Beginning
51 Yehova akuti,
“Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowononga
kuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai.
2 Ndidzatuma alendo ku Babuloni
kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu.
Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse
pa tsiku la masautso ake.
3 Okoka uta musawalekerere
kapena wonyadira chovala chawo chankhondo.
Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo;
koma muwononge ankhondo ake kotheratu.
4 Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni
lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.
5 Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye
ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,
koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo
pamaso pa Woyerayo wa Israeli.
6 “Thawaniko ku Babuloni!
Aliyense apulumutse moyo wake!
Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.
Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;
Yehova adzamulipsira.
7 Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;
kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.
Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;
nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
8 Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.
Mulireni!
Mfunireni mankhwala opha ululu wake;
mwina iye nʼkuchira.”
9 Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,
koma sanachire;
tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,
pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,
wafika mpaka kumwamba.’
10 “ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa;
tiyeni tilengeze mu Ziyoni
zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’
11 “Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,
popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.
Motero adzalipsira Ababuloni
chifukwa chowononga Nyumba yake.
Ndiye Yehova akuti,
‘Nolani mivi, tengani zishango.’
12 Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!
Limbitsani oteteza,
ikani alonda pa malo awo,
konzekerani kulalira.
Pakuti Yehova watsimikiza
ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
13 Inu muli ndi mitsinje yambiri
ndi chuma chambiri.
Koma chimaliziro chanu chafika,
moyo wanu watha.
14 Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti:
Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe,
kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.
15 “Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
ndipo anayala thambo mwaluso lake.
16 Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.
Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.
17 “Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
alibe moyo mʼkati mwawo.
18 Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
19 Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,
kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
20 “Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,
chida changa chankhondo.
Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,
ndi iwe ndimawononga maufumu,
21 ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,
ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.
22 Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,
ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,
ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
23 Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,
ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,
ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.
24 “Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.
25 “Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga,
amene umawononga dziko lonse lapansi,”
akutero Yehova.
“Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga,
kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako,
ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera.
26 Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga
kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba,
chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”
akutero Yehova.
27 “Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko!
Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu!
Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo;
itanani maufumu awa:
Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo.
Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye;
tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.
28 Konzekeretsani mitundu ya anthu.
Amenewa ndiwo mafumu a Amedi,
abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo,
ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.
29 Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira,
chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni;
kusakaza dziko la Babuloni
kuti musapezeke wokhalamo.
30 Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo;
iwo angokhala mʼmalinga awo.
Mphamvu zawo zatheratu;
ndipo akhala ngati akazi.
Malo ake wokhala atenthedwa;
mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
31 Othamanga akungopezanapezana,
amithenga akungotsatanatsatana
kudzawuza mfumu ya ku Babuloni
kuti alande mzinda wake wonse.
32 Madooko onse alandidwa,
malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto,
ndipo ankhondo onse asokonezeka.”
33 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu
pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,
Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”
34 A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,
watiphwanya,
ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.
Watimeza ngati ngʼona,
wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,
kenaka nʼkutilavula.”
35 Anthu a ku Ziyoni anene kuti,
“Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”
Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,
“Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”
36 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
“Taona, ndidzakumenyera nkhondo
ndi kukulipsirira;
ndidzawumitsa nyanja yake
ndipo akasupe ake adzaphwa.
37 Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka,
malo okhala nkhandwe,
malo ochititsa mantha ndi onyozedwa,
malo wopanda aliyense wokhalamo.
38 Anthu ake onse adzabangula ngati mkango,
adzadzuma ngati ana amkango.
39 Ngati achita dyera
ndiye ndidzawakonzera madyerero
ndi kuwaledzeretsa,
kotero kuti adzasangalala,
kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,”
akutero Yehova.
40 “Ine ndidzawatenga
kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa,
ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
41 “Ndithu Babuloni walandidwa,
mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa!
Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha
pakati pa mitundu ya anthu!
42 Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni;
mafunde ake okokoma aphimba Babuloni.
43 Mizinda yake yasanduka bwinja,
dziko lowuma ndi lachipululu,
dziko losakhalamo wina aliyense,
dziko losayendamo munthu aliyense.
44 Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni,
ndidzamusanzitsa zimene anameza.
Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.
Malinga a Babuloni agwa.
45 “Tulukani mʼBabuloni anthu anga!
Pulumutsani miyoyo yanu!
Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova.
46 Musataye mtima kapena kuchita mantha
pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu.
Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera
za ziwawa mʼdziko lapansi,
ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.
47 Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu
pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;
dziko lake lonse lidzachita manyazi
ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
48 Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo
zidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.
Anthu owononga ochokera kumpoto
adzamuthira nkhondo,”
akutero Yehova.
49 “Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.
Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwa
chifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.
50 Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,
chokani pano ndipo musazengereze!
Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,
ganizirani za Yerusalemu.”
51 Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,
chifukwa tanyozedwa
ndipo nkhope zathu zili ndi manyazi,
chifukwa anthu achilendo alowa
malo opatulika a Nyumba ya Yehova.”
52 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
“Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,
ndipo mʼdziko lake lonse
anthu ovulala adzabuwula.
53 Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga
ndi kulimbitsa nsanja zake,
ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,”
akutero Yehova.
54 “Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.
Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulu
kuchokera mʼdziko la Babuloni.
55 Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,
ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.
Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.
Phokoso lawo likunka likwererakwerera.
56 Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,
ankhondo ake agwidwa,
ndipo mauta awo athyoka.
Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;
adzabwezera kwathunthu.
57 Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,
abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;
adzagona kwamuyaya osadzukanso,”
akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
58 Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa
ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;
mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.
Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
59 Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo. 60 Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni. 61 Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa. 62 Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ 63 Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate. 64 Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ”
Mawu a Yeremiya athera pamenepa.
Kuwonongeka kwa Yerusalemu
52 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Yehoyakimu. 3 Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake.
Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.
4 Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo. 5 Mzindawo unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya.
6 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya. 7 Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, 8 koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.
9 Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. 10 Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda. 11 Ndipo inamukolowola maso Zedekiya, ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni kumene inakamuyika mʼndende kuti akhalemo moyo wake wonse.
12 Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 13 Ndipo anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse. 14 Tsono gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene linali ndi mtsogoleri wa ankhondo a mfumu uja linagwetsa malinga onse ozungulira Yerusalemu. 15 Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 16 Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina.
17 Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni. 18 Ankhondowo anatenganso mbiya, zochotsera phulusa, zozimitsira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho pamodzi ndi ziwiya zina zonse za mkuwa zimene ankagwiritsira ntchito mʼNyumba ya Yehova. 19 Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva.
20 Nsanamira ziwiri zija, chimbiya, maphaka ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri za mkuwa zochirikizira chimbiyacho zimene mfumu Solomoni anapangira Nyumba ya Yehova kulemera kwake kunali kosawerengeka. 21 Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi. 22 Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija. 23 Mʼmbali mwake munali makangadza 96; makangadza onse pamodzi analipo 100 kuzungulira ukonde onse.
24 Mtsogoleri wa ankhondo uja, anagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apachipata. 25 Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. 26 Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondoyo anawatenga onse napita nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula. 27 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe.
Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo. 28 Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi:
Mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023;
29 mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,
anatenga anthu 832 kuchokera mu Yerusalemu;
30 mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,
Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo.
Onse pamodzi analipo anthu 4,600.
Kumasulidwa kwa Yehoyakini
31 Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo. 32 Evili-Merodaki anakomera mtima Yehoyakini, namupatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babuloni. 33 Choncho Yehoyakini analoledwa kuvula zovala zake za ku ndende ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. 34 Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.