Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kalata Yolembera Anthu a ku Ukapolo
29 Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
4 Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, 5 “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. 6 Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. 7 Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.”
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.
66 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
2 Imbani ulemerero wa dzina lake;
kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
3 Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!
Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri
kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
4 Dziko lonse lapansi limaweramira inu;
limayimba matamando kwa Inu;
limayimba matamando pa dzina lanu.”
Sela.
5 Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
6 Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,
iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.
Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
7 Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.
Anthu owukira asadzitukumule.
8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
9 Iye watchinjiriza miyoyo yathu
ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.
8 Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino 9 umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo. 10 Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha.
11 Mawu oyenera kuwadalira ndi awa:
Ngati ife tinafa naye pamodzi,
tidzakhalanso moyo pamodzi naye.
12 Ngati tinapirira,
tidzalamuliranso naye pamodzi.
Ngati ife timukana,
Iye adzatikananso.
13 Ngati ndife osakhulupirika,
Iye adzakhalabe wokhulupirika
popeza sangathe kudzikana.
Kuthana ndi Aphunzitsi Onyenga
14 Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. 15 Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola.
Yesu Achiritsa Akhate Khumi
11 Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. 12 Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13 ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!”
14 Iye atawaona, anati, “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.
15 Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16 Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.
17 Yesu anafunsa kuti, “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18 Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” 19 Pamenepo anati kwa iye, “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.