Beginning
46 Yehova anamupatsa Yeremiya uthenga wonena za anthu a mitundu ina.
Uthenga Wonena za Igupto
2 Kunena za Igupto:
Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,
3 anati, “Konzani zishango zanu ndi malihawo,
ndipo yambanipo kupita ku nkhondo!
4 Mangani akavalo,
ndipo kwerani inu okwerapo!
Khalani pa mzere
mutavala zipewa!
Nolani mikondo yanu,
valani malaya anu ankhondo!
5 Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani?
Achita mantha
akubwerera,
ankhondo awo agonjetsedwa.
Akuthawa mofulumirapo
osayangʼananso mʼmbuyo,
ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,”
akutero Yehova.
6 Waliwiro sangathe kuthawa
ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kupulumuka.
Akunka napunthwa ndi kugwa
kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.
7 “Kodi ndani amene akukwera ngati Nailo,
ngati mtsinje wa madzi amkokomo?
8 Igupto akusefukira ngati Nailo,
ngati mitsinje ya madzi amkokomo.
Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi;
ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’
9 Tiyeni, inu akavalo!
Thamangani inu magaleta!
Tulukani, inu ankhondo,
ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango,
ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.
10 Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse;
tsiku lolipsira, lolipsira adani ake.
Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi,
lidzaledzera ndi magazi.
Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe
mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
11 “Pita ku Giliyadi ukatenge mankhwala
iwe namwali Igupto.
Wayesayesa mankhwala ambiri koma osachira;
palibe mankhwala okuchiritsa.
12 Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako;
kulira kwako kwadzaza dziko lapansi.
Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana,
onse awiri agwa pansi limodzi.”
13 Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za kubwera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kudzathira nkhondo Igupto ndi uwu:
14 “Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli.
Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi.
Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza,
chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’
15 Chifukwa chiyani mulungu wanu wamphamvu uja Apisi wathawa?
Iye sakanatha kulimba chifukwa Yehova anamugwetsa.
16 Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa.
Aliyense akuwuza mnzake kuti,
‘Tiyeni tibwerere kwathu,
ku dziko kumene tinabadwira,
tithawe lupanga la adani athu.’
17 Kumeneku iwo adzafuwula kuti,
‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti,
Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’
18 “Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu,
imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse,
“wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena,
ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.
19 Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo
inu anthu a ku Igupto,
pakuti Mefisi adzasanduka chipululu
ndipo adzakhala bwinja mopanda wokhalamo.
20 “Igupto ali ngati mwana wangʼombe wokongola,
koma chimphanga chikubwera
kuchokera kumpoto kudzalimbana naye.
21 Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye
ali ngati ana angʼombe onenepa.
Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi.
Palibe amene wachirimika.
Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira;
ndiyo nthawi yowalanga.
22 Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa
pamene adani abwera ndi zida zawo,
abwera ndi nkhwangwa
ngati anthu odula mitengo.
23 Iwo adzadula nkhalango ya Igupto,”
akutero Yehova,
“ngakhale kuti ndi yowirira.
Anthuwo ndi ochuluka kupambana dzombe,
moti sangatheke kuwerengeka.
24 Anthu a ku Igupto achita manyazi
atengedwa ukapolo ndi anthu a kumpoto.”
25 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira. 26 Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.
27 “Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha;
usataye mtima, iwe Israeli.
Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali,
ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere,
ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.
28 Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha,
pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova.
“Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu
a ku mayiko kumene ndakupirikitsira,
Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu.
Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera;
sindidzakulekerera osakulanga.”
Uthenga Wonena za Afilisti
47 Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:
2 Yehova akuti,
“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;
adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.
Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,
mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.
Anthu adzafuwula;
anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
3 akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,
phokoso la magaleta ake
ndi kulira kwa mikombero yake.
Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;
manja awo adzangoti khoba.
4 Pakuti tsiku lafika
lowononga Afilisti onse
ndi kupha onse otsala,
onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.
Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,
otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.
5 Anthu a ku Gaza ameta mipala;
anthu a ku Asikeloni akhala chete.
Inu otsala a ku chigwa,
mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?
6 “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,
kodi udzapumula liti?
