Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini.
7 Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu;
pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,
2 mwina angandikadzule ngati mkango,
ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.
3 Inu Yehova Mulungu wanga,
ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,
4 ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere,
kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,
5 pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira,
lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi
ndipo mundigoneke pa fumbi.
Sela
6 Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu;
nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga.
Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.
7 Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani.
Alamulireni muli kumwambako;
8 Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo.
Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa,
monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.
9 Inu Mulungu wolungama,
amene mumasanthula maganizo ndi mitima,
thetsani chiwawa cha anthu oyipa
ndipo wolungama akhale motetezedwa.
10 Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba,
amene amapulumutsa olungama mtima.
11 Mulungu amaweruza molungama,
Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.
12 Ngati munthu satembenuka,
Mulungu adzanola lupanga lake,
Iye adzawerama ndi kukoka uta.
13 Mulungu wakonza zida zake zoopsa;
Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.
14 Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse.
Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.
15 Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa
amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.
16 Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini;
chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.
17 Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;
ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.
9 Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi
ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto:
“Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya;
onani chisokonezo pakati pake
ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”
10 “Iwo sadziwa kuchita zolungama,
ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova.
11 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi:
“Mdani adzalizungulira dzikoli;
iye adzagwetsa malinga ako,
ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.”
12 Yehova akuti,
“Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango
miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu,
moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli
amene amakhala mu Samariya
pa msonga za mabedi awo,
ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.”
13 “Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
14 “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake,
ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli;
nyanga za guwa zidzathyoka
ndipo zidzagwa pansi.
15 Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira
pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha;
nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa
ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,”
akutero Yehova.
Israeli Sanabwerere kwa Mulungu
4 Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya,
inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa
ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!”
2 Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti,
“Nthawi idzafika ndithu
pamene adzakukokani ndi ngowe,
womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza.
3 Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma
aliyense payekhapayekha,
ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,”
akutero Yehova.
4 “Bwerani ku Beteli mudzachimwe;
ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa.
Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse,
bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.
5 Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko
ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu.
Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo,
pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,”
akutero Ambuye Yehova.
Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa
2 Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. 2 Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. 3 Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” 4 kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?
5 Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? 6 Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? 7 Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.