Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:17-32

Gimeli

17 Chitirani zokoma mtumiki wanu, ndipo ndidzakhala ndi moyo;
    kuti tsono ndisunge mawu anu.
18 Tsekulani maso anga kuti ndithe kuona
    zinthu zodabwitsa mʼmalamulo anu.
19 Ine ndine mlendo pa dziko lapansi;
    musandibisire malamulo anu.
20 Moyo wanga wafowoka polakalaka
    malamulo anu nthawi zonse.
21 Inu mumadzudzula onyada, otembereredwa,
    amene achoka pa malamulo anu.
22 Mundichotsere chitonzo ndi mnyozo
    pakuti ndimasunga malamulo anu.
23 Ngakhale mafumu akhale pamodzi kundinyoza,
    mtumiki wanu adzalingalirabe zophunzitsa zanu.
24 Malamulo anu amandikondweretsa;
    ndiwo amene amandilangiza.

Daleti

25 Moyo wanga wakangamira fumbi;
    tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.
26 Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha;
    phunzitseni malamulo anu.
27 Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu;
    pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.
28 Moyo wanga wafowoka ndi chisoni;
    limbikitseni monga mwa mawu anu.
29 Mundichotse mʼnjira zachinyengo;
    mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
30 Ndasankha njira ya choonadi;
    ndayika malamulo anu pa mtima panga.
31 Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova;
    musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
32 Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu,
    pakuti Inu mwamasula mtima wanga.

Amosi 7:1-6

Dzombe, Moto ndi Chingwe Chowongolera Khoma

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

Kotero Yehova anakhululuka.

Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.”

Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”

Kotero Yehova anakhululuka.

Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.”

Akolose 1:27-2:7

27 Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.

28 Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu. 29 Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.

Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.

Za Moyo Weniweni mwa Khristu

Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.