Beginning
1 Mawu a Yeremiya mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, mʼdziko la Benjamini. 2 Mawuwa Yehova anayankhula naye mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya Yuda. 3 Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.
Kuyitanidwa kwa Yeremiya
4 Yehova anayankhula nane kuti,
5 “Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,
iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;
ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
6 Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”
7 Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. 8 Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
9 Pamenepo Yehova anatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga, nandiwuza kuti, “Taona, tsopano ndayika mawu anga mʼkamwa mwako. 10 Lero ndakusankha kuti ukhale ndi ulamuliro pa mitundu ya anthu ndi pa maufumu awo kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kugumula, kuti uwamange ndi kudzala.”
11 Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona nthambi ya mtengo wa mtowo.”
12 Yehova anandiwuza kuti, “Waona bwino, chifukwa Ine ndikuonetsetsa kuti mawu angawa akwaniritsidwe.”
13 Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”
14 Yehova anandiwuza kuti, “Mavuto a anthu onse okhala mʼdziko lino adzachokera kumpoto. 15 Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova.
“Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu
polowera pa zipata za Yerusalemu;
iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake
ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.
16 Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo
chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine.
Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina,
ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.
17 “Koma iwe Yeremiya konzeka! Nyamuka ndipo ukawawuze zonse zimene ndakulamulira. Usachite nawo mantha, kuopa kuti Ine ndingakuchititse mantha iwo akuona. 18 Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo. 19 Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
Aisraeli Asiya Mulungu
2 Yehova anandiwuza kuti, 2 “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti,
“ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako,
mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi,
mmene unkanditsata mʼchipululu muja;
mʼdziko losadzalamo kanthu.
3 Israeli anali wopatulika wa Yehova,
anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola;
onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa
ndipo mavuto anawagwera,’ ”
akutero Yehova.
4 Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo,
inu mafuko onse a Israeli.
5 Yehova akuti,
“Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji,
kuti andithawe?
Iwo anatsata milungu yachabechabe,
nawonso nʼkusanduka achabechabe.
6 Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti,
amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto
natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma
ndi lokumbikakumbika,
mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima,
dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
7 Ndinakufikitsani ku dziko lachonde
kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.
Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa
ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.
8 Ansembe nawonso sanafunse kuti,
‘Yehova ali kuti?’
Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe;
atsogoleri anandiwukira.
Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala,
ndi kutsatira mafano achabechabe.
9 “Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,”
akutero Yehova.
“Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
10 Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone,
tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino;
ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:
11 Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake?
(Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe).
Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero
ndi mafano achabechabe.
12 Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi,
ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,”
akutero Yehova.
13 “Popeza anthu anga achita machimo awiri:
Andisiya Ine
kasupe wa madzi a moyo,
ndi kukadzikumbira zitsime zawo,
zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.
14 Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi.
Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?
15 Adani ake abangulira
ndi kumuopseza ngati mikango.
Dziko lake analisandutsa bwinja;
mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
16 Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi
akuphwanyani mitu.
17 Zimenezitu zakuchitikirani
chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu
pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
18 Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,
kukamwa madzi a mu Sihori?
Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,
kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
19 Kuyipa kwanuko kudzakulangani;
kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.
Tsono ganizirani bwino,
popeza ndi chinthu choyipa
kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;
ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
20 “Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu
ndi kudula msinga zanu;
munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’
Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.
Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali
ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
21 Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;
unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.
Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa
wachabechabe wonga wa kutchire?
22 Ngakhale utasamba ndi soda
kapena kusambira sopo wambiri,
kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”
akutero Ambuye Yehova.
23 “Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse;
sindinatsatire Abaala’?
Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja;
zindikira bwino zomwe wachita.
Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro
yomangothamanga uku ndi uku,
24 wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu,
yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika.
Ndani angayiretse chilakolako chakecho?
Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika.
Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.
25 Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi
ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu.
Koma unati, ‘Zamkutu!
Ine ndimakonda milungu yachilendo,
ndipo ndidzayitsatira.’
26 “Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,
moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;
Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,
ansembe ndi aneneri awo.
27 Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’
ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’
Iwo andifulatira Ine,
ndipo safuna kundiyangʼana;
Koma akakhala pa mavuto amati,
‘Bwerani mudzatipulumutse!’
28 Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha?
Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani
pamene muli pamavuto!
Inu anthu a ku Yuda,
milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.
29 “Kodi mukundizengeranji mlandu?
Nonse mwandiwukira,”
akutero Yehova.
30 “Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu;
iwo sanaphunzirepo kanthu.
Monga mkango wolusa,
lupanga lanu lapha aneneri anu.
31 “Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova:
“Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli
kapena ngati dziko la mdima wandiweyani?
Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;
sitidzabweranso kwa Inu’?
32 Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,
kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?
Komatu anthu anga andiyiwala
masiku osawerengeka.
33 Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi!
Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.
34 Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo
magazi a anthu osauka osalakwa.
Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba.
Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
35 inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,
sadzatikwiyira.’
Ndidzakuyimbani mlandu
chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’
36 Chifukwa chiyani
mukunkabe nimusinthasintha njira zanu?
Aigupto adzakukhumudwitsani
monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.
37 Mudzachokanso kumeneko
manja ali kunkhongo.
Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira,
choncho sadzakuthandizani konse.
3 “Ngati munthu asudzula mkazi wake
ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,
kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?
Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?
Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.
Komabe bwerera kwa ine,”
akutero Yehova.
2 “Tayangʼana ku zitunda zowuma.
Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?
Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,
ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.
Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu
ndi ntchito zanu zoyipa.
3 Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,
ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.
Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;
ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
4 Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena
kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
5 kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?
Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’
Umu ndimo mmene umayankhulira,
koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”
Kusakhulupirika kwa Israeli
6 Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. 7 Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. 8 Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. 9 Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. 10 Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.
11 Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. 12 Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,
“ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,
pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
13 Ungovomera kulakwa kwako
kuti unawukira Yehova Mulungu wako.
Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo
pansi pa mtengo uliwonse wogudira,
ndiponso kuti sunandimvere,’ ”
akutero Yehova.
14 “Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. 15 Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. 16 Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”
akutero Yehova.
17 Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. 18 Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
19 “Ine mwini ndinati,
“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga
ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,
cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’
Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’
ndi kuti simudzaleka kunditsata.
20 Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,
momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”
akutero Yehova.
21 Mawu akumveka pa magomo,
Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo
chifukwa anatsata njira zoyipa
ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.
22 Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;
ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.”
“Inde, tidzabwerera kwa Inu
pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
23 Ndithu kupembedza pa magomo
komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.
Zoonadi chipulumutso cha Israeli
chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
24 Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu
la ntchito za makolo athu,
nkhosa ndi ngʼombe zawo,
ana awo aamuna ndi aakazi.
25 Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,
ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.
Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,
ife pamodzi ndi makolo athu
kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino
sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.