M’Cheyne Bible Reading Plan
Sauli ndi Mfiti ya ku Endori
28 Mʼmasiku amenewo Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo kuti akamenyane ndi Aisraeli. Akisi anawuza Davide kuti, “Udziwe kuti iwe pamodzi ndi anthu ako mudzapita nane ku nkhondo.”
2 Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.”
Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.”
3 Nthawi imeneyi nʼkuti Samueli atamwalira, ndipo Aisraeli onse anamulira namuyika mʼmanda ku mzinda wake wa Rama. Sauli anali atachotsa mʼdzikomo anthu owombeza mawula ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa.
4 Tsono Afilisti anasonkhana nabwera kudzamanga misasa yawo ku Sunemu. Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kumanga misasa yawo ku Gilibowa. 5 Sauli ataona gulu lankhondo la Afilisti anaopa ndipo ananjenjemera kwambiri. 6 Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri. 7 Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, “Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye.”
Nduna zakezo zinamuyankha kuti, “Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori.”
8 Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.”
9 Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?”
10 Koma Sauli analonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Yehova wamoyo, iweyo sudzalangidwa chifukwa cha zimenezi.”
11 Kenaka mkaziyo anafunsa, “Ndikuyitanireni yani?”
Iye anati, “Undiyitanire Samueli.”
12 Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!”
13 Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?”
Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.”
14 Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?”
Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.”
Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.
15 Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?”
Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.”
16 Samueli anati, “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa ine, pakuti tsopano Yehova wakufulatira ndipo wasanduka mdani wako? 17 Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide. 18 Yehova wachita zimenezi lero chifukwa sunamvere mawu ake ndipo sunawawonongeretu Aamaleki. 19 Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.”
20 Nthawi yomweyo Sauli anagwa pansi atadzazidwa ndi mantha chifukwa cha mawu a Samueli. Analibenso mphamvu, pakuti sanadye tsiku lonse.
21 Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza. 22 Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.”
23 Iye anakana ndipo anati, “Ayi, ine sindidya.”
Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo anamuwumiriza, ndipo anawamvera. Choncho anadzuka pansi nakhala pa bedi.
24 Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti. 25 Tsono anapereka bulediyo kwa Sauli ndi nduna zake ndipo anadya. Pambuyo pake ananyamuka kupita kwawo usiku womwewo.
Paulo Chitsanzo cha Mtumiki wa Uthenga Wabwino
9 Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinamuone Ambuye athu Yesu? Kodi inu sindiye zotsatira za ntchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngakhale kwa ena sindingakhale mtumwi, mosakayika ndine mtumwi kwa inu! Poti inu ndi chizindikiro cha utumwi wanga mwa Ambuye.
3 Kwa iwo wofuna kundizenga milandu ndimawayankha kuti: 4 Kodi ife tilibe ulamuliro wakudya ndi kumwa? 5 Kodi ife tilibe ulamuliro wotenga mkazi wokhulupirira nʼkumayenda naye monga amachitira atumwi ena ndi abale awo a Ambuye ndiponso Kefa? 6 Kodi kapena ine ndekha ndi Barnaba ndiye tikuyenera kugwira ntchito kuti tipeze zotisowa?
7 Ndani angagwire ntchito ya usilikali namadzipezera yekha zofunika zonse? Kodi ndani amadzala mpesa koma wosadyako zipatso zake? Ndani amaweta nkhosa koma wosamwako mkaka wake? 8 Kodi moti zimene ndikunenazi ndimaganizo a umunthu chabe? Kodi Malamulo sakunena chimodzimodzinso? 9 Popeza analemba mʼMalamulo a Mose kuti, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.” Kodi pamene Mulungu ananena zimenezi ankalabadira za ngʼombe zokha? 10 Ndithu Iyeyo amanena za ifenso, kodi si choncho? Inde, izi anazilemba chifukwa cha ife, pakuti wolima ndiponso wopuntha, onsewo amagwira ntchito mwachiyembekezo chodzagawana zokololazo. 11 Ngati tidzala mbewu yauzimu pakati panu, kodi ndi chovuta kwambiri kuti tikolole zosowa zathu kuchokera kwa inu? 12 Ngati ena ali ndi ufulu wothandizidwa ndi inu, kodi ife sitikuyenera kukhala nawo ufulu ochulukirapo?
Koma ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewu. Mʼmalo mwake timangodzichitira chilichonse posafuna kutsekereza ena kumva Uthenga Wabwino wa Khristu.
13 Kodi simukudziwa kuti wogwira ntchito mʼNyumba ya Mulungu amapeza chakudya chawo mʼNyumbamo, ndipo kuti otumikira pa guwa lansembe amagawana zimene zaperekedwa pa guwa lansembelo. 14 Chomwechonso Ambuye akulamula kuti wolalikira Uthenga Wabwino azilandira thandizo lawo polalikira Uthenga Wabwinowo.
