Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 4:11-12

11 Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; 12 koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”

Yeremiya 4:22-28

22 Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;
    iwo sandidziwa.
Iwo ndi ana opanda nzeru;
    samvetsa chilichonse.
Ali ndi luso lochita zoyipa,
    koma sadziwa kuchita zabwino.”

23 Ndinayangʼana dziko lapansi,
    ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;
ndinayangʼana thambo,
    koma linalibe kuwala kulikonse.
24 Ndinayangʼana mapiri,
    ndipo ankagwedezeka;
    magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
25 Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;
    mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
26 Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;
    mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja
    pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.

27 Yehova akuti,

“Dziko lonse lidzasanduka chipululu
    komabe sindidzaliwononga kotheratu.
28 Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira
    ndipo thambo lidzachita mdima,
pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,
    ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”

Masalimo 14

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

14 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
    “Kulibe Mulungu.”
Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa;
    palibe amene amachita zabwino.

Yehova kumwamba wayangʼana pansi,
    kuyangʼana anthu onse
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
    amene amafunafuna Mulungu.
Onse atembenukira kumbali,
    onse pamodzi asanduka oyipa;
palibe amene amachita zabwino,
    palibiretu ndi mmodzi yemwe.

Kodi anthu ochita zoyipawa sadziwa chilichonse?
    Akudya anthu anga ngati chakudya chawo
    ndipo satamanda Yehova?
Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu,
    pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.
Inu ochita zoyipa mumalepheretsa chikonzero cha anthu osauka,
    koma Yehova ndiye pothawirapo pawo.

Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni!
    Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake,
    Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!

1 Timoteyo 1:12-17

Chisomo cha Ambuye kwa Paulo

12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. 13 Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. 14 Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.

15 Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. 16 Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. 17 Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Luka 15:1-10

Fanizo la Nkhosa Yotayika

15 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”

Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”

Fanizo la Ndalama Yotayika

“Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza? Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’ 10 Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.