Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 91:1-6

91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
    adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
    Mulungu wanga amene ndimadalira.”

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje
    ndi ku mliri woopsa;
Adzakuphimba ndi nthenga zake,
    ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
    kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,
    kapena muvi wowuluka masana,
kapena mliri umene umayenda mu mdima,
    kapena zowononga za pa nthawi ya masana.

Masalimo 91:14-16

14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
    ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
    ndidzakhala naye pa mavuto,
    ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
    ndi kumupulumutsa.”

Yeremiya 24

Madengu Awiri a Nkhuyu

24 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova. Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.

Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”

Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi. Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula. Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.

“ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto. Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira. 10 Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’ ”

Luka 9:43-48

43 Ndipo iwo onse anadabwa ndi ukulu wa Mulungu.

Yesu Abwereza Kunena za Imfa yake

Aliyense akudabwa ndi zimene Yesu anachita, Iyeyo anati kwa ophunzira ake, 44 “Tamvetsetsani zimene ndikufuna kukuwuzani: Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu.” 45 Koma iwo sanazindikire zimene amatanthauza. Izi zinawadabwitsa kotero sanathe kuzimvetsa ndipo anaopa kumufunsa.

Wamkulu Ndani?

46 Mkangano unayambika pakati pa ophunzira wa kuti wamkulu koposa akanakhala ndani mwa iwo. 47 Yesu podziwa maganizo awo, anatenga kamwana nakayimika pambali pake. 48 Ndipo Iye anawawuza kuti, “Aliyense wolandira bwino kamwana aka mʼdzina langa, ndiye kuti akulandiranso bwino Ine; ndipo aliyense wolandira bwino Ine, ndiye kuti akulandiranso bwino amene anandituma Ine. Pakuti amene ndi wamngʼono pakati panu, ndiye amene ali wamkulu koposa.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.