Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 102:1-17

Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.

102 Yehova imvani pemphero langa;
    kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
Musandibisire nkhope yanu
    pamene ndili pa msautso.
Munditcherere khutu;
    pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;
    mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;
    ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula
    ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,
    monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
Ndimagona osapeza tulo; ndakhala
    ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;
    iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa
    ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu,
    popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;
    Ine ndikufota ngati udzu.

12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;
    kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni
    pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;
    nthawi yoyikika yafika.
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;
    fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,
    mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni
    ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;
    sadzanyoza kupempha kwawo.

Yeremiya 25:15-32

Chikho cha Ukali wa Mulungu

15 Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma. 16 Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”

17 Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako: 18 Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino. 19 Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse, 20 ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi; 21 Edomu, Mowabu ndi Amoni. 22 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja; 23 ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali. 24 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu. 25 Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya; 26 ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.

27 “Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ 28 Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’ ” 29 Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.

30 “Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti,

“ ‘Yehova adzabangula kumwamba;
    mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika.
    Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake.
Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa,
    kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
31 Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi,
    chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse;
adzaweruza mtundu wonse wa anthu
    ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ”
            akutero Yehova.

32 Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani! Mavuto akuti akachoka
    pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina;
mphepo ya mkuntho ikuyambira
    ku malekezero a dziko.”

Mateyu 10:5-15

Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10 musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11 Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12 Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13 Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.