Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
2 Samueli 22

Nyimbo ya Mayamiko ya Davide

22 Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. Iye anati,

“Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga.
    Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo,
    chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa.
Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga.
    Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

“Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
    ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

“Mafunde a imfa anandizinga;
    mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
    misampha ya imfa inalimbana nane.

“Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
    ndinapemphera kwa Mulungu wanga.
Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga;
    kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.

“Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi,
    maziko a miyamba anagwedezeka;
    ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi;
    moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake,
    makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
10 Iye anangʼamba thambo natsika pansi;
    pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda.
11 Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka;
    nawuluka ndi mphepo mwaliwiro.
12 Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake,
    mitambo yakuda ya mlengalenga.
13 Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake
    munkachokera makala amoto alawilawi.
14 Yehova anabangula kumwamba ngati bingu,
    mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse.
15 Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake,
    ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa.
16 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera,
    ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera,
Yehova atabangula mwaukali,
    pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.

17 “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira;
    anandivuwula mʼmadzi ozama.
18 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,
    adani anga amene anali amphamvu kuposa ine.
19 Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto,
    koma Yehova anali thandizo langa.
20 Iye anandipititsa kumalo otakasuka;
    anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

21 “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa;
    molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa.
22 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova;
    ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga.
23 Malamulo ake onse ali pamaso panga,
    sindinasiye malangizo ake.
24 Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake
    ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo.
25 Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa,
    molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake.

26 “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu,
    kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino,
27 Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu,
    koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo.
28 Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa,
    koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa.
29 Inu Yehova, ndinu nyale yanga;
    Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika.
30 Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo,
    ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu.

31 “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro;
    mawu a Yehova alibe cholakwika.
Iye ndi chishango
    kwa onse amene amathawira kwa iye.
32 Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova?
    Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu?
33 Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu
    ndi kulungamitsa njira yanga.
34 Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi;
    Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri.
35 Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo;
    manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo.
36 Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso;
    mumawerama kuti mundikweze.
37 Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino,
    kuti mapazi anga asaterereke.

38 “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha;
    sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa.
39 Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso;
    Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.
40 Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo;
    munagwaditsa adani anga pa mapazi anga.
41 Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa;
    ndipo ndinawononga adani anga.
42 Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa.
    Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe.
43 Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi;
    ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu.

44 “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu;
    Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
45     Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
    akangomva za ine, amandigonjera.
46 Iwo onse anataya mtima;
    anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.

47 “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa.
    Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga!
48 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
    amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga,
49     amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
    munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
50 Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina;
    ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.

51 “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake,
    amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake,
    kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”

Agalatiya 2

Atumwi Alandira Paulo

Kenaka, patatha zaka khumi ndi zinayi, ndinapitanso ku Yerusalemu, nthawi iyi ndinapita ndi Barnaba. Ndinatenganso Tito kuti apite nafe. Ine ndinapita chifukwa Mulungu anachita kundionetsera kuti ndipite ndipo ndinakakumana ndi atsogoleri mu msonkhano mwamseri ndi kuwafotokozera Uthenga Wabwino umene ndimalalikira pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinachita zimenezi kuti ndikhale ndi chitsimikizo kuopa kuti mwina ndinathamanga kapena ndimathamanga liwiro pachabe. Komatu ngakhale Tito, amene anali nane sanakakamizidwe kuti achite mdulidwe, ngakhale iyeyo anali Mgriki. Nkhani iyi inayambika chifukwa abale ena achinyengo amene analowerera pakati pathu kuti adzaone za ufulu umene tili nawo mwa Khristu Yesu ndikuti atisandutse akapolo. Ife sitinawagonjere ndi pangʼono pomwe, nʼcholinga chakuti choonadi cha Uthenga Wabwino chikhalebe ndi ife.

Koma kunena za aja ankaoneka ngati ofunika kwambiri, chimene iwo anali sichisintha kanthu kwa ine; chifukwa Mulungu alibe tsankho, iwowo sanawonjezepo kanthu pa uthenga wanga. Makamaka anaona kuti ine ndinapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa anthu a mitundu ina monga momwe Petro anapatsidwa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino kwa Ayuda. Pakuti Mulungu, amene amagwira ntchito mu utumiki wa Petro monga mtumwi kwa Ayuda, amagwiranso ntchito mu utumiki wanga monga mtumiki kwa anthu a mitundu ina. Yakobo, Petro ndi Yohane, amene ankatengedwa ngati mizati, atazindikira chisomo chimene chinapatsidwa kwa ine, anagwirana chanza ndi ine ndi Barnaba kusonyeza chiyanjano chathu. Iwo anavomereza kuti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa Ayuda. 10 Chimene iwo anapempha ndi chakuti ife tipitirize kukumbukira osauka, chinthu chimene ine ndinali okonzeka kuchichita.

