Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 11

Davide ndi Batiseba

11 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.

Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”

Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.

10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”

11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”

12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. 13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.

14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. 15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.”

16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. 17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.

18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. 19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, 20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? 21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ”

22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. 23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. 24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”

25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”

26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. 27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.

2 Akorinto 4

Chuma Chosungidwa Mʼmbiya Zadothi

Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima. Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake. Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika. Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu. Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.

Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife. Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka. 10 Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu. 11 Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa. 12 Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.

13 Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula, 14 chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake. 15 Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.

16 Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. 17 Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. 18 Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.

Ezekieli 18

Munthu Wochimwa Adzafa

18 Yehova anandiyankhula nati: “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:

“ ‘Nkhuyu zodya akulu zimapota
    ndi ana omwe?’ ”

“Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.

“Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama
    amene amachita zolungama ndi zolondola.
Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo
    kapena kupembedza mafano a Aisraeli.
Iye sayipitsa mkazi wa mnzake
    kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
Iye sapondereza munthu wina aliyense,
    koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.
Iye salanda zinthu za osauka,
    koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,
    ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,
    kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.
Amadziletsa kuchita zoyipa
    ndipo sakondera poweruza milandu.
Iye amatsatira malangizo anga,
    ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.
Munthu ameneyo ndi wolungama;
    iye adzakhala ndithu ndi moyo,
            akutero Ambuye Yehova.

10 “Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. 11 Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.

“Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.
Amayipitsa mkazi wa mnzake.
12 Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.
Amalanda zinthu za osauka.
Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.
Iye amatembenukira ku mafano
nachita zonyansa.
13 Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.

Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.

14 “Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.

15 “Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.
    Sapembedza mafano a ku Israeli.
Sayipitsa mkazi wa mnzake.
16 Sapondereza munthu wina aliyense.
    Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.
Salanda zinthu za munthu.
    Amapereka chakudya kwa anthu anjala.
    Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
17 Amadziletsa kuchita zoyipa.
    Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.
Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.

Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. 18 Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.

19 “Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. 20 Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.

21 “ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. 22 Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. 23 Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.

24 “ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.

25 “Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? 26 Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. 27 Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. 28 Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. 29 Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?

30 “Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. 31 Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? 32 Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”

Masalimo 62-63

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.

62 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;
    chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
    Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.

Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?
    Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,
    ngati mpanda wogwedezeka?
Iwo akufunitsitsa kumugwetsa
    kuti achoke pa malo ake apamwamba.
    Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.
Ndi pakamwa pawo amadalitsa
    koma mʼmitima yawo amatemberera.

Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
    chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
    Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
    Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
    khuthulani mitima yanu kwa Iye,
    pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
            Sela

Anthu wamba ndi mpweya chabe;
    anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
    iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
    kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
    musayike mtima wanu pa icho.

11 Mulungu wayankhula kamodzi,
    ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12     komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
    molingana ndi ntchito zake.

Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.

63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
    moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
    thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
    kumene kulibe madzi.

Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
    ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
Chifukwa chikondi chanu
    ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
    ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
    Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.

Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
    ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
Chifukwa ndinu thandizo langa,
    ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
Moyo wanga umakangamira Inu;
    dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.

Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;
    adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga
    ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.

11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
    onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
    koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.