Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 139:1-6

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

139 Inu Yehova, mwandisanthula
    ndipo mukundidziwa.
Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
    mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
    mumadziwa njira zanga zonse.
Mawu asanatuluke pa lilime langa
    mumawadziwa bwinobwino, Inu Yehova.

Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
    mwasanjika dzanja lanu pa ine.
Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
    ndi zapamwamba kuti ine ndizipeze.

Masalimo 139:13-18

13 Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
    munandiwumba pamodzi mʼmimba mwa amayi anga.
14 Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
    ntchito zanu ndi zodabwitsa,
    zimenezi ndimazidziwa bwino lomwe.
15 Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
    pamene ndimapangidwa mʼmalo achinsinsi,
pamene ndinkawumbidwa mwaluso mʼmimba ya amayi anga.
16 Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
    Masiku onse amene anapatsidwa kwa ine, analembedwa mʼbuku lanu
    asanayambe nʼkuwerengedwa komwe.

17 Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
    ndi zosawerengeka ndithu!
18 Ndikanaziwerenga,
    zikanakhala zochuluka kuposa mchenga;
    pamene ndadzuka, ndili nanube.

Yeremiya 16:14-17:4

14 Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ 15 koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”

16 Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. 17 Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa. 18 Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”

19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa,
    pothawirapo panga nthawi ya masautso,
anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu
    kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti,
“Makolo anthu anali ndi milungu yonama,
    anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
20 Kodi anthu nʼkudzipangira milungu?
    Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”

21 “Choncho Ine ndidzawaphunzitsa,
    kokha kano kuti adziwe
    za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga.
Pamenepo adzadziwa kuti
    dzina langa ndi Yehova.

17 “Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,
    lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.
Uchimowo walembedwa pa mitima yawo
    ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
Ngakhale ana awo amakumbukira
    maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,
pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,
    pa mapiri aatali mʼdzikomo.
Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense
    ndidzazipereka kwa ofunkha
kuti zikhale dipo lawo
    chifukwa cha machimo
    ochitika mʼdziko lonse.
Mudzataya dziko limene ndinakupatsani
    kuti likhale cholowa chanu.
Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu
    mʼdziko limene inu simukulidziwa,
chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,
    ndipo udzayaka mpaka muyaya.”

Akolose 4:7-17

Mawu Otsiriza

Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.

10 Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). 11 Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. 12 Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. 13 Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. 14 Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. 15 Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.

16 Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.

17 Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.