Paulo Adzudzula Petro

11 Petro atafika ku Antiokeya, ine ndinamudzudzula pa gulu chifukwa anapezeka wolakwa. 12 Pakuti asanafike anthu otumidwa ndi Yakobo, iye ankadya pamodzi ndi anthu a mitundu ina. Koma atafika, iyeyo anachoka pakati pa anthuwo nakakhala pa yekha chifukwa ankaopa anthu a mʼgulu la mdulidwe. 13 Ayuda enanso anamutsata pochita zachinyengozi, kotero kuti ngakhale Barnaba anasocheretsedwa chifukwa cha chinyengo chawocho.

14 Koma nditaona kuti iwo sankachita molingana ndi choonadi cha Uthenga Wabwino, ndinawuza Petro pamaso pa anthu onse kuti, “Iwe ndiwe Myuda koma ukukhala ngati munthu wa mtundu wina, osati Myuda. Nanga nʼchifukwa chiyani ukukakamiza anthu a mitundu ina kuti akhale ngati Ayuda?

15 “Ife amene ndife Ayuda mwachibadwa, osati anthu a mitundu ina ochimwa, 16 tikudziwa kuti munthu salungamitsidwa pochita ntchito za lamulo koma ndi chikhulupiriro mwa Yesu Khristu. Chomwecho, ifenso tinakhulupirira Khristu Yesu kuti tilungamitsidwe mwachikhulupiriro mwa Khristu ndipo osati pochita ntchito za lamulo, chifukwa palibe amene adzalungamitsidwa pochita ntchito za lamulo.

17 “Tsono ngati ife, pamene tikufuna kulungamitsidwa mwa Khristu, zikuonekeratu poyera kuti ndifenso ochimwa, kodi zikutanthauza kuti Khristu amalimbikitsa uchimo? Ayi. Nʼkosatheka! 18 Ngati ine ndimanganso chimene ndinachigumula, ndikuonetsa kuti ndine wophwanya lamulo.

19 “Pakuti pamene ndinayesera kutsatira lamulo, lamulolo linandionetsa kuti ndine wochimwa. Choncho ndinasiya kutsatira lamulo kuti ndikhale ndi moyo kwa Mulungu. 20 Ndinapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano mʼthupi lino, ndi moyo mwachikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu, amene anandikonda nadzipereka yekha chifukwa cha ine. 21 Ine sindikukankhira kumbali chisomo cha Mulungu, chifukwa ngati chilungamo chikanapezeka pochita ntchito za lamulo, ndiye kuti Khristu anafa pachabe.”

Ezekieli 29

Za Chilango cha Igupto

29 Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
    iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
    ndinadzipangira ndekha.’
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
    ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
    pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
Ndidzakutaya ku chipululu,
    iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
    popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
    cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.

Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.

“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10 nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11 Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12 Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.

13 “ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14 Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15 Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16 Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”

Mphotho ya Nebukadinezara

17 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19 Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20 Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.

21 “Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Masalimo 78:1-37

Ndakatulo ya Asafu.

78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
    mvetserani mawu a pakamwa panga.
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
    ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
    zimene makolo athu anatiwuza.
Sitidzabisira ana awo,
    tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
    mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo
    ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,
zimene analamulira makolo athu
    kuphunzitsa ana awo,
kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,
    ngakhale ana amene sanabadwe,
    ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu
    ndipo sadzayiwala ntchito zake
    koma adzasunga malamulo ake.
Iwo asadzakhale monga makolo awo,
    mʼbado wosamvera ndi wowukira,
umene mitima yake inali yosamvera Mulungu,
    umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.

Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,
    anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
10 iwo sanasunge pangano la Mulungu
    ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
11 Anayiwala zimene Iye anachita,
    zozizwitsa zimene anawaonetsa.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
    mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
    Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
    ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
    ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
    ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.

17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
    kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala
    pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
    “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe
    madzi anatuluka,
    ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.
Koma iye angatipatsenso ife chakudya?
    Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri;
    moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo,
    ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu
    kapena kudalira chipulumutso chake.
23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba
    ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
24 anagwetsa mana kuti anthu adye,
    anawapatsa tirigu wakumwamba.
25 Anthu anadya buledi wa angelo,
    Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,
    ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,
    mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,
    kuzungulira matenti awo onse.
29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka
    pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,
    chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira;
    Iye anapha amphamvu onse pakati pawo,
    kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.

32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;
    ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.
    Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;
    iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,
    kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,
    kumunamiza ndi malilime awo;
37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,
    iwo sanakhulupirike ku pangano lake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.