M’Cheyne Bible Reading Plan
Davide agonjetsa Aamoni
10 Patapita nthawi, mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.
Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni, 3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” 4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anameta munthu aliyense mbali imodzi ya ndevu zake, ndi kudula zovala zake pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera, ndipo anawabweza kwawo.
5 Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”
6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.
7 Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. 8 Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene Aaramu a ku Aramu-Zoba ndi Rehobu ndi ankhondo a ku Tobu ndi Maaka anali kwa wokha ku malo wopanda mitengo.
9 Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 10 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 11 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 12 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”
13 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 14 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
15 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anasonkhananso. 16 Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri.
17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. 18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo. 19 Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo.
Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.
Akhristu ndi Kalata Yochokera kwa Khristu
3 Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? 2 Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. 3 Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.
4 Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. 5 Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. 6 Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.
Ulemerero wa Pangano Latsopano
7 Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, 8 kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? 9 Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo! 10 Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo. 11 Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!
12 Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri. 13 Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala. 14 Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha. 15 Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo. 16 Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.” 17 Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu. 18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.
Fanizo la Ziwombankhanga Ziwiri ndi Mtengo Wamphesa
17 Yehova anayankhula nane kuti, 2 “Iwe mwana wa munthu, aphere mwambi anthu a Israeli ndi kuwawuza fanizo. 3 Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza. 4 Chinabudula msonga yeniyeni ya nthambiyo nʼkupita nayo ku dziko lamalonda ndipo anakayika mu mzinda wa anthu amalonda.
5 “ ‘Kenaka chinatenga mbewu ina ya mʼdziko ndi kukayidzala ku malo a chonde kumene kunali madzi ambiri. Anayidzala ngati mmene amadzalira mtengo wa msondozi. 6 Ndipo inaphuka nisanduka mtengo wa mpesa wotambalala chamʼmunsi. Nthambi zake zinaloza mmwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake inalowa pansi. Kotero unakhala mtengo wamphesa ndipo unasanduka wa nthambi ndiponso wa masamba ambiri.
7 “ ‘Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu, cha mapiko amphamvu ndi cha nthenga zambiri. Tsopano mtengo wamphesa uja unakhotetsera mizu yake kwa chiwombankhangacho kuchokera pa malo amene unadzalidwa ndipo unatambalitsa nthambi zake kwa chiwombankhangacho kufuna kuthiridwa madzi. 8 Koma mtengowo unadzalidwa kale pa nthaka yabwino mʼmbali mwa madzi kuti ukhale ndi nthambi zambiri, ubereke zipatso ndi kukhala wokongola.’
9 “Ukawawuze Aisraeli kuti, ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Kodi udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzawuzula mizu ndi kubudula nthambi zake kuti ufote? Masamba ake onse anthete adzafota. Sipadzafunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti awuzule. 10 Ngakhale utawokedwa pena, kodi udzaphuka? Kodi sudzafoteratu mphepo ya kummawa ikadzawomba, kufotera pa malo pamene anawuwokerapo?’ ”
11 Kenaka Yehova anandiyankhula nati: 12 “Tawafunsa anthu owukirawa kuti, ‘kodi mukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Uwafotokozere kuti, ‘Mfumu ya Babuloni inapita ku Yerusalemu ndikukatengako mfumu ndi anthu ake otchuka ndi kubwera nawo ku Babuloni. 13 Ndipo anatenga mmodzi wa banja laufumu ndi kuchita naye mgwirizano, ndipo anamulumbiritsa kuti akhale womvera. Inatenganso akulu onse a mʼdzikomo 14 kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzaphukenso, koma kuti ukhalepobe posunga pangano limene unachita. 15 Koma mfumu inawukira mfumu ya ku Babuloni potumiza nthumwi ku dziko la Igupto kukatenga akavalo ndi gulu lalikulu la nkhondo. Kodi mfumu yotereyi ingapambane? Kodi wochita zinthu zoterezi angapulumuke? Kodi angaphwanye mgwirizano ndi kupulumuka?
16 “ ‘Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, mfumuyo idzafera ku Babuloni, mʼdziko la mfumu imene inayika pa mpando waufumu. Inapeputsa lumbiro lake nʼkuphwanya pangano limene inachita ndi mfumu inayo. 17 Farao ndi gulu lake lankhondo lamphamvu sadzatha kumuthandiza pa nkhondo, pamene mfumu ya Babuloni idzapanga mitumbira ya nkhondo ndi nsanja za nkhondo kuti iwononge miyoyo yambiri. 18 Mfumu ya ku Yuda inanyoza lumbiro lake pophwanya pangano. Inalonjeza komabe sinatsatire malonjezo ake. Choncho sidzapulumuka.
19 “ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndithu pali Ine wamoyo, Ine ndidzalanga mfumu imeneyi chifukwa inanyoza lumbiro langa, ndi kuphwanya pangano langa. 20 Ndidzayitchera ukonde ndipo idzakodwa mu msampha wanga. Ndidzapita nayo ku Babuloni ndi kuyilanga kumeneko chifukwa inali yosakhulupirika kwa Ine. 21 Asilikali ake onse amene akuthawa adzaphedwa ndi lupanga, ndipo opulumuka adzabalalitsidwa ku mbali zonse. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova ndayankhula.
22 “ ‘Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndidzatenga nthambi pamwamba penipeni pa mkungudza ndi kuyidzala; ndidzathyola nthambi yanthete kuchokera pa nthambi zapamwamba penipeni ndi kuyidzala pamwamba pa phiri lalitali. 23 Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake. 24 Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma.
“ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.
60 Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.
Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
2 Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,
konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
3 Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;
inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.
4 Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera
kuti tisonkhanireko pothawa uta.
5 Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja,
kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
6 Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
“Mwakupambana ndidzagawa Sekemu
ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
7 Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
8 Mowabu ndi mbale yanga yosambira,
pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga,
pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”
9 Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa?
Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife
ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu,
pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano
ndipo tidzapondaponda adani athu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.
61 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;
mvetserani pemphero langa.
2 Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu
ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;
tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
3 Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,
nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.
4 Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya
ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
5 Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;
mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.
6 Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,
zaka zake kwa mibado yochuluka.
7 Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;
ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.
8 Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu
ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.