ndinali wachangu koposa pa miyambo ya makolo athu. 15 Koma Mulungu, amene anandipatula ine ndisanabadwe, ndi kundiyitana mwachisomo chake, atakondweretsedwa 16 kuvumbulutsa Mwana wake mwa ine, kuti ndikalalikire Khristuyo pakati pa anthu a mitundu ina, ine sindinapemphe nzeru kwa munthu aliyense. 17 Ine sindinapite ku Yerusalemu kukaonana ndi amene anali atumwi ine ndisanakhale mtumwi. Mʼmalo mwake nthawi yomweyo ndinapita ku Arabiya ndi kubwereranso ku Damasiko.
18 Pambuyo pake, patatha zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu kukaonana ndi Petro ndikukhala naye masiku khumi ndi asanu. 19 Ine sindinaonane ndi atumwi enawo koma Yakobo yekha, mʼbale wa Ambuye. 20 Ine ndikutsimikizira inu pamaso pa Mulungu kuti zimene ndikukulemberani si zonama ayi. 21 Pambuyo pake ndinapita ku Siriya ndi ku Kilikiya. 22 Koma sindimadziwika ndi nkhope ku mipingo ya ku Yudeya imene ili mwa Khristu. 23 Iwo anangomva mbiri yokha yakuti, “Munthu amene poyamba anatizunza ife, tsopano akulalikira chikhulupiriro chimene iyeyo nthawi ina anafuna kuchiwononga.” 24 Ndipo iwo anayamika Mulungu chifukwa cha ine.
Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo
28 Yehova anandiyankhula nati: 2 “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza
umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;
ndimakhala pa mpando wa mulungu
pakati pa nyanja.’
Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,
ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
3 Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.
Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
4 Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako
unadzipezera chuma
ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva
mʼnyumba zosungira chuma chako.
5 Ndi nzeru zako zochitira malonda
unachulukitsa chuma chako
ndipo wayamba kunyada
chifukwa cha chuma chakocho.
6 “ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Popeza umadziganizira
kuti ndiwe mulungu,
7 Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,
kuti adzalimbane nawe.
Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,
ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
8 Iwo adzakuponyera ku dzenje
ndipo udzafa imfa yoopsa
mʼnyanja yozama.
9 Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’
pamaso pa iwo amene akukupha?
Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,
mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
10 Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe
mʼmanja mwa anthu achilendo.
Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”
11 Yehova anandiyankhula kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,
wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
13 Iwe unkakhala ngati mu Edeni,
munda wa Mulungu.
Miyala yokongola ya mitundu yonse:
rubi, topazi ndi dayimondi,
kirisoliti, onikisi, yasipa,
safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.
Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.
Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
14 Ndinayika kerubi kuti azikulondera.
Unkakhala pa phiri langa lopatulika,
ndipo unkayendayenda
pakati pa miyala ya moto.
15 Makhalidwe ako anali abwino
kuyambira pamene unalengedwa
mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
16 Unatanganidwa ndi zamalonda.
Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu
ndi kumachimwa.
Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.
Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa
kukuchotsa ku miyala yamoto.
17 Unkadzikuza mu mtima mwako
chifukwa cha kukongola kwako,
ndipo unayipitsa nzeru zako
chifukwa chofuna kutchuka.
Kotero Ine ndinakugwetsa pansi
kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
18 Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.
Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.
Choncho ndinabutsa moto pakati pako,
ndipo unakupsereza,
ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi
pamaso pa anthu onse amene amakuona.
19 Anthu onse amitundu amene ankakudziwa
akuchita mantha chifukwa cha iwe.
Watheratu mochititsa mantha
ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”
Za Chilango cha Sidoni
20 Yehova anandiyankhula nati: 21 “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, 22 ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,
ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.
Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova
ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti
ndine woyera pakati pako.
23 Ndidzatumiza mliri pa iwe
ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.
Anthu ophedwa ndi lupanga
adzagwa mbali zonse.
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
24 “ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
25 “ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. 26 Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.
77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
2 Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
usiku ndinatambasula manja mosalekeza
ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.
3 Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
Sela
4 Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
5 Ndinaganizira za masiku akale,
zaka zamakedzana;
6 Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,
7 “Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
8 Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
9 Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”
10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”
13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
Sela
16 Madzi anakuonani Mulungu,
madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
mu mlengalenga munamveka mabingu;
mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.
20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.