Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 23-25

Nthambi Yolungama

23 “Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.

Yehova akuti, “Masiku akubwera,
    pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.
Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka
    ndipo Israeli adzakhala pamtendere.
Dzina limene adzamutcha ndi ili:
    Yehova ndiye Chilungamo Chathu.

Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”

Aneneri Onyenga

Kunena za aneneri awa:

Mtima wanga wasweka;
    mʼnkhongono mwati zii.
Ndakhala ngati munthu woledzera,
    ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,
chifukwa cha Yehova
    ndi mawu ake opatulika.
10 Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;
    lili pansi pa matemberero.
    Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.
Aneneri akuchita zoyipa
    ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.

11 “Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.
    Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”
            akutero Yehova.
12 “Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;
    adzawapirikitsira ku mdima
    ndipo adzagwera kumeneko.
Adzaona zosaona
    mʼnthawi ya chilango chawo,”
            akutero Yehova.

13 “Pakati pa aneneri a ku Samariya
    ndinaona chonyansa ichi:
Ankanenera mʼdzina la Baala
    ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
14 Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu
    ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:
    amachita chigololo, amanena bodza
ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.
    Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.
Kwa Ine anthu onsewa
    ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”

15 Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa
    ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,
chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse
    ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”

16 Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;
    zomwe aloserazo nʼzachabechabe.
Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,
    osati zochokera kwa Yehova.
17 Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,
    ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’
Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,
    ‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
18 Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?
    Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?
    Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
19 Taonani ukali wa Yehova
    uli ngati chimphepo chamkuntho,
inde ngati namondwe.
    Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
20 Mkwiyo wa Yehova sudzaleka
    mpaka atachita zonse zimene
    anatsimikiza mu mtima mwake.
Mudzazizindikira bwino zimenezi
    masiku akubwerawa.”
21 Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,
    komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;
Ine sindinawayankhule,
    komabe iwo ananenera.
22 Iwo akanakhala pa msonkhano wanga
    ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.
Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa
    kuti aleke machimo awo.”

23 Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
    ndiye sindine Mulungu?
24 Kodi wina angathe kubisala
    Ine osamuona?”
    “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
            Akutero Yehova.

25 “Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26 Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27 Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28 Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29 Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.

30 Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31 Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32 Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.

Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza

33 Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ 34 Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. 35 Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ 36 Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. 37 Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ 38 Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, 39 ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. 40 Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”

Madengu Awiri a Nkhuyu

24 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova. Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.

Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”

Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi. Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula. Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.

“ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto. Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira. 10 Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’ ”

Zaka 70 za Ukapolo

25 Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Choncho mneneri Yeremiya anawuza anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi onse amene amakhala mu Yerusalemu kuti: Kwa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda mpaka lero lino, Yehova wakhala akundipatsa mauthenga ake ndipo ine ndakhala ndikuyankhula ndi inu kawirikawiri, koma inu simunamvere.

Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu. Aneneriwo ankanena kuti, “Ngati aliyense wa inu abwerere, kusiya njira zake zoyipa ndi machitidwe ake oyipa, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko limene Yehova anapereka kwa makolo anu kwamuyaya. Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.

“Koma inu simunandimvere,” akutero Yehova, “ndipo munaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene munapanga ndi manja anu. Choncho munadziwononga nokha.”

Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Chifukwa simunamvere mawu anga, ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya. 10 Ndidzathetsa mfuwu wachimwemwe ndi wachisangalalo, mawu a mkwati ndi mkwatibwi, phokoso la mphero ndi kuwala kwa nyale. 11 Dziko lonse lidzakhala bwinja ndi chipululu, ndipo mitundu ina idzatumikira mfumu ya ku Babuloni kwa 70.

12 “Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya. 13 Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa. 14 Iwo eni adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi mafumu amphamvu. Ndidzawabwezera molingana ndi zochita zawo ndi ntchito za manja awo.”

Chikho cha Ukali wa Mulungu

15 Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma. 16 Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”

17 Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako: 18 Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino. 19 Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse, 20 ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi; 21 Edomu, Mowabu ndi Amoni. 22 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja; 23 ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali. 24 Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu. 25 Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya; 26 ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.

27 “Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ 28 Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’ ” 29 Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.

30 “Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti,

“ ‘Yehova adzabangula kumwamba;
    mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika.
    Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake.
Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa,
    kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
31 Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi,
    chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse;
adzaweruza mtundu wonse wa anthu
    ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ”
            akutero Yehova.

32 Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Taonani! Mavuto akuti akachoka
    pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina;
mphepo ya mkuntho ikuyambira
    ku malekezero a dziko.”

33 Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.

34 Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu;
    gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa.
Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika;
    mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.
35 Abusa adzasowa kothawira,
    atsogoleri a nkhosa adzasowa malo opulumukira.
36 Imvani kulira kwa abusa,
    atsogoleri a nkhosa akulira,
    chifukwa Yehova akuwononga msipu wawo.
37 Makola awo a nkhosa amene anali pamtendere adzasanduka bwinja
    chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
38 Ngati mkango, Yehova wasiya phanga lake,
    pakuti dziko lawo lasanduka chipululu
chifukwa cha nkhondo ya owazunza
    ndiponso chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.