M’Cheyne Bible Reading Plan
Natani Adzudzula Davide
12 Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. 2 Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, 3 koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo.
4 “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.”
5 Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! 6 Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”
7 Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli. 8 Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri. 9 Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. 10 Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’
11 “Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. 12 Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ”
13 Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.”
Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi. 14 Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.”
15 Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. 16 Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse. 17 Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo.
18 Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.”
19 Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?”
Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.”
20 Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya.
21 Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!”
22 Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’ 23 Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.”
24 Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye. 25 Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya.
26 Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. 27 Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. 28 Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.”
29 Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. 30 Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, 31 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu.
Matupi Atsopano
5 Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. 2 Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, 3 chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. 4 Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. 5 Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.
6 Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. 7 Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. 8 Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. 9 Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. 10 Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
Ntchito Yoyanjanitsa
11 Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. 12 Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. 13 Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. 14 Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. 15 Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.
16 Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17 Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18 Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19 Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20 Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21 Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.
Nyimbo ya Maliro a Akalonga a Israeli
19 “Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli. 2 Uzinena kuti,
“ ‘Amayi ako anali ndani?
Anali ngati mkango waukazi!
Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna;
unkalera ana ake pakati pa misona.
3 Unalera mmodzi mwa ana ake,
ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu.
Unaphunzira kugwira nyama,
ndipo unayamba kudya anthu.
4 Anthu amitundu anamva za mkangowo,
ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo.
Iwo anawukoka ndi ngowe
kupita nawo ku dziko la Igupto.
5 “ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera,
amayiwo anatenganso mwana wina
namusandutsa mkango wamphamvu.
6 Unkayendayenda pakati pa mikango inzake,
pakuti tsopano unali mkango wamphamvu.
Unaphunzira kugwira nyama
ndipo unayamba kudya anthu.
7 Unagwetsa malinga awo,
ndikuwononga mizinda yawo.
Onse a mʼdzikomo
anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.
8 Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira,
inabwera kudzalimbana nawo.
Anawutchera ukonde wawo,
ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.
9 Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga.
Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni
ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende
ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso
ku mapiri a Israeli.
10 “ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa
wodzalidwa mʼmbali mwa madzi.
Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri
chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.
11 Nthambi zake zinali zolimba,
zoyenera kupangira ndodo yaufumu.
Unatalika nusomphoka pakati pa
zomera zina.
Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake,
ndi nthambi zake zambiri.
12 Koma unazulidwa mwaukali
ndipo unagwetsedwa pansi.
Unawuma ndi mphepo ya kummawa,
zipatso zake zinayoyoka;
nthambi zake zolimba zinafota
ndipo moto unapsereza mtengo wonse.
13 Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu,
dziko lowuma ndi lopanda madzi.
14 Moto unatulukanso mu mtengomo
ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake.
Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo
yoyenera kupangira ndodo yaufumu.
Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
64 Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga;
tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani.
2 Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa,
ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa.
3 Iwo amanola malilime awo ngati malupanga,
amaponya mawu awo olasa ngati mivi.
4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa;
amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.
5 Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa,
amayankhula zobisa misampha yawo;
ndipo amati, “Adzayiona ndani?”
6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati,
“Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!”
Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi;
mwadzidzidzi adzakanthidwa.
8 Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa
ndi kuwasandutsa bwinja;
onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza.
9 Anthu onse adzachita mantha;
adzalengeza ntchito za Mulungu
ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita.
10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehova
ndi kubisala mwa Iye,
owongoka mtima onse atamande Iye!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo.
65 Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni;
kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
2 Inu amene mumamva pemphero,
kwa inu anthu onse adzafika.
3 Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,
Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
4 Odala iwo amene inu muwasankha
ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!
Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,
za mʼNyumba yanu yoyera.
5 Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,
Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi
ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
6 amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,
mutadziveka nokha ndi mphamvu.
7 Amene munakhalitsa bata nyanja
kukokoma kwa mafunde ake,
ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
8 Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;
kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.
Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
9 Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;
Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.
Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi
kuti upereke tirigu kwa anthu,
pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10 Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,
mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11 Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,
ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12 Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;
mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13 Madambo akutidwa ndi zoweta
ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu;
izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.