Add parallel Print Page Options

19 Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.”

Read full chapter