Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 26-29

Yeremiya Amangidwa

26 Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe. Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa. Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”

Ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akuyankhula mawu amenewa mʼNyumba ya Yehova. Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa! Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.

10 Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova. 11 Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”

12 Ndipo Yeremiya anawuza nduna zija ndi anthu onse kuti, “Yehova anandituma kunenera mawu onse amene mwawamva otsutsa Nyumba ino ndi mzinda uno. 13 Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni. 14 Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera. 15 Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.”

16 Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”

17 Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, 18 “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
    Yerusalemu adzasanduka bwinja,
    ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’

19 Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”

20 (Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. 21 Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. 22 Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. 23 Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).

24 Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.

Yuda Adzatumikira Nebukadinezara

27 Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.

“ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ 10 Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. 11 Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”

12 Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. 13 Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? 14 Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. 15 Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”

16 Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? 18 Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. 19 Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. 20 Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 21 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, 22 ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”

Hananiya Atsutsana ndi Yeremiya

28 Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni. Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni. Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”

Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova. Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni. Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse: Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”

10 Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola, 11 ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.

12 Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti, 13 “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo. 14 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”

15 Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza. 16 Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”

17 Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.

Kalata Yolembera Anthu a ku Ukapolo

29 Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo. Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:

Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.” Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova.

10 Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. 11 Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. 12 Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. 13 Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse 14 mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.”

15 Inu mumati, “Yehova watiwutsira aneneri athu ku Babuloni,” 16 koma zimene Yehova akunena za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide pamodzi ndi anthu onse amene anatsala mu mzinda muno, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo ndi izi, 17 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawapha ndi nkhondo, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa ngati nkhuyu zowola kwambiri, zosati nʼkudya. 18 Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako. 19 Zidzatero chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinkawatumizira kudzera mwa atumiki anga, aneneri. Ngakhale inu amene muli ku ukapolo simunamverenso,” akutero Yehova.

20 Choncho, imvani mawu a Yehova, inu akapolo nonse amene ndinakuchotsani mu Yerusalemu ndi kukupititsani ku Babuloni. 21 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya. 22 Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’ 23 Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.

Kalata ya Semaya

24 Ukamuwuze Semaya wa ku Nehelamu kuti, 25 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti, 26 ‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo. 27 Nanga tsono chifukwa chiyani simunamuchitire zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? 28 Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ”

29 Koma wansembe Zefaniya anayiwerenga kalatayo pamaso pa mneneri Yeremiya. 30 Ndipo Yehova anawuza Yeremiya kuti, 31 “Tumiza uthenga uwu kwa akapolo onse: ‘Yehova akuti zokhudza Semaya wa ku Nehelamu: Semaya wakuloserani, ngakhale kuti Ine sindinamutume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira bodza. 32 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.