Bwerera mʼmalo ako;
ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’
7 Koma lupangalo lidzapumula bwanji
pamene Yehova walilamulira
kuti lithire nkhondo
Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”
Uthenga Wonena za Mowabu
48 Ponena za Mowabu:
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.
Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;
linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
2 Palibenso amene akutamanda Mowabu;
ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:
‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’
Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;
ankhondo adzakupirikitsani.
3 Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.
Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
4 Mowabu wawonongeka;
ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
5 Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,
akulira kwambiri pamene akupita.
Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka
pa njira yotsikira ku Horonaimu.
6 Thawani! Dzipulumutseni;
khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
7 Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,
nanunso mudzatengedwa ukapolo,
ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
8 Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,
ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.
Chigwa chidzasanduka bwinja
ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa
monga Yehova wayankhulira.
9 Mtsineni khutu Mowabu
chifukwa adzasakazika;
mizinda yake idzasanduka mabwinja,
wopanda munthu wokhalamo.
10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!
Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!
11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,
ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;
iye sanatengedwepo ukapolo.
Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja
ndipo fungo lake silinasinthe.
12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko
ndipo adzamukhutula;
adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake
pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,
monga momwe Aisraeli anachitira manyazi
ndi Beteli amene ankamukhutulira.
14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.
Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
15 Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;
anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”
ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16 Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;
masautso ake akubwera posachedwa.
17 Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,
inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;
nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,
taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”
18 “Tsikani pa ulemerero wanu
ndipo khalani pansi powuma,
inu anthu okhala ku Diboni,
pakuti wowononga Mowabu
wabwera kudzamenyana nanu,
wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
19 Inu amene mumakhala ku Aroeri,
imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.
Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,
afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”
20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.
Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!
Lengezani ku mtsinje wa Arinoni
kuti Mowabu wawonongedwa.
21 Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,
ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
22 Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
23 Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
24 Keriyoti ndi Bozira
ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
25 Mphamvu za Mowabu zawonongeka;
mkono wake wathyoka,”
akutero Yehova.
26 “Muledzeretseni Mowabu,
chifukwa anadzikuza powukira Yehova.
Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;
mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
27 Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?
Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba
kuti nthawi zonse poyankhula za iye,
iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
28 Inu amene mumakhala ku Mowabu,
siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.
Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake
pa khomo la phanga.
29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu,
kunyada kwake nʼkwakukulu.
Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.
Ali ndi mtima wodzikweza.
30 Ine ndikuzidziwa ntchito zake,
akutero Yehova.
Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
31 Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,
ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,
ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.
Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa
imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;
zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.
Wowononga wasakaza
zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
33 Chimwemwe ndi chisangalalo zatha
ku minda ya zipatso ya ku Mowabu.
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;
palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.
Ngakhale kufuwula kulipo,
koma sikufuwula kwa chimwemwe.
34 “A ku Hesiboni ndi Eleali akulira
ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,
kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.
Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35 Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu
kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera
ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”
akutero Yehova.
36 “Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.
Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro
chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
37 Aliyense wameta mutu wake
ndi ndevu zake;
manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,
ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
38 Pa madenga onse a ku Mowabu
ndiponso mʼmisewu yake
anthu akungolira,
pakuti ndaphwanya Mowabu
ngati mtsuko wopanda ntchito,”
akutero Yehova.
39 “Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!
Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.
Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,
chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
40 Yehova akuti,
“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga
chimene chatambalitsa mapiko ake.
41 Mizinda idzagwidwa
ndipo malinga adzalandidwa.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu
idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
42 Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu
chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
43 Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira
inu anthu a ku Mowabu,”
akutero Yehova.
44 “Aliyense wothawa zoopsa
adzagwera mʼdzenje,
aliyense wotuluka mʼdzenje
adzakodwa mu msampha.
Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu
pa nthawi ya chilango chake,”
akutero Yehova.
45 “Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni
chifukwa chotopa.
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,
malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.
Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,
dziko la anthu onyada.
46 Tsoka kwa iwe Mowabu!
Anthu opembedza Kemosi awonongeka.
Ana ako aamuna ndi aakazi
atengedwa ukapolo.
47 “Komabe masiku akutsogolo
ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”
akutero Yehova.
Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.