Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Hoseya 1:2-10

Mkazi wa Hoseya ndi Ana Ake

Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.

Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli. Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”

Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”

Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna. Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.

10 “Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’

Masalimo 85

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

85 Yehova munakomera mtima dziko lanu;
    munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
Munakhululukira mphulupulu za anthu anu
    ndi kuphimba machimo awo onse.
            Sela
Munayika pambali ukali wanu wonse
    ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.

Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
    ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
    Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
Kodi simudzatitsitsimutsanso,
    kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova,
    ndipo tipatseni chipulumutso chanu.

Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;
    Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,
    koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,
    kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;
    chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,
    ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,
    ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
13 Wolungama amapita patsogolo pake
    ndi kukonza njira za mapazi ake.

Akolose 2:6-15

Za Moyo Weniweni mwa Khristu

Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.

Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.

Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. 10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. 11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. 12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.

13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. 14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. 15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.

Akolose 2:16-19

Ufulu Wathu

16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. 17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. 18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. 19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.

Luka 11:1-13

Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera

11 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”

Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti:

“ ‘Atate,
dzina lanu lilemekezedwe,
ufumu wanu ubwere.
Mutipatse chakudya chathu chalero,
mutikhululukire machimo athu,
    monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.
Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”

Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’

“Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.

“Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

11 “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.