Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Dengu la Zipatso Zakupsa
8 Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa. 2 Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?”
Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.”
Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.
3 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”
4 Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa
ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.
5 Mumanena kuti,
“Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti
kuti tigulitse zinthu?
Ndipo tsiku la Sabata litha liti
kuti tigulitse tirigu,
kuti tichepetse miyeso,
kukweza mitengo
kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
6 tigule osauka ndi ndalama zasiliva
ndi osowa powapatsa nsapato,
tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”
7 Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.
8 “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi,
ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni?
Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo;
lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata
ngati mtsinje wa ku Igupto.
9 “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzadetsa dzuwa masana
ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10 Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni
ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro.
Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu
ndi kumeta mipala mitu yanu.
Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo,
ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
11 “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti,
“Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse;
osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi,
koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12 Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina.
Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa,
kufunafuna mawu a Yehova,
koma sadzawapeza.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.”
52 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?
Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,
iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;
lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,
ntchito yako nʼkunyenga.
3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.
Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona.
Sela
4 Umakonda mawu onse opweteka,
iwe lilime lachinyengo!
5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:
iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;
iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;
adzamuseka nʼkumanena kuti,
7 “Pano tsopano pali munthu
amene sanayese Mulungu linga lake,
koma anakhulupirira chuma chake chambiri
nalimbika kuchita zoyipa!”
8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi
wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;
ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu
kwa nthawi za nthawi.
9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;
chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera
pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.
Kupambana Koposa kwa Khristu
15 Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. 16 Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. 17 Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. 18 Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. 19 Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu. 20 Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.
21 Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. 22 Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho 23 ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
Utumiki wa Paulo ku Mpingo
24 Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo. 25 Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu, 26 chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. 27 Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.
28 Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu.
Marita ndi Mariya
38 Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. 39 Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. 40 Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!”
41 Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri, 42 koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.