Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
91 Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba
adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse.
2 Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa,
Mulungu wanga amene ndimadalira.”
3 Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje
ndi ku mliri woopsa;
4 Adzakuphimba ndi nthenga zake,
ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo;
kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo.
5 Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku,
kapena muvi wowuluka masana,
6 kapena mliri umene umayenda mu mdima,
kapena zowononga za pa nthawi ya masana.
14 “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa;
ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa.
15 Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha;
ndidzakhala naye pa mavuto,
ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza.
16 Ndidzamupatsa moyo wautali
ndi kumupulumutsa.”
23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
ndiye sindine Mulungu?
24 Kodi wina angathe kubisala
Ine osamuona?”
“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
Akutero Yehova.
25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Amene anali Akufa Alandira Moyo
2 Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu, 2 mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera. 3 Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. 4 Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, 5 anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo. 6 Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu, 7 ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu. 8 Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, 9 osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire. 10 Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.