Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
7 Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. 8 Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?”
Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.”
Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso.
9 “Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa
ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja;
ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.”
Amosi ndi Amaziya
10 Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. 11 Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi:
“ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga,
ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo,
kutali ndi dziko lake.’ ”
12 Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. 13 Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.”
14 Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. 15 Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ 16 Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti,
“ ‘Usanenere zotsutsa Israeli,
ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”
17 “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi:
“ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu,
ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga.
Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa,
ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu.
Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo,
kutali ndi dziko lake.’ ”
Salimo la Asafu.
82 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;
Iye akuweruza pakati pa “milungu.”
2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti,
ndi kukondera anthu oyipa?
3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;
apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.
5 “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.
Amayendayenda mu mdima;
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,
nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
7 Koma mudzafa ngati anthu wamba;
mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”
8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mʼbale wathu.
2 Kulembera abale oyera mtima ndi okhulupirira a ku Kolose mwa Khristu.
Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu.
Kuyamika ndi Pemphero
3 Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani. 4 Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse. 5 Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino 6 umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse. 7 Inu munaphunzira zimenezi kuchokera kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwathu. 8 Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.
9 Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa. 10 Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu. 11 Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe 12 ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika. 13 Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
Fanizo la Msamariya Wachifundo
25 Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”
26 Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”
27 Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”
28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”
29 Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”
30 Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31 Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32 Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33 Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34 Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35 Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’
36 “Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”
37 Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”
Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.