Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 32:1-3

Yeremiya Agula Munda

32 Yehova anayankhula ndi Yeremiya mʼchaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinalinso chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara. Pa nthawi imeneyi nʼkuti ankhondo a mfumu ya ku Babuloni atazinga Yerusalemu, ndipo mneneri Yeremiya ndiye anamutsekera mʼbwalo la alonda mʼnyumba yaufumu ya ku Yuda.

Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda.

Yeremiya 32:6-15

Yeremiya anati, “Yehova wandiwuza kuti: Taonani, Hanameli mwana wa Salumu, amalume ako akubwera ndipo adzakuwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, chifukwa iwe ndiwe mʼbale wanga ndipo ndiwe woyenera kuwuwombola.’ ”

Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.”

“Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja; choncho ndinagula munda wa ku Anatoti kwa Hanameli msuweni wanga, ndipo ndinamupatsa masekeli asiliva 17. 10 Ndinasayina panganolo ndikulimata pamaso pa mboni, kenaka ndinayeza ndalama zasilivazo pa sikelo.” 11 Pambuyo pake ndinatenga makalata anga a pangano, imodzi yomatidwa mʼmene munali malamulo onse a panganolo ndi ina yosamatidwa. 12 Ndinapereka makalatawo kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseya pamaso pa Hanameli msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zinasayina panganoli ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala mʼbwalo la alonda.

13 “Ndinamulangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti, 14 ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Tenga makalata awa a umboni wapangano, iyi yokhala ndi chizindikiro ndi yopanda chizindikiro, uwasunge mʼmbiya kuti akhale nthawi yayitali. 15 Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Anthu adzagulanso nyumba, minda ndi mitengo yamphesa mʼdziko lino.’ ”

Masalimo 91:1-6

91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
    adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
    Mulungu wanga amene ndimadalira.”

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje
    ndi ku mliri woopsa;
Adzakuphimba ndi nthenga zake,
    ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
    kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,
    kapena muvi wowuluka masana,
kapena mliri umene umayenda mu mdima,
    kapena zowononga za pa nthawi ya masana.

Masalimo 91:14-16

14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
    ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
    ndidzakhala naye pa mavuto,
    ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
    ndi kumupulumutsa.”

1 Timoteyo 6:6-19

Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. 10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo

11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. 12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. 13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. 14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera. 15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye. 16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.

Za Kudalira Chuma

17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. 18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. 19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.

Luka 16:19-31

Za Munthu Wachuma ndi Lazaro

19 “Panali munthu wachuma amene ankavala zovala zofiirira za mtengowapatali ndipo ankakhala moyo wachisangalalo tsiku lililonse. 20 Pa khomo la mpanda wake ankagonekapo munthu wopempha wotchedwa Lazaro, wazilonda thupi lonse 21 ndipo ankafunitsitsa atadya zomwe zinkagwa pansi kuchokera pamene munthu wolemerayo amadyerapo. Agalu ankabweranso ndi kumanyambita zilonda zake.

22 “Nthawi inafika imene wopemphayo anamwalira ndipo angelo anamunyamula nakamuyika mʼmanja mwa Abrahamu. Munthu wolemerayo anamwaliranso ndipo anayikidwa mʼmanda. 23 Ali mʼgehena kuzunzika, anakweza maso ake ndipo anaona Abrahamu ali ndi Lazaro pambali pake. 24 Ndipo anafuwula kwa iye kuti, ‘Abambo Abrahamu, mundimvere chisoni ine ndipo mutumeni Lazaroyo kuti aviyike msonga ya chala chake mʼmadzi kuti aziziritse lilime langa, chifukwa ndikumva ululu mʼmoto muno.’

25 “Koma Abrahamu anayankha kuti, ‘Mwanawe kumbukira kuti nthawi yamoyo wako unalandira zinthu zako zabwino, pamene Lazaro analandira zinthu zoyipa, koma tsopano akusangalatsidwa kuno ndipo iwe uli mʼmazunzo. 26 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi, pakati pa inu ndi ife pali chiphompho chachikulu chimene chinayikidwa, kotero kuti amene akufuna kubwera kumeneko sangathe, kapena palibe amene angawoloke kuchokera kumeneko kudzafika kuno.’

27 “Iye anayankha kuti, ‘Ndipo ndikupemphani inu, abambo, mutumeni Lazaro ku nyumba ya abambo anga, 28 pakuti ine ndili ndi abale asanu. Lolani iye akawachenjeze kotero kuti asadzabwere kumalo ano amazunzo.’

29 “Abrahamu anayankha kuti, ‘Ali ndi Mose ndi Aneneri; aleke amvere iwo.’

30 “Iye anati, ‘Ayi, bambo Abrahamu, koma ngati wina ochokera kwa akufa adzapita kwa iwo, adzatembenuka mtima.’

31 “Anati kwa iye, ‘Ngati iwo samvera Mose ndi Aneneri, sadzakhulupirira ngakhale wina atauka kwa akufa.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.