Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Samueli 27

Davide Pakati pa Afilisti

27 Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.”

Choncho Davide ndi anthu 600 amene anali nawo anachoka napita kwa Akisi mwana wa Maoki mfumu ya ku Gati. Davide anakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi ankhondo ake, aliyense ndi banja lake. Davide ali ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wamasiye wa Nabala. Sauli anamva kuti Davide wathawira ku Gati, ndipo sanamufunefunenso.

Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?”

Choncho tsiku limenelo Akisi anamupatsa Zikilagi ndipo mzindawo wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero. Davide anakhala mʼdziko la Afilisti kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi.

Tsono Davide ndi anthu ake ankapita kukathira nkhondo Agesuri, Agirizi ndi Aamaleki. (Mitundu ya anthu imeneyi kuyambira kale inkakhala mʼdziko la pakati pa Suri ndi Igupto). Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi.

10 Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.” 11 Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi wamoyo kuti akafotokozere anthu a ku Gati zochitikazo kuopa kuti opulumukawo akhoza kudzanena kuti “Davide watichita zakutizakuti.” Tsono izi ndi zimene Davide ankachita pamene ankakhala mʼdziko la Afilisti. 12 Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.”

1 Akorinto 8

Nyama ya Nsembe za Mafano

Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa. Munthu amene amaganiza kuti amadziwa kanthu, ndiye kuti sakudziwa monga mmene amayenera kudziwira. Koma munthu amene amakonda Mulungu amadziwika ndi Mulunguyo.

Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha. Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri), koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.

Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi. Koma chakudya sichitisendeza kufupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya si vuto, tikadya sitisinthikanso.

Komabe samalani kuti ufulu wanu ochita zinthu usafike pokhumudwitsa ofowoka. 10 Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano? 11 Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu. 12 Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu. 13 Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse.

Ezekieli 6

Uneneri Wotsutsa Mapiri a Israeli

Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku mapiri a Israeli; yankhula nawo modzudzula kuti, ‘Inu mapiri a ku Israeli, imvani mawu a Ambuye Yehova. Iye akuwuza mapiri, magomo, mitsinje ndi zigwa kuti: Ine ndizakuthirani nkhondo ndipo ndidzawononga nyumba zanu mʼmene mukupembedzeramo mafano. Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu. Ine ndidzagoneka mitembo ya Aisraeli pamaso pa mafano awo, ndipo ndidzamwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu ansembe. Konse kumene mumakhala, mizinda yanu idzasanduka bwinja. Nyumba zanu zopembedzera mafano zidzagumulidwa kotero kuti maguwa anu adzawonongedwa ndi kusakazidwa, mafano anu adzaphwanyidwa ndi kuwonongedwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa pansi ndipo zonse zimene munapanga zidzatheratu. Anthu anu adzaphedwa pakati panu, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’

“Komabe ndidzasiya ena pangʼono opulumuka ku nkhondo. Iwowa ndidzawamwazira ku mayiko ena pakati pa anthu a mitundu ina. Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata. 10 Ndipo iwo adzadziwa kuti ndine Yehova ndi kuti sindinkawaopseza chabe pamene ndinanena kuti ndidzawawononga.

11 “Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri. 12 Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo. 13 Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse. 14 Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Masalimo 44

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

44 Ife tamva ndi makutu athu, Inu Mulungu;
    makolo athu atiwuza
zimene munachita mʼmasiku awo,
    masiku akalekalewo.
Ndi dzanja lanu munathamangitsa mitundu ya anthu ena
    ndi kudzala makolo athu;
Inu munakantha mitundu ya anthu,
    koma makolo athuwo Inu munawapatsa ufulu.
Sanalande dziko ndi lupanga lawo,
    si mkono wawo umene unawabweretsera chigonjetso,
koma ndi dzanja lanu lamanja, mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,
    pakuti munawakonda.

Inu ndinu Mfumu yanga ndi Mulungu wanga
    amene mumalamulira chigonjetso cha Yakobo.
Kudzera kwa inu ife timabweza adani athu;
    kudzera mʼdzina lanu timapondereza otiwukirawo.
Sindidalira uta wanga,
    lupanga langa silindibweretsera chigonjetso;
koma Inu mumatigonjetsera adani athu,
    mumachititsa manyazi amene amadana nafe.
Timanyadira mwa Mulungu wathu tsiku lonse,
    ndipo tidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.

Koma tsopano mwatikana ndi kutichepetsa;
    Inu simupitanso ndi ankhondo athu.
10 Munachititsa ife kubwerera mʼmbuyo pamaso pa mdani
    ndipo amene amadana nafe atilanda katundu.
11 Inu munatipereka kuti tiwonongedwe monga nkhosa
    ndipo mwatibalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina.
12 Inu munagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika,
    osapindulapo kanthu pa malondawo.

13 Mwachititsa kuti tikhale chochititsa manyazi kwa anthu a mitundu ina,
    chonyozeka ndi chothetsa nzeru kwa iwo amene atizungulira.
14 Mwachititsa kuti tikhale onyozeka pakati pa anthu a mitundu ina;
    anthu amapukusa mitu yawo akationa.
15 Manyazi anga ali pamaso panga tsiku lonse
    ndipo nkhope yanga yaphimbidwa ndi manyazi
16 chifukwa cha mawu otonza a iwo amene amandinyoza ndi kundichita chipongwe,
    chifukwa cha mdani amene watsimikiza kubwezera.

17 Zonsezi zinatichitikira
    ngakhale kuti ifeyo sitinayiwale Inu
    kapena kuonetsa kusakhulupirika pa pangano lanu.
18 Mitima yathu sinabwerere mʼmbuyo;
    mapazi athu sanatayike pa njira yanu.
19 Koma Inu mwatiphwanya ndi kuchititsa kuti tikhale ozunzidwa ndi ankhandwe
    ndipo mwatiphimba ndi mdima waukulu.

20 Tikanayiwala dzina la Mulungu wathu
    kapena kutambasulira manja athu kwa mulungu wachilendo,
21 kodi Mulungu wathu sakanazidziwa zimenezi,
    pakuti Iye amadziwa zinsinsi zamumtima?
22 Komabe chifukwa cha Inu timakumana ndi imfa tsiku lonse,
    tili ngati nkhosa zoyenera kuti ziphedwe.

23 Dzukani Ambuye! Nʼchifukwa chiyani mukugona!
    Dziwutseni nokha! Musatikane kwamuyaya.
24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu,
    ndi kuyiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?

25 Tatsitsidwa pansi mpaka pa fumbi;
    matupi athu amatirira pa dothi.
26 Imirirani ndi kutithandiza,
    tiwomboleni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.