15 Koma ine sindinagwiritse ntchito ufulu woterewu. Sindikulemba izi ndi chiyembekezo choti mundichitire zoterezi. Kuli bwino ndife kusiyana nʼkuti wina alande zomwe ndimazinyadira. 16 Komatu ndikamalalikira Uthenga Wabwino, sindingadzitamandire popeza ndimawumirizidwa kulalikira. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino! 17 Ngati ndikugwira ntchitoyi mwakufuna kwanga, ndili ndi mphotho; koma ngati si mwakufuna kwanga, ndiye kuti ntchitoyi ndi Ambuye anandipatsa. 18 Tsono mphotho yanga ndi chiyani? Ndi iyi: kuti polalikira Uthenga Wabwino ndiwupereke kwaulere komanso kuti ndisagwiritse ntchito ufulu wanga polalikira uthengawo.
Ufulu wa Paulo
19 Ngakhale ndine mfulu ndipo sindine kapolo wa munthu, ndimadzisandutsa kapolo wa aliyense kuti ndikope ambiri mmene ndingathere. 20 Kwa Ayuda ndimakhala ngati Myuda kuti ndikope Ayuda. Kwa olamulidwa ndi Malamulo ndimakhala ngati wolamulidwa nawo (ngakhale kuti sindine wolamulidwa ndi Malamulowo) kuti ndikope amene amalamulidwa ndi Malamulo. 21 Kwa amene alibe Malamulo ndimakhala wopanda Malamulo (ngakhale kuti sindine wopanda Malamulo a Mulungu koma ndili pansi pa ulamuliro wa Khristu) kuti ndikope wopanda Malamulo. 22 Kwa ofowoka ndimakhala wofowoka, kuti ndikope ofowoka. Ndimachita zinthu zilizonse kwa anthu onse kuti mwanjira ina iliyonse ndipulumutse ena. 23 Ndimachita zonsezi chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndigawane nawo madalitso ake.
Kufunika kwa Kudziretsa
24 Kodi simukudziwa kuti pa mpikisano wa liwiro onse amathamanga ndithu, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Motero thamangani kuti mupate mphotho. 25 Aliyense wochita mpikisano amakonzekera mwamphamvu. Amachita izi kuti alandire mphotho yankhata yamaluwa yomwe imafota. Koma ife timachita izi kuti tilandire mphotho yosafota. 26 Choncho sindithamanga monga wothamanga wopanda cholinga; komanso sindichita mpikisano wankhonya monga munthu amene amangomenya mophonya. 27 Ine ndimazunza thupi langa ndi kulisandutsa kapolo kuti nditatha kulalikira ena, ineyo ndingadzapezeke wosayenera kulandira nawo mphotho.
Chimaliziro Chafika
7 Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:
“Chimaliziro! Chimaliziro chafika
ku ngodya zinayi za dziko.
3 Chimaliziro chili pa iwe tsopano.
Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.
Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
4 Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa
komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.
Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
5 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:
“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!
Taona chikubwera!
6 Chimaliziro chafika!
Chimaliziro chafika!
Chiwonongeko chakugwera.
Taona chafika!
7 Inu anthu okhala mʼdziko,
chiwonongeko chakugwerani.
Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
8 Ine ndili pafupi kukukwiyirani,
ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;
Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
9 Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako
ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’
10 “Taona, tsikulo!
Taona, lafika!
Chiwonongeko chako chabwera.
Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.
Kudzitama kwaphuka.
11 Chiwawa chasanduka ndodo
yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.
Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.
Palibiretu ndipo sipadzapezeka
munthu wowalira maliro.
12 Nthawi yafika!
Tsiku layandikira!
Munthu wogula asakondwere
ndipo wogulitsa asamve chisoni,
popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
13 Wogulitsa sadzazipezanso zinthu
zimene anagulitsa kwa wina
chinkana onse awiri akanali ndi moyo,
pakuti chilango chidzagwera onsewo
ndipo sichingasinthike.
Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense
amene adzapulumutsa moyo wake.
14 “Lipenga lalira,
ndipo zonse zakonzeka.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,
pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
15 Ku bwalo kuli kumenyana
ndipo mʼkati muli mliri ndi njala.
Anthu okhala ku midzi
adzafa ndi nkhondo.
Iwo okhala ku mizinda
adzafa ndi mliri ndi njala.
16 Onse amene adzapulumuka
ndi kumakakhala ku mapiri,
azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.
Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
17 Dzanja lililonse lidzalefuka,
ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
18 Iwo adzavala ziguduli
ndipo adzagwidwa ndi mantha.
Adzakhala ndi nkhope zamanyazi
ndipo mitu yawo adzameta mpala.
19 “Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu
ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.
Siliva ndi golide wawo
sizidzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,
kapena kukhala okhuta,
pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
20 Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka
ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.
Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa
kukhala zowanyansa.
21 Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.
Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda
ndi kudziyipitsa.
22 Ine ndidzawalekerera anthuwo
ndipo adzayipitsa malo anga apamtima.
Adzalowamo ngati mbala
ndi kuyipitsamo.
23 “Konzani maunyolo,
chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo
ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
24 Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa
kuti idzalande nyumba zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu
pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
25 Nkhawa ikadzawafikira
adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
26 Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,
ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.
Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.
Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,
ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
27 Mfumu idzalira,
kalonga adzagwidwa ndi mantha.
Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.
Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,
ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.
45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2 Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
3 Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu;
mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
4 Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso
mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo;
dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
5 Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu,
mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.