Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 94

94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
    Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
    bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
    mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?

Amakhuthula mawu onyada;
    onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
    amapondereza cholowa chanu.
Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
    amapha ana amasiye.
Iwo amati, “Yehova sakuona;
    Mulungu wa Yakobo salabadirako.”

Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
    zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
    Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
    Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
    Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.

12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
    munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
    mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
    Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
    ndipo onse olungama mtima adzachitsata.

16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
    Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
    bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
    chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
    chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
    umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
    ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
    ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
    ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
    Yehova Mulungu wathu adzawawononga.

Yeremiya 5:18-31

18 “Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. 19 Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”

20 “Lengeza izi kwa ana a Yakobo
    ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
21 Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
    inu amene maso muli nawo koma simupenya,
    amene makutu muli nawo koma simumva.
22 Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
            Akutero Yehova.
    “Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
    malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
    mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
23 Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
    andifulatira ndipo andisiyiratu.
24 Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
    ‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
    Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
25 Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
    ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.

26 “Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
    amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
    ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
27 Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
    ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
28     Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
    saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
    sateteza ufulu wa anthu osauka.
29 Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
    Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
            Akutero Yehova.

30 “Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
    chachitika mʼdzikomo:
31 Aneneri akunenera zabodza,
    ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
    Koma mudzatani potsiriza?

2 Petro 3:8-13

Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.

10 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.

11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.