Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 67

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo.

67 Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa,
    achititse kuti nkhope yake itiwalire.
Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi,
    chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse.

Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.
Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe,
    pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo
    ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi.
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu;
    mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

Nthaka yabereka zokolola zake;
    tidalitseni Mulungu wathu.
Mulungu atidalitse
    kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

Miyambo 2:6-8

Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,
    ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.
Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.
    Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,
pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.
    Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.

Machitidwe a Atumwi 16:1-8

Timoteyo Atsagana ndi Paulo ndi Sila

16 Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki. Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino. Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki. Pamene amayenda mzinda ndi mzinda, amafotokoza zimene atumwi ndi akulu ampingo ku Yerusalemu anagwirizana kuti anthu azitsatire. Kotero mipingo inalimbikitsidwa mʼchikhulupiriro ndipo anthu amachulukirachulukirabe tsiku ndi tsiku.

Paulo Awona Masomphenya

Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya. Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero. Ndipo iwo anadutsa Musiya ndipo anapita ku Trowa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.